Aroma 8:1-39
8 Chotero amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu.+
2 Pakuti chilamulo+ cha mzimu+ umene umapatsa moyo+ mwa Khristu Yesu chakumasulani+ ku chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.+
3 Mulungu anatsutsa uchimo mwa kugwiritsa ntchito thupi potumiza Mwana wake+ m’thupi lofanana ndi lauchimo+ kuti athane ndi uchimo.+ Pakuti Chilamulo sichinathe kuchita zimenezi+ pokhala chofooka+ chifukwa cha thupi.
4 Mulungu anachita izi kuti ife amene tikuyenda motsatira za mzimu,+ osati motsatira zofuna za thupi, tikwaniritse miyezo yolungama ya Chilamulo.+
5 Chifukwa otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi,+ koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.+
6 Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa,+ koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu+ kumabweretsa moyo ndi mtendere,
7 chifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani+ ndi Mulungu, popeza thupi siligonjera+ chilamulo cha Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingachigonjere.
8 Choncho, otsatira zofuna za thupi+ sangakondweretse Mulungu.
9 Komabe, inu mukutsatira za mzimu,+ osati za thupi, ngati mzimu wa Mulungu ukukhaladi mwa inu.+ Ngati wina alibe mzimu wa Khristu,+ ameneyu si wa Khristu.
10 Koma ngati Khristu ali wogwirizana ndi inu,+ ngakhale kuti thupi ndi lakufa chifukwa cha uchimo, mzimu ndiwo moyo+ chifukwa cha chilungamo.
11 Chotero, mzimu wa amene anaukitsa Yesu kwa akufa ukakhala mwa inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu kwa akufa+ adzachititsanso matupi anu otha kufawo kukhala ndi moyo+ mwa mzimu wake umene ukukhala mwa inu.
12 Choncho abale, tili ndi ngongole, osati kwa thupi kuti tizikhala motsatira zofuna za thupi.+
13 Pakuti ngati mukukhala motsatira zofuna za thupi, ndiye kuti mosakayikira mudzafa.+ Koma mukapha zochita za thupi+ mwa mzimu, mudzakhala ndi moyo.
14 Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewa ndiwo ana a Mulungu.+
15 Popeza simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha,+ koma munalandira mzimu+ wakuti mukhale ana,+ umene timafuula nawo kuti: “Abba,*+ Atate!”
16 Pakuti mzimuwo+ umachitira umboni+ limodzi ndi mzimu wathu+ kuti ndife ana a Mulungu.+
17 Chotero, ngati tili ana, tilinso olandira cholowa: Olandira cholowa a Mulungu, komanso olandira cholowa anzake+ a Khristu, malinga ngati tivutika+ naye limodzi kuti tikalandire ulemerero limodzi ndi iye.+
18 Ndiye chifukwa chake ndikuona kuti masautso+ amene tili nawo tsopano si kanthu powayerekeza ndi ulemerero+ umene udzaonekere kudzera mwa ife.
19 Pakuti chilengedwe+ chikudikira mwachidwi+ nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu udzaonekere.+
20 Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo+
21 chakuti chilengedwecho+ chidzamasulidwa+ ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.
22 Pakuti tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.
23 Si zokhazo ayi, komanso ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambirira+ zomwe ndi mzimu, tikubuula+ mumtima mwathu pamene tikudikira ndi mtima wonse kuti titengedwe kukhala ana a Mulungu,+ kumasulidwa ndi dipo* kuti tituluke m’matupi athu.
24 Pakuti tinapulumutsidwa tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ koma chimene chikuyembekezedwa chikaoneka sichikhalanso choyembekezedwa, chifukwa munthu akaona chinthu chimene anali kuchiyembekezera, kodi amachiyembekezanso?
25 Koma ngati tikuyembekezera+ chimene sitikuchiona,+ timachidikirabe mopirira.+
26 Mofanana ndi zimenezi, mzimu+ umatithandiza pa zofooka zathu.+ Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa,+ koma mzimu+ umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza.
27 Koma iye amene amasanthula mitima+ amadziwa zimene mzimu ukutanthauza,+ chifukwa umachonderera m’malo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.+
28 Tikudziwa tsopano kuti Mulungu amagwirizanitsa zochita zake zonse+ pofuna kupindulitsa amene amakonda Mulungu, anthu oitanidwa mogwirizana ndi cholinga chake.+
29 Amatero chifukwa amene anawadziwa choyamba+ anawasankhiratu+ kuti adzakhale ofanana+ ndi Mwana wake,+ kuti iye akhale woyamba kubadwa+ pakati pa abale ake ambiri.+
30 Ndiponso, amene anawasankhiratu+ ndi amenenso anawaitana,+ ndipo amene anawaitanawo ndi amenenso anawayesa olungama.+ Kenako amene anawayesa olungama ndi amenenso anawapatsa ulemerero.+
31 Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+
32 Iye amene sanaumire ngakhale Mwana wake+ koma anamupereka m’malo mwa ife tonse,+ angalephere bwanji kutipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo?+
33 Ndani adzasumira mlandu anthu a Mulungu ochita kusankhidwa?+ Mulungu ndiye amawayesa olungama.+
34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, zoonadi, amenetu anaukitsidwa kwa akufa. Iye ali kudzanja lamanja+ la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.+
35 Ndani adzatilekanitsa ndi chikondi cha Khristu?+ Chisautso kodi, kapena zowawa, chizunzo, njala, usiwa, zoopsa, kapena lupanga?+
36 Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.”+
37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi+ kudzera mwa iye amene anatikonda.
38 Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo,+ angelo,+ maboma,+ zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu,+
39 msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Bambo anga!”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.