Aroma 13:1-14

13  Munthu aliyense azimvera+ olamulira akuluakulu,+ chifukwa palibe ulamuliro+ umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola.+ Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana+ mololedwa ndi Mulungu.+  Chotero amene akutsutsana ndi ulamuliro akutsutsana ndi dongosolo la Mulungu. Amene akutsutsana ndi dongosolo limeneli adzalandira chiweruzo.+  Pakuti olamulira amaopsa ngati ukuchita zoipa,+ osati ngati ukuchita zabwino. Choncho kodi ukufuna kuti usamachite mantha ndi olamulira? Pitiriza kuchita zabwino,+ ndipo olamulira adzakutamanda.  Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino.+ Koma ngati ukuchita zoipa,+ chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, pakuti iye ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa.+  Chotero pali chifukwa chabwino chakuti anthu inu mukhalire ogonjera, osati chabe chifukwa choopa mkwiyo umenewo, komanso chifukwa cha chikumbumtima chanu.+  N’chifukwa chake mumakhomanso misonkho, pakuti iwo ndi antchito a Mulungu otumikira anthu,+ ndipo akukwaniritsa cholinga chimenechi nthawi zonse.  Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, m’patseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.+  Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense,+ kusiyapo kukondana,+ popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa chilamulo.+  Chifukwa malamulo onena kuti, “Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,+ Usabe,+ Usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 10  Chikondi+ sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake,+ chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.+ 11  Chitani zimenezi, makamakanso chifukwa chakuti nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo,+ pakuti chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira.+ 12  Usiku uli pafupi kutha, usana wayandikira.+ Chotero tiyeni tivule ntchito za mdima+ ndipo tivale zida za kuwala.+ 13  Tiyeni tiyende moyenera+ monga usana, osati m’maphwando aphokoso ndi kumwa mwauchidakwa,*+ osati m’chiwerewere ndi khalidwe lotayirira,+ ndiponso osati m’mikangano+ ndi nsanje. 14  Koma valani Ambuye Yesu Khristu,+ ndipo musamakonzekere kuchita zilakolako za thupi.+

Mawu a M'munsi

Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa n’cholinga chofuna kuledzera.