Aroma 14:1-23
14 Landirani munthu wokhala ndi zofooka m’chikhulupiriro+ chake, koma osagamula pa zoganiza za mumtima mwake.+
2 Wina ali ndi chikhulupiriro chakuti angadye china chilichonse,+ koma munthu wofooka amadya zamasamba.
3 Amene amadya, asanyoze amene sadya,+ ndipo wosadyayo asaweruze amene amadya, popeza ameneyo analandiridwa ndi Mulungu.
4 Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wapakhomo wa mnzako?+ Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa.+ Komatu Yehova akhoza kumukomera mtima chifukwa angathe kumuthandiza.+
5 Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake,+ koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi masiku ena onse.+ Choncho munthu aliyense akhale wotsimikiza ndi mtima wonse m’maganizo mwake.
6 Amene amasunga tsiku amalisungira kulemekeza Yehova. Amene amadya, amadya kuti alemekeze Yehova,+ chifukwa amayamika Mulungu.+ Amene sadya, sadya pofuna kulemekeza Yehova,+ chifukwa nayenso amayamika Mulungu.+
7 Kunena zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha,+ ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha.
8 Pakuti tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova,*+ ndipo tikafa, timafera Yehova.+ Chotero kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.+
9 Ndiye chifukwa chake Khristu anafa n’kukhalanso ndi moyo,+ kuti akhale Ambuye wa akufa+ ndiponso wa amoyo.+
10 Nanga n’chifukwa chiyani umaweruza m’bale wako?+ Kapenanso n’chifukwa chiyani umanyoza m’bale wako? Pakuti tonse tidzaimirira patsogolo pa mpando woweruzira milandu+ wa Mulungu.
11 Malembatu amati: “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova,+ ‘bondo lililonse lidzandigwadira ine, ndipo lilime lililonse lidzavomereza poyera kwa Mulungu.’”+
12 Chotero aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.+
13 Pa chifukwa chimenechi, tisamaweruzane,+ koma m’malomwake tsimikizani mtima+ kuti simuikira m’bale wanu+ chokhumudwitsa+ kapena chopunthwitsa.
14 Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chodetsedwa mwa icho chokha.+ Koma ngati munthu akuona chinachake monga chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa.+
15 Chifukwa ngati m’bale wako akuvutika maganizo chifukwa cha chakudya, ndiye kuti simukuyendanso m’chikondi.+ Musawononge* munthu amene Khristu anamufera+ chifukwa cha zakudya zanu.
16 Choncho musalole kuti anthu akunenereni zoipa pa zabwino zimene mukuchita.
17 Pakuti ufumu wa Mulungu+ si kudya ndi kumwa ayi,+ koma chilungamo,+ mtendere+ ndi chimwemwe+ zobwera ndi mzimu woyera.
18 Chifukwa aliyense wotumikira Khristu motere ali wovomerezeka kwa Mulungu ndipo anthu amakondwera naye.+
19 Choncho, tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere+ ndiponso zolimbikitsana.+
20 Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi.+ Zoonadi, zinthu zonse ndi zoyera, koma munthu amene amadya ngakhale pamene akukhumudwitsa ena, amalakwa.+
21 Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.+
22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, khala nacho pakati pa iweyo ndi Mulungu.+ Wodala munthu amene sakudziika pa chiweruzo ndi zinthu zimene wasankha kuchita.
23 Koma ngati akudya ndipo akukayikira, ameneyo watsutsidwa kale,+ chifukwa sakudya mwa chikhulupiriro. Ndithu, chilichonse chochitidwa mosemphana ndi chikhulupiriro ndi tchimo.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 2.
^ Kutanthauza kuwononga chikhulupiriro kapena chiyembekezo cha moyo wosatha wa m’tsogolo.