Cibvumbulutso Coonetsedwa kwa Yohane 21:1-27

  • Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano (1-8)

    • Imfa sidzakhalaponso (4)

    • Zinthu zonse zipangidwa kukhala zatsopano (5)

  • Yerusalemu watsopano afotokozedwa (9-27)

21  Ndiyeno ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, cifukwa kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitacoka, ndipo kunalibenso nyanja. 2  Ndinaonanso mzinda woyela, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kumwamba kwa Mulungu, wokonzedwa ngati mkwatibwi amene wabvala zokongola kuti akalandile mwamuna wake. 3  Kenako ndinamva mau opfuula kucokela kumpando wacifumu akuti: “Taonani! Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu, ndipo adzakhala nao. Iwo adzakhala anthu ake, ndipo Mulunguyo adzakhala nao. 4  Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo sipadzakhalanso imfa, kulila cifukwa ca malilo, kubuula, kapena zopweteka. Zakalezo zapita.” 5  Ndipo wokhala pampando wacifumu uja anati: “Taonani! Ndikupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.” Ananenanso kuti: “Lemba, cifukwa mau amenewa ndi odalilika komanso oona.” 6  Ndiyeno anandiuza kuti: “Zakwanilitsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega,* ciyambi ndi mapeto. Aliyense amene akumva ludzu ndidzam’patsa madzi a pakasupe wa moyo kwaulele. 7  Aliyense amene wapambana adzalandila zinthu zimenezi kuti zikhale colowa cake. Ine ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. 8  Koma anthu amantha, opanda cikhulupililo, onyansa ndi ubve wao, opha anthu, aciwelewele,* ocita zamizimu, olambila mafano, ndi anthu onse abodza, adzaponyedwa mʼnyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimila imfa yaciwili.” 9  Mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi milili 7 yotsiliza, anabwela n’kundiuza kuti: “Bwela ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” 10  Conco ananditenga posewenzetsa mphamvu ya mzimu kundipititsa ku phili lalikulu ndi lalitali, ndipo anandionetsa mzinda woyela wa Yerusalemu, ukutsika kumwamba kwa Mulungu, 11  ndipo unali ndi ulemelelo wa Mulungu. Unali kunyezimila ngati mwala wamtengo wapatali kwambili, ngati mwala wa yasipi wowala mbee ngati galasi. 12  Mzindawo unali ndi mpanda waukulu komanso wautali, ndipo unali ndi mageti 12. Pamagetiwo panali angelo 12, ndipo panalembedwa maina a mapfuko 12 a ana a Isiraeli. 13  Kum’mawa kwa mzindawo kunali mageti atatu, kumpoto mageti atatu, kum’mwela mageti atatu, komanso kumadzulo kwake kunali mageti atatu. 14  Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala 12 ya maziko. Ndipo pamiyalayo panalembedwa maina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa. 15  Ndiyeno uja amene anali kulankhula ndi ine, ananyamula bango lagolide lopimila, kuti apime mzindawo, mageti ake, ndi mpanda wake. 16  Mzindawo unali ndi mbali zinai zofanana m’litali ndi m’lifupi mwake. Mngelo uja anapima mzindawo ndi bango, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulila. M’litali mwake, m’lifupi mwake, komanso kucoka pansi kupita m’mwamba ndi zofanana. 17  Anapimanso mpanda wake, ndipo linali lalitali mikono 144,* malinga ndi mpimo wa munthu, umenenso ndi mpimo wa mngelo. 18  Mpandawo anaumanga ndi miyala ya yasipi, ndipo mzindawo anaumanga ndi golide woyenga bwino woonekela ngati galasi. 19  Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yosiyana-siyana: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, aciwili wa safiro, acitatu wa kalikedo, acinai wa emarodi, 20  acisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12 wa ametusito. 21  Komanso zitseko za mageti 12 aja zinali ngale 12. Citseko ciliconse anacipanga ndi ngale imodzi. Ndipo mseu waukulu wa mumzindawo anaupanga ndi golide woyenga bwino woonekela ngati galasi. 22  Mumzindawo sindinaonemo kacisi aliyense, cifukwa kacisi wake ndi Yehova* Mulungu Wamphamvuzonse komanso Mwanawankhosa. 23  Mzindawo sufunikilanso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, cifukwa kuwala kwa ulemelelo wa Mulungu kumaunikila mzindawo, ndipo Mwanawankhosa ndiye nyale yake. 24  Mitundu ya anthu idzayenda mu kuwalako, ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweletsa ulemelelo wao mu mzindawo. 25  Mageti ake sadzawatseka masana m’pang’ono pomwe, pakuti usiku sudzakhalapo. 26  Iwo adzabweletsa ulemelelo ndi ulemu wa mitundu ya anthu mu mzindawo. 27  Koma ciliconse codetsedwa, ndi aliyense wocita zonyansa komanso zacinyengo, sadzalowa mumzindawo. Amene adzalowamo ndi okhawo amene maina ao analembedwa mu mpukutu wa moyo wa Mwanawankhosa.

Mau a m'Munsi

Kapena kuti, “ndine A ndi Z.” Alefa ndi cilembo coyambilila ca alifabeti ya Cigiriki ndipo Omega ndi cilembo comalizila.
Pafupifupi makilomita 2,220. Sitadiya imodzi ndi yofanana ndi mamita 185. Onani Zakumapeto B14.
Mamita pafupifupi 64. Onani Zakumapeto B14.