Aroma 9:1-33
9 Ndikunena zoona+ mwa Khristu, sindikunama ayi.+ Ine pamodzi ndi chikumbumtima changa tikuchitira umboni mwa mzimu woyera,
2 kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.+
3 Ndikanakonda kuti ineyo ndichotsedwe kwa Khristu monga wotembereredwa m’malo mwa abale anga,+ amene ali anthu a mtundu wanga.+
4 Amenewa ndi Aisiraeli,+ amene Mulungu anawatenga kukhala ana ake.+ Anawapatsanso ulemerero,+ mapangano,+ Chilamulo,+ utumiki wopatulika+ ndi malonjezo.+
5 Iwo ndi ana a makolo akale aja.+ Komanso Khristu monga munthu,+ anatuluka pakati pawo. Mulungu,+ amene ndiye wamkulu pa zinthu zonse, atamandike kwamuyaya. Ame.
6 Komabe, sizili ngati kuti mawu a Mulungu analephera.+ Pakuti si onse ochokera kwa Isiraeli amene alidi “Aisiraeli.”+
7 Ndiponso si onse amene ali ana chifukwa chongokhala mbewu ya Abulahamu.+ Koma Malemba amati, “Amene adzatchedwa ‘mbewu yako’ adzachokera mwa Isaki.”+
8 Izi zikutanthauza kuti, si ana akuthupi+ amene alidi ana a Mulungu,+ koma ana a lonjezo+ ndiwo amayesedwa mbewu.
9 Popeza lonjezo lija linati: “Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+
10 Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi imeneyo yokha ayi, koma linaperekedwanso kwa Rabeka pamene anali ndi pakati pa mapasa+ a Isaki kholo lathu lija.
11 Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chilichonse chabwino kapena choipa,+ kuti cholinga cha Mulungu powasankha chikhalebe chodalira Iye amene amaitana,+ osati chodalira ntchito,
12 Rabeka anauzidwa kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.”+
13 Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”+
14 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Mulungu alibe chilungamo?+ Ayi si zimenezo!
15 Pakuti iye anauza Mose kuti: “Amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo, ndipo ndidzamvera chisoni aliyense amene ndikufuna kumumvera chisoni.”+
16 Chotero, sizidalira munthu wofunayo kapena amene akuthamanga, koma Mulungu,+ amene ali ndi chifundo.+
17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+
18 Chotero, iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo,+ koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+
19 Mwina unganene kwa ine kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani angatsutse chifuniro chake chimene chinanenedwa?”+
20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+
21 Kodi simudziwa kuti woumba mbiya+ ali ndi ufulu woumba chiwiya china cholemekezeka, china chonyozeka kuchokera pa dongo limodzi?+
22 Bwanji ngati Mulungu analekerera moleza mtima kwambiri ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa ngakhale kuti akufuna kuonetsa mkwiyo wake ndi mphamvu zake?+
23 Ndiponso bwanji ngati anachita zimenezo kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake+ kwa ziwiya+ zachifundo, zomwe anazikonzeratu kuti zikhale zaulemerero,+
24 zimene ndi ifeyo amene anatiitana osati kuchokera mwa Ayuda okha komanso mwa mitundu ina?+
25 Zilinso monga mmene ananenera m’buku la Hoseya kuti: “Anthu amene si anthu anga+ ndidzawatcha ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sanali wokondedwa ndidzamutcha ‘wokondedwa.’+
26 Ndipo pamalo pamene anauzidwapo kuti, ‘Inu sindinu anthu anga,’ pamalo omwewo adzatchedwa ‘ana a Mulungu wamoyo.’”+
27 Komanso, Yesaya analankhula mofuula zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ochuluka ngati mchenga wa m’nyanja,+ ndi ochepa okha amene adzapulumuke.+
28 Pakuti Yehova adzazenga milandu padziko lapansi, ndi kuimaliza yonse mwachangu.”+
29 Ndiponso, monga Yesaya ananeneratu kuti: “Yehova wa makamu+ akanapanda kutisiyira mbewu, tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”+
30 Ndiye tinene kuti chiyani? Tinene kuti, ngakhale kuti anthu a mitundu ina sanatsatire chilungamo, iwo anapeza chilungamo+ chimene chimapezeka chifukwa cha chikhulupiriro.+
31 Koma ngakhale kuti Aisiraeli anali kutsatira lamulo la chilungamo, sanalipeze lamulolo.+
32 Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo sanalitsatire mwa chikhulupiriro, koma malinga ndi kuganiza kwawo, analitsatira mwa ntchito.+ Iwo anakhumudwa “pamwala wokhumudwitsa”+
33 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Inetu ndikuika mwala+ wopunthwitsa ndiponso mwala wokhumudwitsa+ m’Ziyoni, koma munthu wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”+