Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulosi Wokhudza Zimene Zikuchitika Masiku Ano

Ulosi Wokhudza Zimene Zikuchitika Masiku Ano

 Ulosi Wokhudza Zimene Zikuchitika Masiku Ano

BAIBULO linaneneratu kuti Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere wosatha ndi chisangalalo padziko lapansi. (Danieli 2:44) M’pemphero la Ambuye, Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:10) Muulosi wodziwika kwambiri umene Yesu anauza ophunzira ake paphiri la Maolivi, iye ananeneratu zinthu zosiyanasiyana zimene zidzachitike Ufumuwo usanabwere. Iye anati zinthu zonsezi zidzakhala chizindikiro chooneka bwino kwa anthu onse oona mtima. Kodi ndi mbali ziti za chizindikiro chimenechi zimene inuyo mwaziona?

Nkhondo Padziko Lonse. Yesu ananeneratu kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyo 24:7) Nkhondo yoyamba yapadziko lonse isanachitike mu 1914, nkhondo zinkangokhala za apa ndi apo m’madera ena. Koma nkhondo yoyamba ya padziko lonse inamenyedwa m’madera ambiri. Inachititsanso kuti anthu  ayambe kupanga zida za nkhondo zambiri ndiponso zoopsa kwambiri kuposa zimene zinkapangidwa kale. Mwachitsanzo, panthawiyo anali atangotulukira kapangidwe ka ndege ndipo ndegezi anazigwiritsira ntchito poponya mabomba amene anapha anthu osalakwa. Kupanga zida zankhondo zochuluka kunachititsa kuti chiwerengero cha anthu ophedwa chichuluke kwambiri. Moti theka la asilikali pafupifupi 65 miliyoni amene ankamenya nkhondoyo anaphedwa kapena kuvulazidwa. Komatu patsogolo pake chiwerengero cha anthu ophedwa pankhondo chinawonjezeka kuposa pamenepa. Katswiri wina wa mbiri yakale ananena kuti “sitingathe kudziwa chiwerengero chonse” cha asilikali ndiponso anthu wamba amene anaphedwa pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ndipo panopa nkhondo zikupitirirabe.

Njala Padziko Lonse. Yesu ananeneratu kuti, “kudzakhala njala.” (Mateyo 24:7) M’chaka cha 2005 magazini ina inati: “Padziko lonse pali anthu 854 miliyoni (anthu pafupifupi 14 pa 100 alionse) amene akuvutika chifukwa cha kuperewera kwa chakudya.” (Science) Mu 2007, lipoti lina la bungwe la United Nations loyang’anira za chakudya padziko lonse linati pali mayiko 33 amene akulephera kupeza chakudya chokwanira anthu a m’mayikowo. Masiku ano anthu padziko lonse akukolola chakudya chambiri. Ndiyeno kodi zikutheka bwanji kuti chakudya chizisowa? Chifukwa chimodzi n’chakuti minda yambiri akuigwiritsira ntchito polima mbewu zimene akupangira mafuta a galimoto. Nyuzipepala ina ya ku South Africa inati: “Kuti apange mafuta odzaza thanki imodzi yagalimoto yaing’ono, amawononga chakudya choti munthu mmodzi angadye kwa chaka chonse.” (The Witness) Ngakhale m’mayiko olemera, chakudya n’chokwera mtengo kwambiri moti anthu ena sadya chakudya chamadzulo n’cholinga choti alipire zinthu zina zofunikira, monga mankhwala ndi magetsi.

Zivomezi Zoopsa. Yesu ananenanso kuti, “kudzachitika zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Mwina inuyo mwaona kuti masiku ano anthu ambiri akuvutika chifukwa cha zivomezi kuposa kale. M’chaka cha 2007, katswiri wina wa maphunziro a zivomezi wa ku India, dzina lake R. K. Chadha, anati: “Sitinali kuyembekezera kuti zivomezi zichuluka chonchi padziko lonse. Ndipo palibe amene akudziwa chifukwa chake.” Komanso anthu ambiri akukhala m’madera amene mumachitika zivomezi kawirikawiri ndipo izi zikuchititsa kuti chiwerengero cha anthu ofa pa zivomezi chiwonjezereke. Mu 2004, pa nyanja ya mchere ya Indian Ocean panachitika chivomezi ndipo kenako kunachitika tsunami. Bungwe lina lofufuza za nthaka linati zimenezi zinachititsa kuti “chaka chimenechi chikhale chaka chimene pafa anthu ambiri chifukwa cha zivomezi poyerekezera ndi zaka pafupifupi 500 zam’mbuyomu. Chaka chimenechi chinali pa nambala 2 pa zaka zimene anthu ambiri anafa ndi zivomezi.”​—U.S. Geological Survey.

Matenda Osamva Mankhwala. Yesu ananeneratunso kuti “kudzakhala miliri.” (Luka 21:11) Padziko lonse lapansi matenda akale komanso atsopano akusautsa anthu ambirimbiri ndipo mankhwala amene amadaliridwa kuti angachize matendawa sakuthandizanso. Mwachitsanzo, padziko lonse mayiko akhala akuyesetsa kuti athetseretu malungo koma zimenezi sizikuphula kanthu. Komanso anthu ambirimbiri akufa ndi matenda akale monga TB, omwe panopo ayamba kuvuta kwambiri chifukwa cha matenda a Edzi ndi matenda enanso atsopano. Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linati: “Munthu mmodzi pa anthu atatu alionse padziko lapansi ali ndi tizilombo toyambitsa matenda a TB.” Bungwelo linanena kuti kachilombo ka HIV kakuchititsa kuti TB ifale m’mayiko ambiri. Pasekondi iliyonse munthu mmodzi amatenga matenda a TB ndipo masiku ano matendawa sakumva mankhwala. Magazini ina inati m’chaka cha 2007 munthu wina wa ku Ulaya anapezeka ndi TB “yosamva mankhwala a mtundu uliwonse amene alipo.”​—New Scientist.

Makhalidwe Oipa. Yesu ananena kuti:  “Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, ochuluka chikondi chawo chidzazirala.” (Mateyo 24:12) Kuwonjezera pa zimene Yesu ananenazi, mtumwi Paulo ananena kuti makhalidwe abwino adzatha. Iye anafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu ukadzatsala pang’ono kuwononga dongosolo la dzikoli, padzakhala “masiku otsiriza,” osautsa kwambiri. Anati: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.” (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi simukuvomereza kuti masiku ano anthu ambiri ali ndi makhalidwe oipa amenewa kusiyana ndi kale?

Yesu ndi Paulo sananene zinthu zonse zokhudza makhalidwe a anthu, ndale za dziko, komanso zochitika zina zimene zikuipitsa dzikoli. Koma mawu amene ananeneratu amafotokoza molondola zochitika za masiku anozi ndiponso makhalidwe a anthu omwe tikuwaonawa. Nanga bwanji zam’tsogolo? Ulosi wa Yesaya, umene umafotokoza momveka za kubwera kwa Mesiya, umanenanso zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padziko lapansi. Tiyeni tione zinthu zimenezi m’nkhani yotsatirayi.

[Chithunzi patsamba 6]

“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina”

[Chithunzi patsamba 7]

“Kudzakhala miliri”

[Mawu a Chithunzi]

© WHO/​P. Virot