Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Adamu Anali Wangwiro, Kodi Zinatheka Bwanji Kuti Achimwe?

Ngati Adamu Anali Wangwiro, Kodi Zinatheka Bwanji Kuti Achimwe?

Zimene Owerenga Amafunsa

Ngati Adamu Anali Wangwiro, Kodi Zinatheka Bwanji Kuti Achimwe?

Mulungu analenga Adamu ndi ufulu wosankha kumvera kapena kusamvera. Pachifukwa chimenecho zinali zotheka kuti Adamu achimwe. Ufulu umenewu sukutsutsana ndi mfundo yakuti Adamu anali munthu wangwiro. Pankhani ya ungwiro, tizidziwa kuti Mulungu yekha ndi amene ali ndi ungwiro wopanda malire. (Deuteronomo 32:3, 4; Salmo 18:30; Maliko 10:18) Komano ungwiro wa wina aliyense kapena china chilichonse umakhala ndi malire ake. Mwachitsanzo, munthu angatchule mpeni kuti ndi wangwiro, potanthauza kuti mpeniwo ungathe kudula bwinobwino nyama kapena zinthu zina. Ngakhale zili choncho, sikuti mungagwiritsire ntchito mpeniwo podyera phala. Chitsanzo chimenechi chikutithandiza kumvetsa kuti ungwiro wa chinthu umangotengera ntchito kapena cholinga cha chinthucho.

Ndiyeno kodi Mulungu analenga Adamu ndi cholinga chotani? Cholinga cha Mulungu chinali choti kudzera mwa Adamu, apange anthu anzeru okhala ndi ufulu wosankha. Choncho anthu amene akufuna kukonda Mulungu ndi njira zake ayenera kusonyeza chikondi chawocho posankha okha kutsatira malamulo ake. Motero Mulungu sanalenge anthu kuti azingomumvera popanda kuganiza. Koma anawalenga kuti azichita kusankha kumumvera, mochokera pansi pamtima. (Deuteronomo 10:12, 13; 30:19, 20) Motero Adamu akanakhala kuti analibe mphamvu yosankha kusamvera, akanakhala woperewera, kapena kuti wopanda ungwiro. Baibulo limasonyeza kuti Adamu anasankha yekha kugwiritsira ntchito ufulu wake wosankhawu mwa kutsatira mkazi wake, amene sanamvere lamulo la Mulungu lokhudza “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.”​—Genesis 2:17; 3:1-6.

Ndiyeno kodi pamenepa tingati Mulungu analenga Adamu m’njira yoti sakanatha kusankha kuchita zinthu zoyenera? Ndipo kodi n’chifukwa chake sanathe kuganiza bwino n’kupewa chiyeso chimene anakumana nacho? Adamu asanasankhe kusamvera Mulungu, Yehova anaona zinthu zonse zimene analenga, kuphatikizapo anthu awiriwo kuti zonse “zinali bwino ndithu.” (Genesis 1:31) Motero, Adamu sanachimwe chifukwa choti Mulungu analakwitsa chinachake pomulenga. N’chifukwa chake iye atachimwa, Mulungu anati mlandu wonse wa tchimolo unali wa Adamuyo. (Genesis 3:17-19) Adamu sanasankhe kuti kukonda Mulungu ndiponso chilungamo kumulimbikitse kumvera Mulungu kuposa wina aliyense.

Komanso kumbukirani kuti Yesu ali padziko pano anali wangwiro ngati Adamu, chifukwa choti anabadwa mwa mphamvu ya mzimu woyera. Motero mosiyana ndi ana onse a Adamu, Yesu sanatengere khalidwe lililonse lomwe likanachititsa kuti azilephera kupewa mayesero. (Luka 1:30, 31; 2:21; 3:23, 38) Komabe Yesu anasankha yekha kukhala wokhulupirika kwa Atate wake ngakhale pamene anakumana ndi mayesero ovuta kwambiri. Choncho, nayenso Adamu anafuna yekha kugwiritsira ntchito ufulu wake wosankha, kuti asamvere malamulo a Yehova.

Komano kodi n’chifukwa chiyani Adamu anasankha kusamvera Mulungu? Kodi iye ankaona kuti akatero ndiye kuti zinthu ziyamba kumuyendera bwino kwambiri? Ayi, chifukwatu mtumwi Paulo analemba kuti “Adamu sananyengedwe.” (1 Timoteyo 2:14) Koma anachita kusankha kumvera zofuna za mkazi wake, yemwe anali atasankha kale kudya zipatso za mumtengo woletsedwa. Adamu anakonda kwambiri kusangalatsa mkazi wake kuposa kumvera Mlengi wake. Pamene Hava ankamupatsa chipatso choletsedwacho, Adamu akanatha kuganizira kaye mmene kusamvera kungasokonezere ubwenzi wake ndi Mulungu. Koma chifukwa choti sankakonda Mulungu ndi mtima wonse, zinali zosavuta kuti Adamu atengeke ndi mayesero, ngakhale ochokera kwa mkazi wake.

Mmene Adamu ankayamba kubereka anali atachimwa kale, motero ana ake onse anabadwa opanda ungwiro. Koma, mofanana ndi Adamu, tonse tili ndi mphatso ya ufulu wosankha. Ndiyetu tiyeni tisankhe kuganizira mozama za ubwino wa Yehova ndi kuyesetsa kuyamba kum’konda kwambiri Mulungu, chifukwa Iye ndi woyenera kuti tizimumvera ndi kumulambira.​—Salmo 63:6; Mateyo 22:36, 37.