Aroma 4:1-25
4 Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za Abulahamu kholo lathu?+
2 Mwachitsanzo, chikhala kuti Abulahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito,+ akanakhala ndi chifukwa chodzitamandira, koma osati kwa Mulungu.
3 Kodi lemba limati chiyani paja? Limati: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”+
4 Chifukwa munthu amene wagwira ntchito+ saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu,+ koma ngati ngongole.+
5 Munthu amene sadalira ntchito zake koma amakhulupirira+ Mulungu, amayesedwa wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake,+ pakuti Mulungu amatha kuona munthu wosatsatira malamulo ake kukhala wolungama.
6 Davide ananena kuti munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama popanda munthuyo kuchita ntchito ndi wodala. Iye anati:
7 “Odala ndi amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo+ ndipo machimo awo aphimbidwa.+
8 Wodala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.”+
9 Chotero, kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala odala choncho? Kapena kodi osadulidwa nawonso amakhala odala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa ngati wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+
10 Koma kodi iye anali wotani pamene anayesedwa wotero? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa?+ Sanali wodulidwa, koma wosadulidwa.
11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe monga chizindikiro.+ Chizindikiro chimenechi chinali chosonyeza kuti, chifukwa cha chikhulupiriro, Mulungu anamuyesa wolungama asanadulidwe, kuti adzakhale tate+ wa onse osadulidwa okhala ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama.
12 Kutinso adzakhale tate wa ana odulidwa, osati wa okhawo ochita mdulidwe, komanso wa amene amayenda moyenerera m’mapazi a chikhulupiriro chimene bambo wathu+ Abulahamu anali nacho asanadulidwe.
13 Pakuti Abulahamu kapena mbewu yake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti anali wolungama mwa chikhulupiriro.+
14 Chifukwa ngati anthu oumirira kusunga chilamulo ndiwo adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa.+
15 Kwenikweni, Chilamulo chimabala mkwiyo,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+
16 Chotero iye anapatsidwa lonjezolo+ chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale mwa kukoma mtima kwakukulu,+ ndiponso kuti likhale lotsimikizika kwa mbewu yake yonse,+ osati yotsatira Chilamulo yokha ayi, komanso yotsatira chikhulupiriro cha Abulahamu. (Iye ndiye tate+ wa ife tonse,
17 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Ndakuika kuti ukhale tate wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Uyo amene Abulahamu anam’khulupirira, inde pamaso pa Mulungu, amene amapereka moyo kwa akufa+ ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.+
18 Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro+ chakuti adzakhala tate wa mitundu yambiri,+ ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+
19 Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, anaganizira za thupi lake, limene linali lakufa tsopano,+ popeza anali ndi zaka pafupifupi 100.+ Anaganiziranso zakuti Sara anali wosabereka.+
20 Koma chifukwa cha lonjezo+ la Mulungu, iye sanagwedezeke pa chikhulupiriro chake+ ndipo chikhulupiriro chakecho chinamulimbitsa.+ Mwa kutero, anapereka ulemerero kwa Mulungu
21 ndipo anali wotsimikiza kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+
22 Ndiye chifukwa chake “anaonedwa ngati wolungama.”+
23 Komabe, zonena kuti “anayesedwa+ wolungama” sizinalembedwere iye yekha,+
24 komanso ife amene tidzayesedwa otero, chifukwa chakuti timakhulupirira iye amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu kwa akufa.+
25 Iye anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tiyesedwe olungama.+