Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndidzafuula Mpaka Liti” Kuti Mundithandize?

“Ndidzafuula Mpaka Liti” Kuti Mundithandize?

 “Ndidzafuula Mpaka Liti” Kuti Mundithandize?

Jayne, yemwe anali ndi matenda a khansa anadandaula kuti: “Ndingofuna kupwetekaku kutasiya.” Iye ankadandaula chifukwa matendawo ankafalikira thupi lake lonse. Achibale ndiponso azinzake ankalakalaka atam’thandiza kuti achire n’cholinga choti asamavutikenso. Choncho iwo ankapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize. Koma kodi Mulungu anamva mapempherowo? Kodi zimam’khudza n’komwe munthu akamavutika?

MULUNGU amadziwa mavuto amene anthu akukumana nawo. Mawu ake, Baibulo, amati: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka.” (Aroma 8:22) Mulungu amadziwa kuti pali anthu mamiliyoni ambirimbiri omwe akumva kupweteka ndiponso kuvutika maganizo, ngati mmene Jayne akuvutikira. Mulungu amadziwanso kuti anthu 800 miliyoni amagona ndi njala tsiku lililonse. Komanso amadziwa kuti pali anthu mamiliyoni ambiri amene amachitiridwa nkhanza pabanja pawo. Amadziwanso kuti pali makolo ambiri omwe amada nkhawa akamaganiza za tsogolo la ana awo. Kodi munayamba mwadzifunsapo ngati Mulungu adzathetse mavuto amenewa? Ngati anthufe mwachibadwa, timafuna kuthandiza achibale athu akamavutika, kuli bwanji Mulungu?

Sizachilendo ngati inuyo munaganizapo zimenezi. Zaka zoposa 2,600 zapitazo, munthu wina wokhulupirika, dzina lake Habakuku, ankaganizanso ngati mmene anthu ambiri masiku ano amaganizira. Iye anafunsa Mulungu kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndewu, nauka makani.” (Habakuku 1:2, 3) Habakuku, amene anali mneneri wachiheberi, anaona zinthu zambiri zoopsa ndiponso zankhanza zimene zinkachitika m’nthawi yake. Masiku ano, zinthu ngati zimenezi zili ponseponse ndipo anthu achifundo amakhumudwa nazo.

Kodi Mulungu ananyozera zimene Habakuku ankadandaula nazozi? Ayi, iye anamvetsera madandaulo ake ndipo anam’limbikitsa. Yehova Mulungu analimbikitsa chikhulupiriro cha Habakuku pomulonjeza kuti Iye athetsa mavutowo. Zimene Mulungu anamuuzazo zingakulimbikitseni ngati mmene zinalimbikitsira Jayne ndi abale ake. Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso awa: Kodi tingatsimikizire bwanji kuti Mulungu amatikonda? Kodi athetsa bwanji mavutowa, nanga awathetsa liti?