Aroma 1:1-32

1  Ndine Paulo kapolo+ wa Yesu Khristu, woitanidwa+ kuti ndikhale mtumwi,+ ndiponso wosankhidwa kuti ndilalikire uthenga wabwino wa Mulungu.+  Uthenga umenewu anaulonjeza kalekale kudzera mwa aneneri+ ake m’Malemba oyera.  Uthengawo umanena za Mwana wake, amene anatuluka m’mbewu ya Davide+ monga munthu,+  koma amene Mulungu mwa mphamvu+ yake anam’lengeza kukhala Mwana wake+ mwa mzimu woyera+ pomuukitsa kwa akufa.+ Ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu.  Kudzera mwa iyeyu, tinalandira kukoma mtima+ kwakukulu ndiponso ndinasankhidwa kukhala mtumwi+ kuti mitundu yonse ikhale yomvera mwa chikhulupiriro+ chifukwa cha dzina lake.  Pakati pa mitundu imeneyo palinso inuyo amene munaitanidwa kuti mukhale ake a Yesu Khristu.  Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma monga okondedwa a Mulungu, oitanidwa+ kukhala oyera:+ Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere+ wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu+ zikhale ndi inu.  Choyamba, ndikuyamika+ Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti chikhulupiriro chanu chikusimbidwa+ m’dziko lonse.  Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ndi moyo wanga wonse polalikira uthenga wabwino wonena za Mwana wake, ndiye mboni yanga+ ya mmene ndimakutchulirani m’mapemphero anga nthawi zonse.+ 10  Ndimamupempha kuti ngati n’kotheka mwa chifuniro+ chake, ulendo uno wokha ndibwere kwanuko. 11  Popeza ndikulakalaka kukuonani+ kuti ndikugawireni mphatso+ inayake yauzimu kuti mukhale olimba, 12  kapena kuti tidzalimbikitsane+ mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.+ 13  Koma sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale,+ kuti nthawi zambiri ndinkafuna kubwera kwanuko,+ koma pakhala zondilepheretsa mpaka pano. Ndikufuna kuti ndidzapeze zipatso+ pakati pa inu monganso ndinachitira pakati pa mitundu ina yonse. 14  Ineyo ndili ndi ngongole kwa Agiriki, kwa anthu amene si Agiriki, kwa anthu anzeru+ ndi kwa opusa. 15  Chotero ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino+ kwa inunso kumeneko ku Roma.+ 16  Pakuti sindichita nawo manyazi+ uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu+ ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba kwa Myuda+ kenako kwa Mgiriki.+ 17  Mu uthenga wabwinowu, chilungamo+ cha Mulungu chimaululidwa chifukwa cha chikhulupiriro cha munthu.+ Zikatero, chikhulupiriro cha munthuyo chimalimbanso monga mmene Malemba amanenera kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+ 18  Mkwiyo wa Mulungu+ ukusonyezedwa kuchokera kumwamba pa anthu onse osaopa Mulungu ndi ochita zosalungama+ amene akupondereza choonadi+ m’njira yosalungama.+ 19  Chifukwa chake n’chakuti, zimene anthu angathe kudziwa ponena za Mulungu zikuonekera pakati pawo,+ popeza Mulungu anazisonyeza kwa iwo.+ 20  Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo,+ makhalidwe a Mulungu osaoneka+ ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu+ wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga+ moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.+ 21  Chifukwa chakuti, ngakhale anam’dziwa Mulungu, iwo sanam’patse ulemerero monga Mulungu kapena kumuyamikira.+ M’malomwake anayamba kulingalira zinthu zopanda pake+ ndipo mtima wawo wopusawo unachita mdima.+ 22  Ngakhale anali kunena motsimikiza kuti ndi anzeru, iwo anakhala opusa+ 23  ndipo anasandutsa ulemerero+ wa Mulungu amene sawonongeka kukhala ngati chifaniziro+ cha munthu, mbalame, zolengedwa za miyendo inayi ndi zokwawa,+ zonsezo zimene zimawonongeka. 24  Chotero malinga ndi zilakolako za m’mitima mwawo, Mulungu anawasiya kuti achite zonyansa,+ kuti matupi awo+ achitidwe chipongwe.+ 25  Anateronso kwa anthu amene anasinthanitsa choonadi+ cha Mulungu ndi bodza+ polambira chilengedwe ndi kuchichitira utumiki wopatulika m’malo mochita zimenezo kwa Iye amene anazilenga, amene ndi wotamandika kosatha. Ame. 26  Ndiye chifukwa chake Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana,+ popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa.+ 27  Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi+ n’kumatenthetsana okhaokha mwachiwawa m’chilakolako choipa, amuna ndi amuna anzawo,+ kuchitirana zonyansa+ ndi kulandiriratu mphoto+ yoyenerera kulakwa kwawo.+ 28  Ndiponso monga mmene iwo sanafunire kumudziwa Mulungu molondola,+ iye anawasiya ndi maganizo awo oipa,+ kuti azichita zinthu zosayenerazo,+ 29  popeza anadzazidwa ndi zosalungama+ zonse, kuipa+ konse, kusirira konse kwa nsanje,+ ndi uchimo+ wonse. Mtima wawo unadzala kaduka,+ umbanda,+ ndewu,+ chinyengo+ ndi njiru.+ Anakonda manong’onong’o+ 30  ndi miseche.+ Anakhala odana ndi Mulungu, achipongwe,+ odzikweza,+ odzimva,+ oyambitsa zoipa,+ osamvera makolo,+ 31  osazindikira,+ osasunga mapangano,+ opanda chikondi chachibadwa+ ndiponso opanda chifundo.+ 32  Amenewa ngakhale kuti amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu,+ lakuti amene amachita zinthu zimenezi n’ngoyenera imfa,+ iwo amapitiriza kuzichita. Kuwonjezera apo, amagwirizananso+ ndi anthu amene amachita zimenezo.

Mawu a M'munsi