Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

 Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?

KODI nkhani ya Adamu ndi Hava, omwe ankakhala m’munda wa Edeni, mumaidziwa? Nkhani imeneyi ndi yodziwika kwa anthu ambiri padziko lonse lapansi. Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani imeneyi. Nkhaniyi imapezeka pa Genesis 1:26–3:24. Mwachidule, nkhaniyi imanena kuti:

Yehova Mulungu * anapanga munthu pogwiritsa ntchito fumbi lapansi ndipo anam’patsa dzina lakuti Adamu. Mulungu anaika munthuyu m’munda umene unali m’dera lina lotchedwa Edeni. Mulungu ndi amene anapanga munda umenewu. Unali ndi madzi okwanira ndipo munali mitengo yobiriwira ndiponso ya zipatso zambiri zokoma. Pakati pamundawu panali “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Mulungu analetsa anthu kudya zipatso za mtengo umenewu ndipo anawauza kuti adzafa ngati sadzamvera zimenezi. Patapita nthawi, Yehova anagwiritsa ntchito nthiti ya Adamu n’kumupangira mnzake. Ameneyu anali mkazi ndipo dzina lake anali Hava. Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava ntchito yoti azisamalira munda wa Edeni ndipo anawauzanso kuti aberekane achuluke adzaze dziko lapansi.

Tsiku lina Hava ali yekha, njoka inamuuza kuti adye zipatso za mtengo umene Mulungu anawaletsa. Inachita zimenezi pomuuza kuti Mulungu anamunamiza ndipo anamubisira zinthu zabwino zimene zikanachititsa  kuti afanane ndi Mulungu. Iye anakopeka n’kudya chipatso choletsedwa chija. Adamu nayenso anagwirizana naye posonyeza kusamvera Mulungu ndipo anadya chipatsocho. Zitatero, Yehova anaweruza Adamu, Hava ndiponso njoka. Kenako anthuwo anathamangitsidwa m’munda wa Edeni ndipo Mulungu anaika angelo kuti azilondera mundawo n’cholinga chakuti anthuwo asabwererenso.

Kale, akatswiri ena amaphunziro ndiponso a mbiri yakale ankavomereza kuti zochitika zotchulidwa m’buku la m’Baibulo la Genesis zinachitikadi. Koma masiku ano pali anthu ambiri amene amatsutsa kuti zimenezi zinachitikadi. Kodi n’chiyani chimachititsa anthuwa kutsutsa kuti nkhani ya m’buku la Genesis yonena za Adamu, Hava ndiponso munda wa Edeni inachitikadi? Tiyeni tikambirane mfundo zinayi zimene otsutsa amanena.

1. Sikunakhalepo munda wa Edeni.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu amakayikira mfundo imeneyi? N’kutheka kuti amatengera zimene akatswiri ena amanena. Kwa zaka zambiri, akatswiri a maphunziro a zaumulungu ankanena kuti munda wa Mulungu umenewu unali udakalipo kwinakwake. Koma iwo ankanena zimenezi chifukwa chotengera nzeru za akatswiri achigiriki monga Plato ndi Aristotle, amene ankaphunzitsa kuti padziko lapansi pano sipangakhale chilichonse changwiro, kapena kuti chopanda vuto lililonse. Iwo ankanena kuti zinthu zoterozo zimangopezeka kumwamba kokha. Pomva zimenezi, akatswiri a maphunziro a zaumulungu anayamba kuganiza kuti ndiye kuti Paradaiso woyambirirayo anali kumwamba. * Ena ankanena kuti munda umenewo unali pamwamba paphiri lalitali kwambiri, zomwe zinachititsa kuti mundawo usakhudzidwe ndi zoipa zimene zimachitika padziko lapansi. Masiku ano akatswiri ena amanena kuti munda umenewu uli kumpoto kapena kum’mwera kwa malekezero a dziko lapansi ndipo ena amanena kuti uli pamwezi kapena pamalo ena pafupi ndi mwezi. Chifukwa cha mfundo ngati zimenezi, anthu anayamba kuona kuti nkhani ya munda wa Edeni ndi nthano chabe yongofuna kusangalatsa anthu. Akatswiri ena amaphunziro masiku ano amatsutsa zimene Baibulo limanena zokhudza kumene kunali munda wa Edeni ndipo amati kunalibe malo ngati amenewo.

Komano Baibulo likamanena za munda wa Edeni silinena mfundo ngati zimenezo. Lemba la Genesis 2:8-14 limatiuza zinthu zingapo zomveka bwino zokhudza munda umenewu. Limatiuza kuti mundawu unali chakum’mawa kwa dera lotchedwa Edeni. M’munda umenewu munadutsa mtsinje wina umene kutsogolo kwake unagawikana n’kukhala mitsinje inayi. Baibulo limatchula mayina a mitsinje inayi yonseyi ndipo limafotokozanso mwachidule kumene mtsinje uliwonse unalowera. Kwa nthawi yaitali, akatswiri ena akhala akuchita chidwi kwambiri ndi mfundo zimenezi ndipo ambiri a iwo akhala akufufuza mwakhama nkhani ya m’Baibulo imeneyi kuti mwina ingawathandize kupeza malo enieni kumene kunali munda wa Edeni. Komabe zimene apeza zachititsa kuti akhale ndi maganizo osiyanasiyana komanso otsutsana pa nkhaniyi. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nkhani zokhudza dera lotchedwa Edeni komanso munda wokongola ndiponso mitsinje imene inali m’derali ndi zabodza, mwinanso nthano chabe?

Taganizirani izi: Nkhani za m’munda wa Edeni zinachitika zaka zoposa 6,000 zapitazo. Mose ndi amene analemba zochitika zimenezi ndipo mwina anauzidwa zimenezi ndi anthu ena kapena anagwiritsa ntchito zolembedwa zimene zinalipo kale. Koma Mose analemba nkhanizi patapita zaka pafupifupi 2,500 kuchokera pamene zinachitika. Choncho pa nthawiyo imene Mose ankalemba zimenezi, munda wa Edeni unali kale mbiri yakale. N’kutheka kuti panopa,  popeza patha zaka zambirimbiri, zinthu zothandiza anthu kuzindikira malo, monga mitsinje, zimene zinatchulidwa m’nkhaniyi zinasintha. Tikutero chifukwa nthaka ya dziko lapansili imayendayenda. Ndiponso kudera kumene kukuoneka kuti kunali Edeni kumachitika zivomezi kawirikawiri, moti zina mwa zivomezi zazikulu kwambiri zimene zachitikapo padziko lonse lapansi zinachitika m’dera limeneli. M’madera oterewa, zinthu zachilengedwe zimasintha nthawi zonse. Kuwonjezera pamenepa, Chigumula cha Nowa chiyenera kuti chinasinthiratu mmene derali linkaonekera moti sitingathenso kudziwa kuti poyamba linkaoneka bwanji. *

Komabe pali mfundo zowerengeka zimene tikudziwa. Mwachitsanzo, nkhani ya m’buku la Genesis imasonyeza kuti munda wa Edeni unalidi malo enieni. Mtsinje wa Firate ndi wa Tigirisi kapena kuti Hidekeli, yomwe ndi iwiri mwa mitsinje inayi imene imatchulidwa m’nkhaniyi, ilipobe mpaka pano ndipo mitsinjeyi inayambira pamalo oyandikana. Nkhaniyi imatchula madera amene mitsinje imeneyi inadutsa ndipo imatchulanso zinthu zachilengedwe zimene ndi zodziwika kwambiri m’madera amenewa. Anthu a ku Isiraeli ndi amene anali oyambirira kuwerenga nkhani imeneyi ndipo mfundo zimenezi zinawathandiza kudziwa zambiri.

Ndiyeno kodi nthano komanso nkhani zopeka zimafotokozedwa chonchi? Ayi. Kawirikawiri, nkhani zoterozo sizitchula mwachindunji zinthu zimene aliyense angafufuze n’kupeza umboni wake mosavuta. Nthawi zambiri zimayamba ndi mawu akuti: “Panangokhala.” Koma nkhani zonena za zinthu zimene zinachitikadi zimakhala ndi mfundo zonse zofunikira kuti munthu amvetse bwino nkhaniyo ngati mmene nkhani yonena za munda wa Edeni ilili.

2. Sizoona kuti Mulungu anapanga Adamu kuchokera ku fumbi ndiponso Hava kuchokera ku nthiti ya Adamu.

Masiku ano asayansi apeza umboni wosonyeza kuti thupi la munthu linapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana monga hayidirojeni, okosijeni ndi kaboni, zimene zimapezekanso munthaka. Koma kodi zinatheka bwanji kuti apange chinthu chamoyo kuchokera ku zinthu zimenezi?

Asayansi ambiri amanena kuti zinthu zamoyo zinakhalapo zokha. Iwo amati poyamba kunali tamoyo tating’ono kwambiri tokhala ndi thupi lopanda zinthu zambiri ndiponso losacholowana. Ndiyeno amati tamoyo timeneti tinkasintha pang’onopang’ono pa zaka mamiliyoni ambiri n’kukhala ndi matupi ocholowana kwambiri. Koma si zoona kuti pangakhale chamoyo cha “thupi lopanda zinthu zambiri ndiponso losacholowana” chifukwa chakuti zamoyo zonse, kuphatikizapo tizilombo tating’ono kwambiri tosaoneka ndi maso, tokhala ndi selo imodzi yokha, tili ndi thupi locholowana kwambiri lovuta kumvetsa. Palibe umboni wosonyeza kuti pali chamoyo chilichonse chimene chinalakhapo chokha. Ndiponso palibe umboni wosonyeza kuti zimenezi zingachitike. M’malo mwake, zolengedwa  zonse zimasonyeza umboni wosatsutsika wakuti zinachita kulengedwa ndi winawake wanzeru kwambiri kuposa anthufe. *​—Aroma 1:20.

Tiyerekeze kuti mukumvetsera nyimbo inayake yoimbidwa mwaluso kwambiri kapena mukuyang’ana chithunzi chojambulidwa bwino zedi kapenanso mukuchita chidwi ndi makina ena ochita zinthu modabwitsa. Kodi munganene kuti zinthu zimenezi zinangokhalapo zokha? N’zodziwikiratu kuti simunganene zimenezi. Ngakhale zili choncho, zinthu zopangidwa mwaluso zimenezi sitingaziyerekezere n’komwe ndi thupi la munthu limene linapangidwa mogometsa komanso mokongola kwambiri. Ndiyeno kodi n’zomveka kunena kuti palibe Mlengi amene anapanga munthu? Ndipotu nkhani ya m’buku la Genesis imanena kuti pa zamoyo zonse zimene zili padziko lapansili, ndi anthu okha amene analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26) N’chifukwa chake anthu okha ndi amene amatha kusonyezako luso lopanga zinthu limene Mulungu ali nalo, moti nthawi zina amatha kuyimba nyimbo mwaluso kwambiri, kujambula zithunzi zokongola komanso kupanga makina odabwitsa. Choncho kodi ziyenera kutidabwitsa kuti Mulungu anapanga zinthu mwaluso kwambiri kuposa mmene anthufe tingapangire?

Ndipo tikanena zolenga mkazi pogwiritsa ntchito nthiti ya mwamuna, kwa Mulungu imeneyo sinkhani. * Mulungu akanatha kugwiritsa ntchito njira ina, koma kulenga mkazi pogwiritsa ntchito nthiti ya mwamuna kunali ndi tanthauzo lalikulu. Iye anafuna kuti mwamuna ndi mkaziyo akwatirane ndi kumakondana kwambiri monga “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mwamuna ndi mkazi angathe kuthandizana pa zinthu zambiri, kupanga ubwenzi wolimba ndiponso wosatha. Kodi umenewu si umboni wakuti kuli Mlengi wanzeru komanso wachikondi?

Komanso akatswiri ena ofufuza za maselo a m’thupi amavomereza kuti anthu onse anachokera kwa mwamuna ndi mkazi mmodzi. Ndiyeno kodi zimenezi sizikugwirizana ndi zimene buku la Genesis limanena?

3. Nkhani ya mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa imamveka ngati yopeka.

Nkhani ya m’buku la Genesis siinena kuti mitengo imeneyi inali ndi mphamvu zapadera. Koma inali mitengo ngati mmene mtengo uliwonse umakhalira kungoti inkaimira zinazake.

Anthunso amachita zofanana ndi zimenezi nthawi zina. Mwachitsanzo poweruza mlandu, woweruza angachenjeze anthu kuti azilemekeza khothi chifukwa kupanda kutero ndiye kuti akuphwanya lamulo. Pamenepo sikuti akutanthauza kuti munthu ayenera kulemekeza mipando, matebulo ndi zipupa za khotilo ayi. Koma akutanthauza anthu amene ali ndi ulamuliro m’khotimo. Mafumu enanso amakhala ndi litchowa, ndodo, kapena chisoti chachifumu monga chizindikiro cha ulamuliro wawo.

 Ndiye kodi mitengo iwiri ija inkaimira chiyani? Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana ovuta kumva pa nkhani imeneyi. Koma yankho la funso limeneli ndi losavuta kumva ndipo lili ndi tanthauzo lalikulu kwambiri. Mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa unkaimira udindo umene Mulungu yekha ndi amene ali nawo, wotha kudziwa chabwino ndi choipa. (Yeremiya 10:23) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti kuba zipatso za mtengo umenewu kunali kuswa lamulo. Mtengo wa moyo unkaimira mphatso ya moyo wosatha yomwe Mulungu yekha ndi amene angaipereke.​—Aroma 6:23.

4. Ena amaona kuti nkhaniyi ndi yopeka chifukwa njoka singalankhule.

Kunena zoona nkhani ya m’buku la Genesis imeneyi ingakhale yovuta kuimvetsa makamaka ngati munthu sakuganizira mfundo zinanso za m’Baibulo. Komabe Malemba amatithandiza kumvetsa nkhani yovuta koma yochititsa chidwi imeneyi.

Kodi ndani anachititsa kuti njoka ija izioneka ngati ikulankhula? Anthu a ku Isiraeli wakale ankadziwa mfundo zina zimene zinawathandiza kumvetsa chimene chinachitika kuti njokayo ilankhule. Mwachitsanzo, iwo ankadziwa kuti ngakhale kuti nyama sizilankhula, mngelo angathe kuchititsa kuti nyama izioneka ngati ikulankhula. Mose analembanso nkhani ya Balamu yonena kuti Mulungu anatumiza mngelo kuti achititse bulu wa Balamu kulankhula ngati munthu.​—Numeri 22:26-31; 2 Petulo 2:15, 16.

Kodi angelo ena omwe ndi adani a Mulungu angachite zozizwitsa? Inde chifukwa Mose anaonapo ansembe amatsenga a ku Iguputo akutsanzira zina mwa zozizwitsa za Mulungu monga kusandutsa ndodo kuti izioneka ngati njoka. N’zoonekeratu kuti angelo opanduka, amene ndi adani a Mulungu, ndi amene anachititsa kuti amatsengawo achite zimenezi.​—Ekisodo 7:8-12.

Zikuoneka kuti Mose ndi amenenso anauziridwa kulemba buku la m’Baibulo la Yobu. Buku limeneli limanenanso zambiri za Satana yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu. Iye anatsutsa zoti atumiki onse a Yehova angakhaledi okhulupirika kwa iye zivute zitani. (Yobu 1:6-11; 2:4, 5) N’kutheka kuti chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli anadziwa kuti Satana ndi amene anachititsa kuti njoka ya m’munda wa Edeni izioneka ngati ikulankhula, n’kunyenga Hava kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu.

Koma kodi Satana ndi amenedi analankhula kudzera mwa njoka ija? Inde, chifukwa patapita nthawi, Yesu ananena kuti Satana ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Mwina mungavomereze kuti amene anayambirira kunena bodza ndiye akuyenera kukhala “tate wake wa bodza.” Bodza loyamba limapezeka m’mawu amene njoka inauza Hava. Njoka inatsutsa zimene Mulungu anachenjeza anthu kuti akadzadya zipatso za mtengo woletsedwa adzafa. Njokayo inati: “Kufa simudzafa ayi.” (Genesis 3:4) N’zodziwikiratu kuti Yesu ankadziwa kuti Satana ndi amene analankhulitsa njokayo. M’masomphenya amene Yesu anaonetsa mtumwi Yohane, Satana akutchulidwa kuti “njoka yakale ija” ndipo zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino nkhani ya m’munda wa Edeni.​—Chivumbulutso 1:1; 12:9.

Kodi ndi zovuta kukhulupirira kuti mzimu wamphamvu ungachititse njoka kulankhula ngati munthu? Ngakhale kuti anthu ndi ochepa mphamvu poyerekezera ndi mizimu, amatha kuchita zinthu zina zodabwitsa kwambiri monga kuchititsa zidole kuoneka ngati zikulankhula komanso kupanga zithunzi zooneka ngati zikuyenda.

 Umboni Wosatsutsika

Tsopano kodi simukuvomereza kuti anthu amene amatsutsa nkhani za m’buku la Genesis alibe zifukwa zenizeni zotsutsira? Ndipotu pali umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhani imeneyi inachitikadi.

Mwachitsanzo Yesu Khristu amatchedwa “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Popeza iye ndi wangwiro sananamepo kapena kupotoza nkhani inayake. Kuwonjezera pamenepo, iye anauza anthu kuti anali kumwamba kwa zaka zambirimbiri asanabwere padziko lapansi. Ndipotu iye ankakhala kumwambako ndi Atate wake, Yehova, “dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:5) Choncho analipo pamene zinthu zamoyo padziko lapansi zinayamba kulengedwa. Kodi Yesu ameneyu, yemwe ndi mboni yodalirika kuposa onse, anapereka umboni wotani wokhudza nkhani ya m’munda wa Edeni?

Yesu ananena za Adamu ndi Hava mosonyeza kuti anali anthu enieni. Iye anatchula za ukwati wawo pamene ankafotokoza zimene Yehova amafuna zoti mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi. (Mateyu 19:3-6) Zikanakhala kuti Adamu ndi Hava sanakhaleko ndipo nkhani yonena za munda wa Edeni, umene iwo ankakhalamo, ndi nthano chabe, ndiye kuti Yesu ananamizidwa kapena ananama. Koma Yesu sanganamizidwe ndiponso sanganame. Pamene nkhani imeneyi inkachitika m’munda wa Edeni, Yesu anali kumwamba ndipo ankaona zimene zinkachitikazo. Choncho palibe umboni wina wolondola kwambiri kuposa wa Yesu.

Kunena zoona kukayikira nkhani za m’buku la Genesis kumachititsanso kuti anthu asamakhulupirire Yesu. Komanso zimachititsa kuti anthu azilephera kukhulupirira malonjezo odalirika ndiponso nkhani zina zikuluzikulu za m’Baibulo. Tiyeni tione chifukwa chake tikutero.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 M’Baibulo dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 7 Mfundo imeneyi ndi yosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa chifukwa Baibulo limaphunzitsa kuti zonse zimene Mulungu analenga zinali zabwino. Limafotokozanso kuti pali wina amene anayambitsa zoipa. (Deuteronomo 32:4, 5) Yehova atamaliza kulenga zinthu padziko lapansi ananena kuti zonse zimene analengazo “zinali zabwino kwambiri.”​—Genesis 1:31.

^ ndime 9 Mulungu ndi amene anabweretsa Chigumula chimenechi ndipo zikuoneka kuti chinafafaniziratu munda wa Edeni. Lemba la Ezekieli 31:18 limasonyeza kuti pofika zaka za m’ma 1600 B.C.E. “mitengo ya mu Edeni” inali itatha kale. Choncho onse amene anayesetsa kufunafuna malo amene panali munda wa Edeni anangotaya nthawi chifukwa sakanaupeza.

^ ndime 14 Onani kabuku kakuti The Origin of Life​—Five Questions Worth Asking, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 N’zochititsa chidwi kuti madokotala masiku ano apeza kuti nthiti imatha kudzichiritsa mwa njira yodabwitsa. Mosiyana ndi mafupa ena, ngati minofu yake siinaduke nthiti imatha kumeranso.