Aroma 5:1-21

5  Chotero, popeza tsopano tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,+ tiyeni tikhale pa mtendere+ ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Mwa ameneyunso, ndiponso chifukwa cha chikhulupiriro, takhala ndi ufulu wolowa+ m’kukoma mtima kwakukulu, mmene tilimo tsopano. Ndipo tiyeni tikondwere chifukwa cha chiyembekezo+ cha ulemerero wa Mulungu.  Si zokhazo, koma tiyeni tikondwere pamene tili m’masautso,+ popeza tikudziwa kuti chisautso chimabala chipiriro.+  Chipiriro chimachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu.+ Kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumabala chiyembekezo,+  ndipo chiyembekezocho sichitikhumudwitsa+ chifukwa Mulungu wadzaza chikondi chake+ m’mitima yathu+ kudzera mwa mzimu woyera+ umene tinapatsidwa.  Popeza pamene tinali ofooka,+ Khristu anafera anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwiratu.+  Pakuti n’chapatali kuti munthu wina afere munthu wolungama.+ Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufera+ munthu wabwino.+  Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake+ kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+  Tsopano adzachita zoposa pamenepo mwa kutipulumutsa ku mkwiyo wake+ kudzera mwa Khristu, popeza tayesedwa olungama kudzera m’magazi a Khristuyo.+ 10  Pakuti ngati pamene tinali adani,+ tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake,+ nanji tsopano pamene tayanjanitsidwa, tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake.+ 11  Ndipo si zokhazo, koma tikukondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene tayanjanitsidwa ndi Mulungu kudzera mwa iye.+ 12  Ndiye chifukwa chake monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi,+ ndi imfa+ kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa+ . . . 13  Paja Chilamulo chisanabwere, uchimo unalimo kale m’dziko, koma munthu saimbidwa mlandu wa kuchimwa pamene palibe lamulo.+ 14  Ngakhale zili choncho, imfa inalamulira monga mfumu kuyambira kwa Adamu mpaka kwa Mose,+ ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe monga mmene anachimwira Adamu,+ yemwe ndi wolingana ndi iye amene anali kubwera.+ 15  Koma mmene zilili ndi mphatsoyi si mmene zinalili ndi uchimowo. Popeza ngati mwa uchimo wa munthu mmodzi ambiri anafa, kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere zinasefukira kwa anthu ambiri.+ Mphatso yaulere imeneyi inaperekedwa limodzi ndi kukoma mtima kwakukulu kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu. 16  Ndiponso, mmene zilili ndi mphatso yaulereyi+ zasiyana ndi mmene zinthu zinachitikira kudzera mwa munthu mmodzi amene anachimwa.+ Pakuti chiweruzo+ chimene chinatsatira tchimo limodzi lija chinabweretsa uchimo kwa onse,+ koma mphatso imene inatsatira machimo ambiri, inachititsa kuti anthu atchedwe olungama.+ 17  Ngati chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo+ imfa inalamulira monga mfumu+ kudzera mwa munthuyo, amene alandira kukoma mtima kwakukulu+ kochuluka ndiponso mphatso yaulere+ yaikuluyo ya chilungamo, adzakhala ndi moyo ndi kulamulira monga mafumu+ kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.+ 18  Chotero, mmene zinakhalira kuti mwa uchimo umodzi anthu kaya akhale amtundu wotani anaweruzidwa kukhala ochimwa,+ momwemonso mwa kuchita chinthu chimodzi cholungamitsa,+ anthu kaya akhale amtundu wotani+ akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.+ 19  Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri+ anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera+ kwa munthu mmodziyu, ambiri+ adzakhala olungama.+ 20  Chilamulo+ chinalowapo kuti kuchimwa kuonekere kuti ndi kwakukulu.+ Koma pamene uchimo+ unawonjezeka, kukoma mtima kwakukulu+ kunasefukiranso. 21  Chifukwa chiyani? Kuti mmene uchimo unalamulira monga mfumu pamodzi ndi imfa,+ momwemonso kukoma mtima kwakukulu+ kulamulire monga mfumu kudzera m’chilungamo. Zimenezi zichitike kuti moyo wosatha+ ubwere kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

Mawu a M'munsi