Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anzeru Akum’mawa Atatu Anapitadi Kukaona Yesu Ali Wakhanda?

Kodi Anzeru Akum’mawa Atatu Anapitadi Kukaona Yesu Ali Wakhanda?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Anzeru Akum’mawa Atatu Anapitadi Kukaona Yesu Ali Wakhanda?

Nkhani imene imanenedwa ndi anthu padziko lonse yokhudza Khirisimasi, imafotokoza kuti mafumu atatu, kapena kuti anzeru akum’mawa, anatenga mphatso kukapereka kwa Yesu ali wakhanda. Kodi zimenezi ndi zoona? Tiyeni tione.

Mabuku awiri a Uthenga Wabwino, Mateyo ndi Luka, amafotokoza nkhani ya kubadwa kwa Yesu. Nkhani zimenezi zimasonyeza kuti ndi abusa wamba okha amene anapita kukaona Yesu atangobadwa kumene. Abusawo anali kubusa pafupi ndi kumene Yesuyo anabadwira. Koma anthu amene amanenedwa kuti anali mafumu, kapena kuti anzeru akum’mawa, kwenikweni anali okhulupirira nyenyezi osati mafumu, ndipo Baibulo silitchula kuti analipo angati. Anthu okhulupirira nyenyeziwa sanafikire kukhola limene Yesu anabadwira ayi, koma anafika Yesu atasinkhuka komanso akukhala m’nyumba. Ndipo kufika kwawo kukanachititsa kuti Yesu aphedwe.

Mukaona bwinobwino nkhani yonena za kubadwa kwa Yesu imene inalembedwa ndi Luka, mupeza kuti nkhaniyi ikuti: “Munalinso abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda. Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova anaima chapafupi ndi iwo, ndipo . . . anawauza kuti: ‘. . . Mukapeza mwana wakhanda wokutidwa m’nsalu, atagona modyeramo ziweto.’ . . . [Abusawo] anapita mwachangu ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyeramo ziweto.”​—Luka 2:8-16.

Yosefe, Mariya ndiponso abusa okha ndi amene analipo Yesuyo ali wakhanda. Palibenso munthu wina amene akutchulidwa malinga ndi zimene Luka analemba.

Tsopano onaninso nkhaniyi pa Mateyu 2:1-11 pogwiritsira ntchito Baibulo la Buku Lopatulika. Lembali limati: “Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu m’Betelehemu wa Yudeya m’masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum’mawa anafika ku Yerusalemu . . . Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Mariya amake.”

Taonani kuti nkhaniyi yangotchula kuti “anzeru a kum’mawa” basi, osati “anzeru a kum’mawa atatu,” ndiponso kuti iwo anafikira ku Yerusalemu, osati kumzinda wa Betelehemu kumene kunabadwira Yesu. Pamene iwo anadzafika ku Betelehemuko, Yesu anali “kamwana,” osatinso wakhanda, komanso anali m’nyumba, osati modyera ziweto.

Chinanso, ngakhale kuti Baibulo la Buku Lopatulika limagwiritsira ntchito mawu akuti “anzeru” pofotokoza za anthu amenewa, Mabaibulo ena amagwiritsira ntchito mawu akuti “okhulupirira nyenyezi.” Mogwirizana ndi zimene buku lina lofotokoza za Uthenga Wabwino wa Mateyo limanena, mawu akuti “anzeru” anamasuliridwa kuchokera “ku dzina lachigiriki limene poyamba linkanena za ansembe a ku Perisiya omwe anali akatswiri odziwa za nyenyezi.” (A Handbook on the Gospel of Matthew) Ndipo buku lina lotanthauzira mawu ochokera mu Chipangano Chatsopano limati mawu amenewa akutanthauza “mfiti, wamatsenga, wonamizira kuti ali ndi mphamvu zamatsenga, sing’anga wa zamatsenga.”​—The Expanded Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words.

Ngakhale kuti masiku ano kwafala akatswiri okhulupirira nyenyezi ndiponso nkhani zaufiti, Baibulo limaletsa zimenezi. (Yesaya 47:13-15) Zimenezi zili m’gulu la kukhulupirira mizimu ndipo Mulungu amadana nazo. (Deuteronomo 18:10-12) Ndiye chifukwa chake palibe mngelo wa Mulungu amene analengeza za kubadwa kwa Yesu kwa okhulupirira nyenyezi. Komabe Mulungu anawachenjeza m’maloto kuti asabwererenso kwa Mfumu Herode, yemwe anali munthu woipa kwambiri popeza kuti ankafuna kupha Yesu. Choncho “anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina.”​—Mateyo 2:11-16.

Ndithudi, Akhristu oona sangasangalale kumafalitsa nkhani yabodza zokhudza kubadwa kwa Yesu.