Aroma 12:1-21

12  Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu abale, kuti mupereke matupi anu+ ngati nsembe+ yamoyo,+ yoyera+ ndi yovomerezeka kwa Mulungu,+ ndiyo utumiki wopatulika+ mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.+  Musamatengere+ nzeru za nthawi* ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu,+ kuti muzindikire+ chimene chili chifuniro+ cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.  Pakuti mwa kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino,+ malinga ndi chikhulupiriro+ chimene Mulungu wamupatsa.+  Pakuti monga tilili ndi ziwalo zambiri+ m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana,  momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi+ mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi chiwalo cha mnzake.+  Chotero, popeza kuti tili ndi mphatso zosiyanasiyana+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu+ kumene tinapatsidwa, kaya tili ndi mphatso ya ulosi, tiyeni tilosere malinga ndi chikhulupiriro chimene tapatsidwa.  Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tichitebe utumikiwo.+ Amene akuphunzitsa,+ aziphunzitsa ndithu.+  Wochenjeza, aike mtima wake pa kuchenjeza.+ Wogawa, agawe mowolowa manja.+ Wotsogolera,+ atsogolere mwakhama. Ndipo wosonyeza chifundo,+ achite zimenezo mokondwa.  Chikondi+ chanu chisakhale cha chiphamaso.+ Nyansidwani ndi choipa,+ gwiritsitsani chabwino.+ 10  Pokonda abale,+ khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu,+ khalani patsogolo. 11  Musakhale aulesi pa ntchito yanu.+ Yakani ndi mzimu.+ Tumikirani Yehova monga akapolo.+ 12  Kondwerani ndi chiyembekezocho.+ Pirirani chisautso.+ Limbikirani kupemphera.+ 13  Gawanani ndi oyera malinga ndi zosowa zawo.+ Khalani ochereza.+ 14  Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani.+ Muzidalitsa,+ osatemberera ayi.+ 15  Sangalalani ndi anthu amene akusangalala.+ Lirani ndi anthu amene akulira. 16  Muziona ena mmene inuyo mumadzionera.+ Musamaganize modzikweza,+ koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musadziyese anzeru.+ 17  Musabwezere choipa pa choipa.+ Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. 18  Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere+ ndi anthu onse, monga mmene mungathere. 19  Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+ 20  Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.+ Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.”+ 21  Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.