Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzitsidwa ndi Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzitsidwa ndi Mulungu?

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzitsidwa ndi Mulungu?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzitsidwa ndi Mulungu?

Mulungu ali ndi uthenga wonena za zinthu zabwino woti anthu audziwe. Iye amatiuza uthenga umenewu kudzera m’Baibulo. Baibulo lili ngati kalata imene Atate wathu wakumwamba watilembera.​—Werengani Yeremiya 29:11.

2. Kodi uthenga wabwino umanena za chiyani?

Anthu akufunikira kulamulidwa ndi boma labwino. Palibe wolamulira aliyense padziko lapansi amene anathetsapo chiwawa, kupanda chilungamo, matenda kapena imfa. Koma tamvani nkhani yabwino iyi. Mulungu adzapatsa anthu boma labwino limene lidzathetsa mavuto onse.​—Werengani Danieli 2:44.

3. N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzitsidwa ndi Mulungu?

Posachedwapa, Mulungu adzawononga anthu onse amene amayambitsa mavuto padzikoli. Koma panopo iye akuphunzitsa anthu ofatsa ambirimbiri kuti azikhala moyo wabwino umene umatheka chifukwa cha chikondi. Anthu akuphunzira m’Baibulo mmene angapiririre mavuto amene akukumana nawo, zimene angachite kuti akhale osangalala ndiponso kuti asangalatse Mulungu.​—Werengani Zefaniya 2:3.

  4. Kodi ndani analemba Baibulo?

Baibulo lili ndi mabuku ang’onoang’ono okwana 66. Amuna okwanira 40 ndi amene analemba mabuku amenewa. Mose ndi amene analemba mabuku oyambirira asanu a m’Baibulo, zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Buku lomaliza la m’Baibulo analemba ndi mtumwi Yohane zaka zoposa 1,900 zapitazo. Koma anthu amene analemba Baibulo analemba maganizo a Mulungu, osati awo. Choncho kwenikweni amene analemba Baibulo ndi Mulungu.​—Werengani 2 Timoteyo 3:16; 2 Petulo 1:21.

Timadziwa kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu chifukwa limanena zam’tsogolo mwatsatanetsanane komanso molondola kwambiri. Palibe munthu amene angakwanitse kuchita zimenezo. (Yesaya 46:9, 10) Komanso Baibulo limafotokoza molondola makhalidwe a Mulungu. Lilinso ndi mphamvu zotha kusintha anthu kuti akhale abwino. Mfundo zimenezi zimachititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.​—Werengani Yoswa 23:14; 1 Atesalonika 2:13.

5. Kodi mungatani kuti muzilimvetsa bwino Baibulo?

Yesu ankadziwika kuti anali mphunzitsi wa Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti anthu ambiri amene analankhula nawo ankalidziwa kale Baibulo, iwo ankafunika kuthandizidwa kuti alimvetse bwino. Pofuna kuwathandiza, Yesu ankatchula Malemba osiyanasiyana ndipo kenako ankafotokozera ‘tanthauzo la Malembawo.’ Mu Nsanja ya Olonda muzituluka nkhani ngati imene mukuwerengayi zokhala ndi mutu wakuti, “Phunzirani pa Zimene Mawu a Mulungu Amanena.” Nkhanizi zizikuthandizani kumvetsa bwino Baibulo pofotokozera bwino tanthauzo la malemba osiyasiyana.​—Werengani Luka 24:27, 45.

Kuphunzitsidwa ndi Mulungu za cholinga cha moyo ndi chinthu chosangalatsa kwambiri. Koma anthu ena sangasangalale kukuonani mukuwerenga Baibulo. Koma musafooke ndi zimenezo chifukwa kuti mudzapeze moyo wosatha mufunika kudziwa Mulungu.​—Werengani Mateyu 5:10-12; Yohane 17:3.

Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 2 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.