Aroma 3:1-31
3 Choncho, kodi Myuda+ ndi woposa ena motani? Kapena kodi phindu la mdulidwe n’chiyani?+
2 Iye amaposadi ena kwambiri m’njira iliyonse. Choyamba, chifukwa chakuti mawu opatulika a Mulungu+ anaikidwa m’manja mwa Ayuda.
3 Nanga ngati ena sanasonyeze chikhulupiriro,+ kodi chifukwa chakuti alibe chikhulupiriro+ ndiye kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kopanda pake?+
4 Ayi! Koma Mulungu akhale wonena zoona,+ ngakhale kuti munthu aliyense angapezeke kukhala wonama,+ monganso Malemba amanenera kuti: “Mukamalankhula mumalankhula zachilungamo, kuti mupambane pamene mukuweruzidwa.”+
5 Komabe, ngati kulungama kwa Mulungu+ kukuonekera chifukwa cha kusalungama kwathu, ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tingati Mulungu ndi wosalungama+ poonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula mmene anthu+ amalankhulira.)
6 Ayi! Chifukwa Mulungu akapanda kutero, kodi dziko adzaliweruza motani?+
7 Tsopano ngati chifukwa cha bodza langa choonadi cha Mulungu+ chaonekera kwambiri, ndipo zimenezo zamubweretsera ulemerero, n’chifukwa chiyaninso ndikuweruzidwabe kukhala wochimwa?+
8 Ndilekeranji kunena zimene amatinamizira zija,+ ndiponso zimene ena amati timanena zakuti: “Tiyeni tichite zoipa kuti pakhale zinthu zabwino”?+ Chiweruzo+ chowafikira anthu amenewo n’chogwirizana ndi chilungamo.+
9 Ndiye zikatero? Kodi tili pabwino kuposa ena?+ Ayi! Pakuti tanena kale poyamba paja kuti onse, Ayuda ndi Agiriki, ndi ochimwa+
10 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+
11 Palibe amene ali wozindikira ngakhale pang’ono, palibiretu amene akuyesetsa kupeza Mulungu.+
12 Anthu onse apanduka, onse pamodzi akhala opanda pake. Palibe amene akusonyeza kukoma mtima, palibiretu ndi mmodzi yemwe.”+
13 “Mmero wawo ndi manda otseguka. Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.”+ “M’milomo yawo muli poizoni wa njoka.”+
14 “Ndipo m’kamwa mwawo mwadzaza mawu otukwana ndi opweteka.”+
15 “Mapazi awo amathamangira kukhetsa magazi.”+
16 “Kusakaza ndi kusautsa kuli m’njira zawo,+
17 ndipo sadziwa njira ya mtendere.”+
18 “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.”+
19 Tikudziwa kuti zinthu zonse zimene Chilamulo+ chimanena chimazinena kwa amene ali m’Chilamulo, kuti pakamwa paliponse patsekedwe+ ndipo dziko lonse likhale loyenera+ kulandira chilango cha Mulungu.+
20 Chotero pamaso pake palibe munthu amene adzayesedwe wolungama+ mwa ntchito za chilamulo,+ popeza chilamulo chimachititsa kuti tidziwe uchimo molondola.+
21 Koma tsopano, zaonekera kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu+ popanda kutsatira Chilamulo. Zimenezi zinatchulidwanso+ m’Chilamulo+ ndi m’Zolemba za aneneri.+
22 Kuoneka wolungama pamaso pa Mulungu kumeneku kungatheke mwa kukhulupirira Yesu Khristu,+ ndipo ndi kotheka kwa onse okhala ndi chikhulupiriro.+ Popeza palibe kusiyanitsa.+
23 Pakuti onse ndi ochimwa+ ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.+
24 Ndiponso, kuyesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo+ lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.+
25 Mulungu anam’pereka monga nsembe yachiyanjanitso,+ mwa kukhala ndi chikhulupiriro m’magazi ake.+ Mulungu anachita izi pofuna kuonetsa chilungamo chake pokhululuka machimo+ amene anachitika kale, pamene iye anali kusonyeza khalidwe losakwiya msanga,+
26 ndipo akuonetsa chilungamo chake+ m’nyengo inoyo pakutcha munthu amene ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu kuti ndi wolungama.+
27 Chotero, kodi pamenepa palinso chifukwa chodzitama nacho?+ Palibiretu. Malinga ndi chilamulo chiti?+ Chija chofuna ntchito?+ Ndithudi ayi, koma mwa lamulo la chikhulupiriro.+
28 Popeza tsopano taona kuti munthu amayesedwa wolungama mwa chikhulupiriro, osati mwa ntchito za chilamulo.+
29 Kapena kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha?+ Kodi salinso Mulungu wa anthu a mitundu ina?+ Inde, iye alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina,+
30 ngati Mulungu alidi mmodzi.+ Iye ndi amene adzayese anthu odulidwa+ kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro, ndiponso anthu osadulidwa+ adzawayesa olungama mwa chikhulupiriro chawo.
31 Koma kodi tikuthetsa chilamulo mwa chikhulupiriro chathu?+ Ayi! M’malomwake, tikulimbikitsa chilamulo.+