Aroma 11:1-36
11 Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake?+ Ayi ndithu! Paja inenso ndine Mwisiraeli,+ wa mbewu ya Abulahamu, wa fuko la Benjamini.+
2 Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyambirira kuwavomereza.+ Kodi ndithu simukudziwa kuti Lemba limati chiyani za Eliya, pamene anali kuchonderera Mulungu motsutsa Aisiraeli?+ Limati:
3 “Yehova, iwo apha aneneri anu, agumula maguwa anu ansembe, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano akufunafuna moyo wanga.”+
4 Koma kodi mawu a Mulungu+ anati chiyani kwa iyeyo? Anati: “Ndadzisungira anthu 7,000, amene sanagwadire Baala.”+
5 Chotero, pa nthawi ino alipo ena ochepa+ amene anasankhidwa+ mwa kukoma mtima kwakukulu.
6 Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwakukulu,+ sanasankhidwe chifukwa cha ntchito zawo ayi.+ Zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima kwakukulu.+
7 Ndiye zili bwanji pamenepa? Chimene Aisiraeli akuchifunitsitsa sanachipeze,+ koma anthu osankhidwa+ ndi amene anachipeza. Enawo anaumitsa mitima yawo+
8 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tatikulu,+ maso osaona ndi makutu osatha kumva, kufikira lero.”+
9 Ndiponso Davide anati: “Tebulo lawo likhale msampha, mbuna, chopunthwitsa ndi chilango kwa iwo.+
10 Maso awo achite mdima kuti asaone, ndipo weramitsani msana wawo nthawi zonse.”+
11 Ndiyeno ndifunse, Kodi anapunthwa mpaka kugweratu?+ Ayi! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo+ pali chipulumutso kwa anthu a mitundu ina,+ kuti olakwawo achite nsanje.+
12 Chotero ngati kulakwa kwawo kukutanthauza chuma ku dziko, ndipo kuchepa kwawo kukutanthauza chuma kwa anthu a mitundu ina,+ bwanji nanga za chiwerengero chawo chokwanira?+ Chidzatanthauzatu zazikulu kuposa pamenepo!
13 Tsopano ndikulankhula kwa inu ochokera m’mitundu ina. Malinga n’kuti ndine mtumwi+ weniweni wotumidwa kwa mitundu ina,+ ndimalemekeza+ utumiki wanga,+
14 kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga kuchita nsanje ndi kupulumutsapo+ ena a iwo.+
15 Chifukwa ngati dziko layanjidwa ndi Mulungu chifukwa chakuti iwo anatayidwa,+ ndiye kuti akadzalandiridwa+ zidzatanthauza moyo kuchokera ku imfa.
16 Ndiponso, ngati mbali ya mtanda imene yadyedwa monga chipatso choyambirira+ ili yoyera, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyeranso. Ngati muzu uli woyera,+ ndiye kuti nthambi nazonso ndi zoyera.
17 Ngati nthambi zina zinadulidwa, koma iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wam’tchire, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala+ ndipo unayamba kugawana nawo muzu wamafuta+ wa mtengo wa maoliviwo,+
18 usakondwere monyoza nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati ukunyoza nthambizo,+ kumbukira kuti si iwe amene ukuchirikiza muzu,+ koma muzu ndi umene ukuchirikiza iweyo.+
19 Komatu tsopano unganene kuti: “Nthambi zina zinadulidwa+ kuti alumikizepo ine.”+
20 N’zoonadi! Iwo anadulidwa chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo waimirira chifukwa cha chikhulupiriro.+ Taya maganizo odzikuzawo,+ koma khala ndi mantha.+
21 Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachilengedwe, sadzakulekereranso iweyo.+
22 Choncho taona kukoma mtima+ komanso kusalekerera+ kwa Mulungu. Amene anagwa anaona kusalekerera+ kwake, koma iweyo ukuona kukoma mtima kwa Mulungu, malinga ngati ukukhalabe+ m’kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa.+
23 Iwonso ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo,+ pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso.
24 Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera m’tchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe, unalumikizidwa+ kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si kwapafupi kulumikiza nthambi izi kumtengo wawo umene zinadulidwako?+
25 Pakuti sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika+ chimenechi, kuopera kuti mungadzione ngati ochenjera. Chinsinsi chopatulikacho n’chakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo+ mpaka chiwerengero chonse+ cha anthu ochokera m’mitundu ina chitakwanira.+
26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+
27 Limeneli lidzakhala pangano langa ndi iwo,+ pamene ndidzawachotsera machimo awo.”+
28 Zoonadi, pa nkhani ya uthenga wabwino iwo ndi adani a Mulungu, ndipo zimenezi zapindulitsa inu.+ Koma kunena za kusankha kwa Mulungu, iwo ndi okondedwa ake chifukwa cha makolo awo oyambirira.+
29 Mulungu sadzadandaula+ chifukwa cha mphatso zake ndiponso chifukwa chakuti anawaitana.
30 Pakuti monga mmene inuyo munalili osamvera+ Mulungu koma tsopano mwasonyezedwa chifundo+ chifukwa cha kusamvera kwawo,+
31 iwowa tsopano akhala osamvera, zimene zapangitsa kuti inuyo musonyezedwe chifundo,+ kuti iwonso tsopano asonyezedwe chifundo.
32 Popeza Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvera,+ kuti onsewo awasonyeze chifundo.+
33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?
34 Pakuti “ndani akudziwa maganizo a Yehova,+ kapena ndani angakhale phungu wake?”+
35 Kapenanso, “Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?”+
36 Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake.+ Ulemerero ukhale wake kwamuyaya.+ Ame.