Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero Chimene Chimachitika Pakapita Mwezi Umodzi M’chaka Chatsopano?

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero Chimene Chimachitika Pakapita Mwezi Umodzi M’chaka Chatsopano?

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero Chimene Chimachitika Pakapita Mwezi Umodzi M’chaka Chatsopano?

CHAKA chilichonse m’mwezi wa January kapena February, anthu ambirimbiri a ku Asia amabwerera kwawo kuti akakhale ndi abale awo pachikondwerero chimene chimachitika pakatha mwezi umodzi m’chaka chatsopano. * Anthuwa amakhala ochuluka kwambiri poyerekezera ndi anthu omwe amabwerera kwawo chaka chilichonse pazifukwa zosiyanasiyana padziko lonse.

Anthu a ku Asia amaona kuti pazikondwerero zonse, chikondwererochi n’chofunika kwambiri. Chimayamba mwezi ukangooneka, mogwirizana ndi kalendala ya ku China ndipo nthawi zambiri pamakhala pakati pa January 21 ndi February 20. Chikondwererochi chimakhala cha masiku angapo ndipo nthawi zina mpaka milungu iwiri.

Cholinga chenicheni cha chikondwererochi n’kutsanzikana ndi chaka chomwe changotha kumene ndiponso kusangalalira chaka chatsopano. Pokonzekera chikondwererochi, anthu amakongoletsa nyumba zawo, amagula zovala zatsopano ndiponso amaphika zakudya zomwe mayina ake amafananirako ndi mawu akuti “mwayi.” Komanso, amayesetsa kubweza ngongole ndiponso kuyanjana ndi ena ngati anasemphana nawo maganizo. Patsiku la chikondwererochi, anthu amapatsana mphatso, kufunirana mafuno abwino omwe nthawi zambiri amakhala oti alemere. Amapatsana zikwama zofiira za ndalama zomwe amakhulupirira kuti n’zopatsa mwayi. Komanso amadya zakudya zapamwamba, amaphulitsa makombola, amaonera magule a nyawu ndipo nthawi zina amangocheza ndi achibale awo kapena anzawo.

Anthu amachita miyambo imeneyi pa zifukwa zosiyanasiyana. Buku lina limanena kuti: “Cholinga chachikulu chimene mabanja, achibale ndiponso anzawo amachitira pamodzi miyambo imeneyi n’kufunirana mafuno abwino a chaka chatsopano, kulemekeza milungu ndiponso mizimu.” (Mooncakes and Hungry Ghosts: Festivals of China) Popeza kuti pachikondwererochi pamachitika zinthu zambiri zokhudza chikhalidwe ndiponso kulambira, kodi Akhristu ayenera kuona bwanji chikondwererochi? Kodi iwo ayenera kuchita nawo?

“Muzikumbukira Kumene Achokera”

Mwambi wina wotchuka wa ku China umati: “Mukamamwa madzi, muzikumbukira kumene achokera.” Mwambi umenewu ukusonyeza mmene anthu ambiri a ku Asia amalemekezera kwambiri makolo awo. Popeza kuti makolo ndi amene anawabereka, sizachilendo kuona ana akulemekeza makolo awo pachikondwererochi.

Mabanja ambiri a ku Asia, amachita zinthu zambiri zapadera patatsala tsiku limodzi kuti chikondwererochi chichitike. Usiku wa tsiku limeneli, mabanja ambiri amadyera limodzi chakudya chapadera. Imeneyi imakhala nthawi yabwino kwambiri kuti anthu apachibale achezere limodzi ndipo aliyense amayesetsa kuti asalephere kupezekapo. Pachakudyacho, iwo samangokonza malo a achibale omwe alipo okha, koma amasunganso malo a achibale awo omwe anamwalira, chifukwa amakhulupirira kuti mizimu yawo imabwera paphwandolo. Buku lina limanena kuti panthawiyi, “pamakhala kulankhulana kwenikweni pakati pa mizimu ya akufa ndi achibale awo.” Buku linanso linati: “Popeza zimenezi zimathandiza kuti ubale wa pakati pa mizimu ya akufa ndi anthu ulimbe, mizimuyo imateteza achibale awowo m’chaka chonsecho.” Ndiyeno kodi Akhristu aziona bwanji mwambo umenewu?

Akhristu amaonanso kuti kukonda ndiponso kulemekeza makolo awo n’kofunika kwambiri. Iwo amatsatira malangizo a Mulungu akuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” (Miyambo 23:22) Iwo amamveranso lamulo la m’Baibulo lakuti: “‘Lemekeza atate wako ndi amayi wako,’ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo: ‘Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndi kutinso ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’” (Aefeso 6:2, 3) Inde, Akhristu oona amakonda makolo awo ndiponso kuwalemekeza.

Baibulo sililetsa anthu kucheza ndi banja lawo. (Yobu 1:4; Luka 15:22-24) Komabe, Yehova akutilamula kuti: “Asapezeke mwa inu . . . wofunsira [mizimu] kapena wofunsira akufa.” (Deuteronomo 18:10, 11) N’chifukwa chiyani Mulungu analetsa zimenezi? Chifukwa Baibulo limanena momveka bwino mmene akufa alili. Limati: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.” Popeza akufa sadziwa chilichonse, sangachite nawo zimene anthu amoyo akuchita komanso sangatithandize kapena kutichitira zoipa. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, anayerekezera imfa ndi tulo. Motero, akufa adzauka ku tulo limeneli panthawi imene Mulungu azidzaukitsa akufa.​—Yohane 5:28, 29; 11:11, 14.

Komanso, Baibulo limasonyeza kuti angelo oipa ndi amene amanamizira kuti ndi “mizimu” ya anthu akufa. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Amafuna kusocheretsa anthu ndiponso kulamulira anthu. (2 Atesalonika 2:9, 10) Malamulo a Mulungu amenewa amatiteteza ku mizimu yoipa. Choncho, chifukwa chokonda Yehova ndiponso pofuna kuti mizimu isamawavutitse, Akhristu amapewa miyambo iliyonse yokhudza kulambira kapena kupempha “mizimu” kuti iwateteze.​—Yesaya 8:19, 20; 1 Akorinto 10:20-22.

Kuwonjezera apo, Akhristu amafunanso kulemekeza “Atate, amene apangitsa banja lililonse, kumwamba ndi padziko lapansi, kukhala ndi dzina.” (Aefeso 3:14, 15) Kodi Atate amenewa n’ndani? Ndi Mlengi wathu Yehova Mulungu amene anatipatsa moyo. (Machitidwe 17:26) Chotero, tikamaganizira zochita nawo chikondwerero chimene chimachitika pakatha mwezi umodzi m’chaka tsopano, tingachite bwino kudzifunsa kuti: Kodi Yehova amaiona bwanji miyambo ya pachikondwererochi? Kodi Mulungu amaiona kuti ndi yabwino?​—1 Yohane 5:3.

Kulemekeza Milungu ya Pakhomo

Pazikondwererozi, pamachitika miyambo yambiri yotchuka yolemekeza milungu yosiyanasiyana ya pakhomo monga mulungu wa chitseko, wa nthaka kapena kuti mzimu woteteza, mulungu wopatsa chuma kapena wobweretsa mwayi ndiponso mulungu wa kukhitchini. Mwachitsanzo, taganizirani zomwe zimachitika pamwambo wolemekeza mulungu wa kukhitchini. * Anthu amakhulupirira kuti kutangotsala masiku ochepa kuti chikondwererochi chichitike, mulungu ameneyu amapita kumwamba kukafotokoza za banja lomwe limamulambira, kwa mulungu wamkulu pa milungu yonse ya ku China wotchedwa Mfumu Jade. Pofuna kuti mulunguyo akanene zabwino zokhudza banjalo, iye asananyamuke, banjalo limamukonzera chakudya chapadera ndipo pamakhala maswiti ndi makeke. Banjalo likafuna kuti iye ayende mofulumira paulendo wake, limatsitsa chithunzi cha mulunguyo pakhoma ndipo nthawi zina amachipaka maswiti pamilomo yake n’kukachiwotcha panja. Ndiyeno pakatsala tsiku limodzi kuti chikondwererochi chichitike, amapachika chithunzi chatsopano cha mulunguyu kukhitchini, pamwamba pa malo ophikira. Iwo amachita zimenezi n’cholinga choti mulunguyu abwererenso m’nyumbamo m’chaka chatsopanocho.

Ngakhale kuti zochitika zambiri pachikondwererochi zingaoneke ngati zabwino, Akhristu amafunitsitsa kutsatira zimene Mawu a Mulungu amanena pankhani ya kulambira. Yesu Khristu anati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.” (Mateyo 4:10) Apa n’zoonekeratu kuti Mulungu amafuna kuti tizilambira iye yekha basi. N’chifukwa chiyani? Taganizirani izi: Yehova ndi Atate wathu wakumwamba. Kodi bambo angamve bwanji ngati ana ake akumukana n’kumanena munthu wina kuti ndiye bambo awo? Zimenezi zingamupweteke kwambiri.

Yesu anazindikira kuti Atate wake wakumwamba ndiye “Mulungu yekha woona,” ndipo Yehova anachita kuuza atumiki ake momveka bwino kuti ‘musakhale nayo milungu ina koma ine ndekha.’ (Yohane 17:3; Eksodo 20:3) Motero, Akhristu oona amafuna kusangalatsa Yehova ndipo safuna kumukhumudwitsa potumikira milungu ina.​—1 Akorinto 8:4-6.

Pamachitika Zokhulupirira Mizimu

Chikondwerero chimene chimachitika pakatha mwezi umodzi m’chaka tsopano, n’chogwirizana kwambiri ndi kukhulupirira nyenyezi. Pakalendala ya ku China, pali nyama 12 zimene zimaimira mwezi uliwonse. Zina mwa nyamazi ndi njoka, nyani ndiponso kalulu. Iwo amakhulupirira kuti khalidwe la munthu aliyense limagwirizana ndi la nyama imene ikuimira mwezi umene munthuyo anabadwa. Komanso, amakhulupirira kuti nyamayo imawathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino m’chakacho. Anthu ambiri amachita miyambo ina ya pachikondwererochi monga kulemekeza mulungu wopatsa chuma kapena wobweretsa mwayi n’cholinga choti awadalitse. Kodi Akhristu ayenera kuona bwanji zochitika zimenezi?

M’Mawu ake, Baibulo, Yehova anachenjeza anthu amene ankadalira openda ‘zam’mwamba, oyang’ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi zimene zidzawagwera.’ Yehova anachenjezanso anthu amene ankalambira “mulungu wamwayi” ndi “mulungu waimfa.” (Yesaya 47:13; 65:11, 12) M’malo mokhulupirira zinthu zina zosadziwika kapena zosaoneka zimene zili zogwirizana ndi mizimu kapena nyenyezi, Akhristu oona akulangizidwa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzaongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Kukhulupirira mizimu kumachititsa munthu kukhala kapolo, koma choonadi cha m’Baibulo chimamasula.​—Yohane 8:32.

Sonyezani Kuti Mumakonda Mulungu

N’zosavuta kudziwa chifukwa chake anthu amachita miyambo ya pachikondwererochi koma n’zovuta kwambiri kusankha kusachita nawo miyamboyi. Ngati mukukhala m’dera limene anthu amachita chikondwererochi, kapena ngati banja lanu limachita nawo chifukwa choti ndi chikhalidwe chanu, ndiye kuti muli ndi udindo waukulu wosankha chochita pankhaniyi.

Ndipotu pamafunika kulimba mtima kuti munthu asachite nawo chikondwererochi pamene anthu ena onse akuchita. Mayi wina wachikhristu wa ku Asia ananena kuti: “Ndinkachita mantha kwambiri chifukwa choti aliyense ankachita chikondwererochi kupatulapo ineyo.” Koma n’chiyani chomwe chinam’thandiza? Iye anapitiriza kuti: “Kukonda kwambiri Mulungu kunandithandiza kuti ndikhalebe wolimba.”​—Mateyo 10:32-38.

Kodi inuyo mumakonda kwambiri Yehova ngati mayi ameneyu? Ngati ndi choncho, mukuchita bwino kwambiri. Iye ndi amene anakupatsani moyo, osati mulungu winawake wosadziwika. Ndipo ponena za Yehova Mulungu, Baibulo limati: “Chitsime cha moyo chili ndi Inu; m’kuunika kwanu tidzaona kuunika.” (Salmo 36:9) Yehova ndi amene amakupatsani zinthu zonse zofunika pamoyo wanu, osati mulungu wa mwayi kapena mulungu wa kukhitchini. (Machitidwe 14:17; 17:28) Ndiyeno popeza Yehova amakuchitirani zimenezi, kodi inuyo mumamukonda? Dziwani kuti ngati mumatero, Yehova adzakudalitsani kwambiri.​—Maliko 10:29, 30.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Chikondwererochi chimatchedwanso Chaka Chatsopano cha ku China, Chikondwerero cha M’dzinja, Chun Jie (China), Tet (Vietnam), Solnal (Korea), kapena Losar (Tibet).

^ ndime 14 Miyambo yomwe imachitika pachikondwererochi imachitika mosiyanasiyana ku Asia koma cholinga chake m’chimodzi. Kuti mudziwe zambiri, onani Galamukani! wachingelezi wa December 22, 1986, masamba 20 ndi 21, ndiponso wa January 8, 1970, masamba 9 mpaka 11.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 23]

Atsimikizireni Achibale Ndiponso Anzanu Kuti Mumawakonda

N’zoona kuti munthu akasiya kuchita nawo chikondwerero chimene chimachitika pakatha mwezi umodzi m’chaka tsopano, anzake ndiponso achibale ake angadabwe ndipo angakwiye komanso kukhumudwa kwambiri. Komabe, pali zambiri zimene mungachite kuti mukhalebe paubwenzi wabwino ndi achibale anu. Mwachitsanzo, taonani zimene Akhristu a m’madera osiyanasiyana ku Asia ananena.

Jiang: “Tisanalowe m’chaka cha tsopano, ndinapita kukachezera achibale anga ndipo ndinawafotokozera mwaulemu chifukwa chake sindizichita nawo miyambo ina yotchuka. Ndinanena zimenezi mosamala kuti iwo asaone ngati ndikunyoza zimene amakhulupirira ndipo ndinayankha mafunso awo mwaulemu pogwiritsa ntchito Baibulo. Zimenezi zinathandiza kuti tikambirane bwino kwambiri nkhani zauzimu.”

Li: “Nthawi ya chikondwererochi isanafike, ndinauza mwamuna wanga mwaulemu kuti ndiyenera kumvera chikumbumtima changa kuti ndikhale wosangalaladi. Ndinam’lonjezanso kuti sindikam’chititsa manyazi tikadzapita kwawo panthawi ya chikondwererochi. Ndipo n’zodabwitsa kuti patsiku limene achibale a mwamuna wanga ankalambira milungu ya makolo, iye ananditenga n’kupita nane kumisonkhano yachikhristu m’dera lina.”

Xie: “Ndinawatsimikizira achibale anga kuti ndimawakonda ndipo ndinawauza kuti zimene ndayamba kukhulupirira zindithandiza kuti ndikhale munthu wabwino. Ndiyeno, ndinayesetsa kusonyeza makhalidwe abwino achikhristu monga kufatsa, chikondi ndiponso kuchita zinthu mwanzeru. Pang’ono ndi pang’ono, iwo anayamba kulemekeza chipembedzo changa. Kenako, mwamuna wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndipo nayenso anakhala Mkhristu woona.”

Min: “Ndinalankhula ndi makolo anga mofatsa komanso mwaulemu. M’malo mowauza kuti ‘akhale ndi mwayi,’ ndinawauza kuti ndimawapempherera nthawi zonse kwa Yehova, yemwe ndi Mlengi wathu, kuti awadalitse ndiponso awathandize kuti akhale ndi mtendere ndiponso chimwemwe.”

Fuong: “Ndinauza makolo anga kuti palibe chifukwa chodikira nthawi ya chikondwererochi kuti ndiwayendere. Choncho ndimawayendera pafupipafupi. Zimenezi zimawasangalatsa kwambiri ndipo anasiya kundinena. Nayenso mng’ono wanga anayamba kuphunzira choonadi cha m’Baibulo.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 20]

Panorama Stock/​age Fotostock