Aroma 7:1-25
7 Kodi mwina simukudziwa abale, (popeza ndikulankhula ndi anthu odziwa chilamulo,) kuti Chilamulo chimakhala mbuye wa munthu pamene munthuyo ali moyo?+
2 Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi amamasuka ku lamulo la mwamuna wake.+
3 Ngati angakwatiwe ndi mwamuna wina, mwamuna wake ali moyo, mkaziyo adzatchedwa wachigololo.+ Koma ngati mwamuna wake wamwalira, mkaziyo wamasuka ku lamulo lake, chotero si wachigololo ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina.+
4 Choncho abale anga, thupi la Khristu linakupangani kukhala akufa ku Chilamulo,+ kuti mukhale a winawake,+ a iye amene anaukitsidwa kwa akufa,+ kuti tibale zipatso+ kwa Mulungu.
5 Chifukwa pamene tinali kukhala mogwirizana ndi thupi,+ zilakolako za uchimo zimene zinaonekera chifukwa cha Chilamulo zinali kugwira ntchito m’ziwalo zathu kuti tibale zipatso za imfa.+
6 Koma tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,+ chifukwa tafa+ ku chilamulo chimene chinali kutimanga chija, kuti tikhale akapolo+ m’njira yatsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ osati m’njira yakale motsogoleredwa ndi malamulo olembedwa.+
7 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo?+ Ayi m’pang’ono pomwe! Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo+ zikanakhala kuti panalibe Chilamulo. Ndiponso, mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje+ zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”+
8 Koma chifukwa cha lamulo,+ uchimo unapeza njira yondichititsa kukhala wosirira chinthu chilichonse mwansanje. Chifukwa popanda chilamulo, uchimo unali wakufa.+
9 Ndinalitu wamoyo chilamulo chisanabwere.+ Koma pamene malamulo anafika,+ uchimo unakhalanso ndi moyo, koma ineyo ndinafa.+
10 Tsopano ine ndinaona lamulo lopatsa moyolo+ kuti ndi lobweretsa imfa.+
11 Pakuti chifukwa cha lamulo, uchimo unapeza njira yondinyenga+ ndipo unandipha.
12 Choncho, Chilamulo kumbali yake n’choyera,+ ndipo malamulo ndi oyera, olungama+ ndi abwino.+
13 Ndiye kodi chinthu chabwino chinakhala imfa kwa ine? Ayi ndithu! Koma uchimo ndiwo unakhala imfa kwa ine, kuti uonekere kuti ndi umene ukubala imfa mwa ine kudzera m’chinthu chabwinocho,+ kuti kudzera m’malamulo, uchimowo uonekere kuti ndi woipa kwambiri.+
14 Pakuti tikudziwa kuti Chilamulo n’chauzimu,+ koma ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.+
15 Sindimvetsetsa kuti n’chifukwa chiyani ndimachita zinthu motere. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita.
16 Komabe, ngati zimene sindifuna kuchita ndi zimene ndimachita,+ ndikuvomereza kuti Chilamulo ndi chabwino.+
17 Koma tsopano amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene uli mwa ine.+
18 Ndikudziwa kuti mwa ine, ndikunenatu za m’thupi langa, simukhala kanthu kabwino.+ Pakuti ndimafuna+ kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.+
19 Chinthu chabwino chimene ndimafuna kuchita sindichita,+ koma choipa chimene sindifuna kuchita ndi chimene ndimachita.
20 Tsopano ngati zimene sindifuna ndi zimene ndikuchita, amene akuchita zimenezo si inenso ayi, koma uchimo umene ukukhala mwa ine.+
21 Chotero kwa ine, ndimapeza lamulo ili lakuti: Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino,+ choipa chimakhala chili ndi ine.+
22 Mumtima mwanga+ ndimasangalala kwambiri+ ndi chilamulo cha Mulungu,
23 koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga+ chikumenyana+ ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga+ n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo+ chimene chili m’ziwalo zanga.
24 Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?+
25 Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.+ Chotero, m’maganizo mwanga ineyo ndine kapolo wa chilamulo cha Mulungu,+ koma m’thupi langa ndine kapolo wa chilamulo cha uchimo.+