Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Anadziwiratu Kuti Adamu ndi Hava Adzachimwa?

Kodi Mulungu Anadziwiratu Kuti Adamu ndi Hava Adzachimwa?

Kodi Mulungu Anadziwiratu Kuti Adamu ndi Hava Adzachimwa?

ANTHU ambiri amafunitsitsa atadziwa yankho la funso limeneli. Anthu akangoyamba kukambirana zimene zinachititsa kuti Mulungu alole kuti zoipa zizichitika, nthawi zambiri chimene chimabwera m’maganizo mwawo ndi nkhani yokhudza uchimo wa mwamuna ndi mkazi oyambirira m’munda wa Edeni. Mfundo yakuti ‘Mulungu amadziwa zinthu zonse’ imachititsa ena kuganiza kuti Mulungu anadziwiratu kuti Adamu ndi Hava sadzamumvera.

Zitakhala zoona kuti Mulungu anadziwiratu kuti Adamu ndi Hava adzachimwa, kodi zimenezi zingasonyeze chiyani? Mwachionekere zingasonyeze kuti Mulungu ndi woipa kwambiri. Zingasonyeze kuti iye ndi wopanda chikondi, chilungamo ndiponso sachita zinthu moona mtima. Anthu ena angaone kuti inali nkhanza kuikira anthu oyambirirawo chinthu chimene Mulunguyo anadziwiratu kuti chidzayambitsa mavuto ambiri. Zikanakhala kuti Mulungu anachitadi zimenezi zingaoneke kuti iye ndi amene anayambitsa zinthu zoipa kapena ndiye amathandizira kuti zinthu zoipa zizichitika. Kuwonjezera pamenepa, zimenezi zingachititse ena kuona Mlengi wathu ngati wopusa.

Koma kodi Malemba amasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi makhalidwe oipa? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione zimene Baibulo limanena zokhudza zinthu zimene Yehova analenga ndiponso makhalidwe ake.

“Zinali Zabwino Kwambiri”

Ponena za zinthu zimene Mulungu analenga kuphatikizapo anthu awiri oyambirira, nkhani ya m’buku la Genesis imati: “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:31) Adamu ndi Hava analengedwa angwiro oyenereradi malo amene ankakhala padziko lapansili. Iwo analengedwa ndi chilichonse chofunika kuti akhale ndi moyo wabwino. Popeza kuti anawalenga ‘bwino kwambiri,’ iwo akanatha kusonyeza khalidwe labwino limene Mulungu ankafuna. Komanso iwo analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Choncho akanatha kusonyeza makhalidwe amene anatengera kwa Mulungu monga nzeru, chikondi chosatha, chilungamo ndi ubwino. Makhalidwe amenewa akanawathandiza kusankha bwino zinthu ndiponso akanachititsa kuti Atate wawo wakumwamba asangalale.

Yehova analenga Adamu ndi Hava ali angwiro ndiponso anzeru. Choncho anawapatsa ufulu wosankha zochita. Iye sanawalenge ngati maloboti amene amangoyaka pa nthawi imene anawatchera kuti aziyaka. Komanso taganizirani izi: Kodi ndi mphatso iti imene ingakusangalatseni kwambiri, yongokupatsani chifukwa chakuti munthu walamulidwa kuti akupatseni, kapena yokupatsani chifukwa chakuti amakukondani? Pamenepa yankho ndi lodziwikiratu. Mofanana ndi zimenezi, ngati Adamu ndi Hava akanasankha kumvera Mulungu chifukwa chomukonda, Mulunguyo akanasangalala kwambiri. Popeza anthu oyamba amenewa anali ndi ufulu wosankha, akanatha kumvera Yehova chifukwa chomukonda.​—Deuteronomo 30:19, 20.

Mulungu ndi Wolungama, Wabwino Ndiponso Amaweruza Mosakondera

Baibulo limatiuza makhalidwe abwino amene Yehova ali nawo. Chifukwa chakuti ali ndi makhalidwe amenewo, iye sangachite tchimo lililonse. Lemba la Salimo 33:5 limati, Yehova “amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.” Ndiye chifukwa chake lemba la Yakobo 1:13 limati: “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Chifukwa chakuti Mulungu ndi wabwino ndiponso ankamukonda Adamu, anamuchenjeza kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Adamu ndi Hava anapatsidwa ufulu wosankha moyo wosatha kapena imfa. Kodi sichikanakhala chinyengo ngati Mulungu akanawachenjezeratu za kuipa kwa kudya chipatso choletsedwa koma akudziwa kuti iwo adzadyabe chipatsocho zivute zitani? Popeza Yehova “amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera,” iye sakanawapatsa ufulu wosankha kumumvera pamene akudziwa kuti iwo sangathe kuchita zimenezo.

Komanso Yehova ndi wabwino kwambiri. (Salimo 31:19) Ponena za ubwino wa Mulungu, Yesu anati: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? (Mateyu 7:9-11) Mulungu amapatsa zolengedwa zake “zinthu zabwino.” Mmene Mulungu analengera anthu ndiponso mmene anakonzera Paradaiso, ndi umboni wakuti iye ndi wabwino. Kodi Wolamulira wabwino ngati ameneyu angachite nkhanza pokonza malo okongola kwambiri oti anthu akhalemo akudziwa kuti awalandanso malo amenewo? Ayi. Mlengi wathu ndi wolungama komanso wabwino, ndipo si amene anachititsa anthu kupanduka.

“Wanzeru Yekhayo”

Malemba amasonyezanso kuti Yehova ndi “wanzeru yekhayo.” (Aroma 16:27) Angelo a Mulungu anaona zinthu zambiri zimene iye anachita zosonyeza kuti alidi ndi nzeru zopanda malire. Yehova atalenga zinthu zapadziko lapansi, iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:4-7) Ndi zosakayikitsa kuti angelo amenewa ankaonetsetsa mwachidwi zonse zimene zinkachitika m’munda wa Edeni. Angelo anaona Mulungu akulenga kumwamba ndiponso zinthu zochititsa chidwi kwambiri za padziko lapansi. Ndiye kodi zikanakhala zomveka kwa iwo kuona kuti kenako Mulungu wanzeru ameneyu, akulenganso anthu awiri koma akudziwiratu kuti anthuwo sapita patali? N’zoonekeratu kuti zimenezi zikanakhala zosamveka.

Komabe mwina wina anganene kuti, ‘Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu, yemwe ndi wanzeru zonse, asadziwiretu za m’tsogolo?’ N’zoonadi kuti Yehova ali ndi nzeru zazikulu ndipo amatha kudziwa “za mapeto kuyambira pa chiyambi.” (Yesaya 46:9, 10) Koma iye sakakamizika kugwiritsa ntchito nzeru zake zonse zodziwiratu zinthu monga mmene zilili kuti kawirikawiri sagwiritsira ntchito mphamvu zake zonse pochita zinthu. Yehova amasankha mwanzeru zinthu zimene akufuna kuzidziwiratu. Ndipo amachita zimenezo akaona kuti ndi pofunikira komanso ngati zikugwirizana ndi mmene zinthu zili pa nthawiyo.

Zimene Mulungu amachita potha kusankha kudziwiratu za m’tsogolo, tingaziyerekezere ndi zimene munthu angachite poonera DVD. Munthu amene akuonera mpira pa DVD angasankhe kuonera kaye mbali yomalizira ya mpirawo kuti adziwe mmene unathera asanaonere mpira wonse. Komabe ndiye kuti iye wangosankha kuchita zimenezi chifukwa akanathanso kuonera mpirawo kuyambira koyambirira. Ndipotu palibe amene angamuimbe mlandu kuti wasankhiranji kuonera mpirawo kuyambira koyambirira. N’chimodzimodzinso ndi zimene Mlengi anachita. Iye anasankha kusadziwiratu zimene anthu awiriwo achite. M’malo mwake, anasankha kudikira kaye kuti aone zimene zichitike ndiponso mmene ana ake apadziko lapansiwo achitire zinthu.

Monga tanena kale, Yehova malinga ndi nzeru zake, sanalenge anthu oyambirira aja ngati maloboti kuti azingochita zinthu zimene iye akufuna basi, popanda kusankha okha. Koma iye mwachikondi anawapatsa ufulu wosankha. Ngati iwo akanasankha njira yabwino akanasonyeza kuti amakonda Mulungu, amamuyamikira komanso amamumvera. Zimenezi zikanawathandiza kukhala osangalala kwambiri komanso zikanasangalatsa Yehova, Atate wawo wakumwamba.​—Miyambo 27:11; Yesaya 48:18.

Malemba amasonyeza kuti m’zochitika zambiri, Mulungu anasankha kusagwiritsa ntchito luso lake lodziwiratu zinthu. Mwachitsanzo, pamene munthu wokhulupirika Abulahamu anatsala pang’ono kupereka nsembe mwana wake, Yehova ananena kuti: “Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.” (Genesis 22:12) Komanso nthawi zina khalidwe loipa la anthu ena ‘linali kumukhumudwitsa’ kwambiri. Kodi Yehova akanakhumudwa choncho zikanakhala kuti anadziwiratu kalekale kuti anthuwo adzachita zinthu zomukhumudwitsa?​—Salimo 78:40, 41; 1 Mafumu 11:9, 10.

Choncho n’zomveka kunena kuti Mulungu wanzeru zonse sanagwiritse ntchito mphamvu zake zotha kudziwiratu zinthu kuti adziwiretu za kuchimwa kwa makolo athu oyamba. Iye si wopusa kuti alenge anthu akudziwiratu kuti anthuwo adzakumana ndi zovuta.

“Mulungu Ndiye Chikondi”

Satana, amene ndi mdani wa Mulungu, ndi amene anachititsa kuti anthu apandukire Mulungu m’munda wa Edeni. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ayambe kukumana ndi mavuto ambirimbiri kuphatikizapo uchimo ndi imfa. N’chifukwa chake Satana ndi “wopha anthu.” Iye wasonyezanso kuti ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Popeza kuti Satana ali ndi zolinga zoipa, amayesetsa kuchititsa anthu kuti aziona ngati Mlengi wathu ndi woipa. Cholinga chake ndi choti Yehova aoneke ngati ndi amene anachititsa kuti anthu achimwe.

Chikondi ndi chimene chinachititsa kwambiri Yehova kusankha kusadziwiratu kuti Adamu ndi Hava adzachimwa. Chikondi ndiye khalidwe lalikulu la Mulungu. Lemba la 1 Yohane 4:8 limati: “Mulungu ndiye chikondi.” Chikondi chimachititsa munthu kuchita zinthu zabwino osati zoipa. Chimachititsa munthu kuti azifuna kuti anthu ena zinthu ziwayendere bwino. Choncho Yehova Mulungu ankafunira anthu oyambirira aja zabwino chifukwa ankawakonda.

Ana a Mulungu a padziko lapansiwa anali ndi ufulu wosankha. Koma ngakhale zinali choncho, Mulungu wathu wachikondi sankakayikira ana ake angwiro amenewa kapena kumangoyembekezera kuti iwo asankha zoipa basi. Iye anawapatsa chilichonse chimene anafunika pamoyo wawo ndipo sanawabisire kanthu. M’pake kuti Mulungu ankayembekezera kuti iwo amumvera mwachikondi osati kumupandukira. Iye ankadziwa kuti Adamu ndi Hava akanatha kukhala okhulupirika ngati mmene anthu ena opanda ungwiro pambuyo pake anachitira. Ena mwa anthuwa ndi Abulahamu, Yobu ndi Danieli.

Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mateyu 19:26) Zimenezi ndi zolimbikitsa kwambiri. Chikondi cha Yehova komanso makhalidwe ake ena akuluakulu monga chilungamo, nzeru ndiponso mphamvu ndi umboni wakuti pa nthawi yake iye adzachotsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha uchimo ndiponso imfa.​—Chivumbulutso 21:3-5.

Ndiyetu apa ndi zoonekeratu kuti Yehova sanadziwiretu kuti Adamu ndi Hava adzachimwa. Kusamvera kwawo komanso zotsatira zake zoipa zinamukhumudwitsa kwambiri. Komabe iye anadziwa kuti zimenezi sizilepheretsa cholinga chake chokhudza dziko lapansili ndi anthu. Tikukupemphani kuti mudziwe zambiri za cholinga chimenechi komanso zimene mungachite kuti mudzasangalale cholinga chimenechi chikadzakwaniritsidwa. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 23 Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi, werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Yehova sanalenge anthu awiri oyambirira ngati maloboti kuti azingochita zinthu zimene iye akufuna basi, popanda kusankha okha

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Mulungu ankadziwa kuti Adamu ndi Hava akanatha kukhala okhulupirika