Aroma 6:1-23

6  Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tipitirize kuchimwa kuti kukoma mtima kwakukulu kuwonjezeke?+  Tisatero ayi! Popeza kuti tinafa ku uchimo,+ kodi tipitirize kuchimwa chifukwa chiyani?+  Kapena simudziwa kuti tonsefe amene tinabatizidwa ndipo tsopano tili mu mgwirizano ndi Khristu Yesu+ tinabatizidwanso mu imfa yake?+  Motero tinaikidwa m’manda+ pamodzi ndi iye pobatizidwa mu imfa yake, kuti monga mmene Khristu anaukitsidwira kwa akufa mwa ulemerero wa Atate,+ ifenso tiziyenda m’moyo watsopano.+  Chifukwa ngati tagwirizana naye pokhala ndi imfa yofanana ndi yake,+ ndithudi tidzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.+  Pakuti tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi iye pamtengo,+ kuti thupi lathu lauchimo likhale ngati lakufa,+ kuti tisapitirize kukhala akapolo a uchimo.+  Chifukwa munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.+  Ndiponso, ngati tinafadi limodzi ndi Khristu, timakhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye.+  Tikudziwa kuti pamene tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa,+ sadzafanso.+ Imfa sikuchitanso ufumu pa iye. 10  Popeza imfa imene anafa, anafa kuti achotse uchimo kamodzi kokha basi,+ koma moyo umene ali nawo, akukhala nawo kuti azichita chifuniro cha Mulungu.+ 11  Momwemonso inuyo dzioneni ngati akufa+ ku uchimo koma amoyo+ kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. 12  Choncho musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu+ m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.+ 13  Ndipo musapereke ziwalo zanu ku uchimo+ kuti zikhale zida zochitira zinthu zosalungama,+ koma dziperekeni kwa Mulungu monga anthu amene auka kwa akufa.+ Ziwalo zanunso muzipereke kwa Mulungu monga zida+ zochitira chilungamo. 14  Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa simuli pansi pa chilamulo+ koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.+ 15  Ndiye zikatero? Kodi tichite tchimo chifukwa chakuti sitili m’chilamulo+ koma m’kukoma mtima kwakukulu?+ Tisayese n’komwe kutero! 16  Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake chifukwa chakuti mumamumvera,+ kaya mukhale akapolo a uchimo+ umene umatsogolera ku imfa,+ kapena mukhale akapolo a kumvera+ kumene kumatsogolera ku chilungamo?+ 17  Koma tikuyamika Mulungu kuti ngakhale poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mtundu wa chiphunzitso chimene chinaperekedwa kwa inu.+ 18  Inde, popeza munamasulidwa+ ku uchimo, munakhala akapolo+ a chilungamo.+ 19  Ndikulankhulatu monga munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu.+ Pakuti mmene munaperekera ziwalo zanu+ kuti zikhale akapolo a zonyansa+ ndiponso akapolo a kusamvera malamulo ndi cholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a chilungamo kuti muzichita ntchito za chiyero.+ 20  Popeza pamene munali akapolo a uchimo,+ munali omasuka ku chilungamo. 21  Kodi pa nthawiyo munali kukhala ndi zipatso zotani?+ Zinali zinthu+ zimene tsopano mumachita nazo manyazi. Ndipo pothera pake pa zinthu zimenezo ndi imfa.+ 22  Koma tsopano chifukwa munamasulidwa ku uchimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu,+ mukukhala ndi zipatso+ za chiyero, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.+ 23  Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa,+ koma mphatso+ imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha+ kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+

Mawu a M'munsi