Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Oyambirira Kulengedwa Ankakhaladi M’munda wa Edeni?

Kodi Anthu Oyambirira Kulengedwa Ankakhaladi M’munda wa Edeni?

Kodi Anthu Oyambirira Kulengedwa Ankakhaladi M’munda wa Edeni?

TAYEREKEZANI kuti muli pamalo ena amaluwa ndi mitengo yambiri. Palibe zinthu zosokoneza zilizonse, piringupiringu wa anthu, phokoso la magalimoto ndiponso nyumba zamipanda. Malo okongolawa ndi aakulu, ndipo palibe chilichonse chosokoneza mtendere. Kuwonjezera pamenepo mulibe nkhawa, simukudwala matenda aliwonse kapena kumva kupweteka kulikonse. Mukungosangalala ndi bata komanso kukongola kwa malowo.

Kulikonse kumene mukuyang’ana mukuona maluwa okongola a mitundu yosiyanasiyana. Mukuonanso mtsinje wa madzi oyera, mitengo yogudira bwino ndiponso udzu wobiriwira. Dzuwa likuwala koma pali mithunzi yambiri. Kukuwomba kamphepo kayaziyazi kamene kakubweretsa kafungo konunkhira bwino ka maluwa ndi mitengo. Mukumvanso kaphokoso kamasamba a mitengo, phokoso la madzi amene akugwera pamiyala ikuluikulu, kulira kwa mbalame ndiponso phokoso la tizilombo touluka. Mukaganizira zimenezi, kodi simukulakalaka mutamakhala malo ngati amenewa?

Padziko lonse anthu amakhulupirira kuti poyamba anthu ankakhala malo ngati amenewa. Kwa zaka zambiri Ayuda, Akhristu ndiponso Asilamu akhala akuphunzitsidwa kuti Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni kuti azikhala mmenemo. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, iwo ankakhala mwamtendere ndiponso mosangalala. Ankakhala mwamtendere ndi nyama ndiponso ndi Mulungu, amene mokoma mtima anakonza zoti anthu amenewa akhale ndi moyo kwamuyaya pamalo abwino amenewa.​—Genesis 2:15-24.

Ahindu nawo amanena nkhani zosiyanasiyana zokhudza mmene moyo m’paradaiso unalili. Abuda amakhulupirira kuti atsogoleri awo achipembedzo otchuka, amene amatchedwa kuti Buda, amakhalapo zinthu padziko lapansi zikakhala kuti zili bwino kwambiri ngati m’paradaiso. Komanso zipembedzo zambiri za ku Africa kuno zimaphunzitsa nkhani zimene zimafanana kwambiri ndi nkhani ya Adamu ndi Hava.

Ndipotu mfundo yakuti kalelo kunali paradaiso imapezeka m’zipembedzo zambiri ndiponso m’miyambo ya anthu ambiri. Munthu wina analemba kuti: “Anthu ambiri amakhulupirira kuti kale kwambiri kunali paradaiso ndipo chilichonse pa nthawi imeneyo chinali bwino. Iwo amati anthu ankakhala mwaufulu, mwamtendere, mosangalala ndiponso kunali chilichonse chimene munthu angafune. Kunalibe munthu woopseza mnzake, kunalibe kusamvana, kapena kukangana. . . . Chikhulupiriro chimenechi chinachititsa kuti anthu kulikonse azilakalaka paradaiso ndiponso kuti aziyesetsa kupeza njira zopezeranso paradaiso ameneyo.”

Kodi n’kutheka kuti pali chimene chinayambitsa nkhani ndi ziphunzitso zonsezi? Kodi mwina “anthu kulikonse” amafuna paradaiso chifukwa chakuti poyamba analipodi? Kodi kale kwambiri kunalidi munda wa Edeni ndiponso Adamu ndi Hava?

Anthu ena amatsutsa mfundo yakuti zimenezi ndi zoona. Chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi masiku ano, anthu ambiri amaganiza kuti nkhani zimenezi ndi nthano zongopeka, ndipo chodabwitsa kwambiri n’chakuti ena amene amakayikira zimenezi ndi atsogoleri achipembedzo. Atsogoleriwa amachititsa anthu kuti asamakhulupirire kuti kunalidi munda wa Edeni. Amanena kuti malo amenewa kunalibe. Iwo amanenanso kuti nkhani imeneyi ndi yongoyerekezera ndipo nthano kapenanso fanizo chabe.

Ndi zoona kuti Baibulo lili ndi nkhani zina zomwe ndi mafanizo chabe, ndipo otchuka mwa mafanizo amenewo anawanena ndi Yesu. Komabe Baibulo limafotokoza nkhani ya mu Edeni osati ngati fanizo, koma ngati mbiri yakale, yoti inachitikadi ndiponso ndi yosavuta kumva. Chifukwa ngati zimenezi sizinachitikedi ndiye kuti nkhani zina zonse zimene zili m’Baibulo nazonso sizinachitike, choncho sitingazikhulupirire. Tiyeni tione chifukwa chake anthu ena amakayikira zakuti kunalidi munda wa Edeni ndiponso tione ngati zifukwa zawozo zilidi zomveka. Kenako tikambirane chifukwa chake nkhani imeneyi ndi yofunika kwa tonsefe.