Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero cha Chaka Chatsopano?

Kodi Akristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero cha Chaka Chatsopano?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Ayenera Kuchita Nawo Chikondwerero cha Chaka Chatsopano?

“NTHAŴI zambiri madzulo a usiku woloŵera m’chaka chatsopano sikukhala zochitikachitika. Ndiye cha m’ma leveni koloko usiku, kumayamba kubwera anthu ambiri obayidwa kapena owomberedwa, achinyamata ovulala pangozi za magalimoto, ndi akazi omenyedwa ndi amuna awo. Pafupifupi nthaŵi zonse chimachititsa zonsezi ndi mowa, ” anatero Fernando, dokotala wa ku Brazil.

Poganizira zimenezi, n’zosadabwitsa kuti nyuzipepala ina ya ku Brazil inati tsiku loyamba m’chaka chatsopano limakhala tsiku la matsire padziko lonse. Bungwe lina lofalitsa nkhani ku Ulaya linati “Tsiku lokondwerera chaka chatsopano ndilo tsiku limene anthu amaganiza kuti kusangalala ndiko kofunika kwambiri m’moyo,” ndipo linawonjezeranso kuti ndi “tsiku limene moŵa umawasokoneza kwambiri anthu.”

N’zoona kuti si aliyense amene amakondwerera chaka chatsopano poledzera ndi kuchita zachiwawa. Kwenikweni, pali anthu ambiri amene chikondwererochi amachilakalaka kwambiri. Fernando, amene tam’tchula poyamba paja anati, “Tili ana, tinkalakalaka kwambiri titafika usiku woloŵera m’chaka cha tsopano. Nthaŵi zonse tinkachita maseŵera osiyanasiyana, ndipo zakudya ndi zakumwa nazo zinkangoti mbwee. Usiku tinkakupatirana, kumpsompsonana, ndi kufunirana ‘mafuno abwino m’chaka chatsopano!’”

Masiku anonso pali anthu ambiri amene amaganiza kuti sachita zinthu mopitirira muyezo akamakondwerera chaka chatsopano. Komabe Akristu ayenera kufufuza bwino chiyambi ndiponso cholinga cha chikondwerero chotchuka chimenechi. Kodi chikondwerero cha chaka chatsopano n’chosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?

Umboni wa M’mbuyomo

Chikondwerero cha chaka chatsopano sichinayambe lero. Zolembedwa zakale zimasonyeza kuti ku Babulo ankachitanso zimenezi kale kwambiri cha m’ma 2000 B.C.E. Chikondwererochi, chimene anali kuchita pakati pa mwezi wa March, chinali chofunika kwambiri. “Panthaŵi imeneyo mulungu wotchedwa Maduki anali kuganiza zoti achite ndi dzikolo chaka chotsatira,” limatero buku la The World Book Encyclopedia. Chikondwerero cha ku Babulo cha chaka chatsopano chinkakhala masiku 11 ndipo pa chikondwererocho anthu ankapereka nsembe, ankaguba m’chigulu, ndiponso ankachita miyambo yokhudza kubereka.

Kwa nthaŵi yaitali ndithu, Aroma nawo ankayamba chaka chawo chatsopano m’mwezi wa March. Koma m’chaka cha 46 B.C.E., Mfumu Julius Caesar analamula kuti chikondwererochi chiziyamba tsiku loyamba la mwezi wa January. Tsiku limeneli linali tsiku lokumbukira Janus, mulungu woyambitsa zinthu, ndipo tsopano ankafuna kuti likhale tsiku loyamba la chaka cha Aroma. Tsikulo linasinthadi, koma anthu anapitirizabe kuchita chikondwererocho. Pa tsiku loyamba la mwezi wa January, buku lina lolembedwa ndi McClintock ndi Strong limanena kuti, anthu “ankangotayirira pochita zinthu, ndipo ankakhulupirira miyambo yabodza yosiyanasiyana yachikunja.”

Ngakhale masiku ano, pa chikondwerero cha chaka chatsopano pamakhala miyambo yabodza yosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’madera ena a ku South America, anthu ambiri amaloŵa chaka chatsopano ataimirira ndi mwendo wakumanja. Ena amaimba malipenga ndi kuphulitsa timabomba totulutsa moto. Malingana ndi mwambo wina wa anthu a chi Czech, usiku woloŵera chaka chatsopano imakhala nthaŵi yoti adye msuzi wa mphodza, pamene mwambo wa anthu a chi Slovak panthaŵiyi anthuwo amaika ndalama kapena mamba ansomba kunsi kwa nsalu yoyala patebulo. Miyambo yotereyi, imene cholinga chake n’kupeŵa malodza ndiponso kupereka mwayi, imangolimbikitsa chikhulupiriro chakalekale chija chakuti chaka chatsopano chikamayamba m’pamene mulungu winawake amaganiza zoti achite ndi anthu.

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhaniyi

Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti “Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ayi.” * (Aroma 13:12-14; Agalatiya 5:19-21; 1 Petro 4:3) Akristu sachita nawo chikondwerero cha chaka chatsopano pakuti nthaŵi zambiri anthu amatayirira kuchita zinthu zenizenizo zimene Baibulo limatsutsa. Apa si ndiye kuti Akristu amaletsa anthu kusangalala. Zimenezi si zoona, pakuti iwo amadziŵa kuti Baibulo limalangiza mobwerezabwereza anthu olambira Mulungu woona kuti azisangalala, ndipo limapereka zifukwa zingapo ndithu zoyenera kukondwera nazo. (Deuteronomo 26:10, 11; Salmo 32:11; Miyambo 5:15-19; Mlaliki 3:22; 11:9) Baibulo limanenanso kuti pachikondwerero nthaŵi zambiri pamakhalanso zakudya ndi zakumwa.—Salmo 104:15; Mlaliki 9:7a.

Komabe monga taonera, chikondwerero cha chaka chatsopano chinayambira m’miyambo yachikunja. Chipembedzo chonyenga n’chodetsedwa ndipo n’chonyansa pamaso pa Yehova Mulungu, ndipo Akristu sachita miyambo iliyonse imene inayamba motere. (Deuteronomo 18:9-12; Ezekieli 22:3, 4) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Pachifukwa chomveka, Paulo anawonjezera kuti: “Musakhudza kanthu kosakonzeka.”—2 Akorinto 6:14-17a.

Akristu amazindikiranso kuti kuchita nawo miyambo yabodza yachikunja sikubweretsa chimwemwe ndi kum’pangitsa munthu kukhala pabwino, makamaka chifukwa chakuti Mulungu sayanjana ndi munthu wochita zoterozo. (Mlaliki 9:11; Yesaya 65:11, 12) Chinanso n’chakuti Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti azikhala odzisunga ndiponso odziletsa pochita zinthu. (1 Timoteo 3:2, 11) N’zoonekeratu kuti ngati timavomereza kuti timatsatira ziphunzitso za Kristu n’kulakwa kuchita nawo chikondwerero chodziŵika ndi kuchita zinthu motayirira.

Ngakhale chikondwerero cha chaka chatsopano chitatidolola mtima, Baibulo limatiuza kuti “musakhudza kanthu kosakonzeka” ndi kuti ‘tileke chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.’ Kwa amene amamvera, Yehova akuwatsimikizira ndi mawu okoma aŵa: “Ine ndidzalandira inu, . . . ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa ine ana aamuna ndi aakazi.” (2 Akorinto 6:17b–7:1) N’zoonadi, iye akulonjeza kuti anthu okhulupirika kwa iye adzawadalitsa ndiponso adzawakhazika pabwino kwamuyaya.—Salmo 37:18, 28; Chivumbulutso 21:3, 4, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Ponena kuti “madyerero ndi kuledzera” n’kutheka kuti Paulo amatanthauzanso zinthu zimene zinkachitika pa chikondwerero cha chaka chatsopano, chifukwa anthu ambiri ku Roma ankachita zimenezi m’zaka zapakati pa 1 mpakana 100 C.E.