Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bambo Wabwino?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bambo Wabwino?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bambo Wabwino?

“Atate inu, musamakwiyitse ana anu, kuti asakhale opsinjika mtima.”​—Akolose 3:21

KODI bambo angatani kuti asamakwiyitse ana ake? Ayenera kudziwa bwino kufunika kwa udindo wake monga bambo. Magazini ina yofotokoza za maganizo inati: “Zochita za bambo zimakhudza kwambiri maganizo ndiponso nzeru za ana.”

Kodi udindo wa bambo ndi wotani? M’mabanja ambiri bambo amangooneka ngati munthu wolanga ana basi. Mwachitsanzo, ana akalakwa, azimayi ambiri amakonda kuwauza kuti: ‘Uona bambo ako akabwera!’ Inde, kuti ana akule bwino amafunika kulangidwa moyenerera komanso safunika kuwalekerera. Komabe, kukhala bambo wabwino kumafuna zambiri.

N’zomvetsa chisoni kuti abambo ambiri analibe munthu wowapatsa chitsanzo chabwino pankhani yolera ana. Amuna ena analeredwa popanda bambo. Ndipo ena analeredwa ndi bambo wovuta kwambiri, moti nawonso akakula amadzakhala bambo wovuta. Kodi abambo otere angasinthe bwanji kuti ayambe kulera bwino ana awo?

Pali buku limene lili ndi malangizo abwino kwambiri okhudza mmene mungakhalire bambo wabwino. Buku limeneli ndi Baibulo ndipo lili ndi malangizo othandiza kwambiri m’banja. Malangizo ake si ofanana ndi a anthu moti n’zosatheka kugwa nawo m’mavuto. Malangizo a m’Baibulo amasonyeza nzeru za Mlembi wa bukuli, Yehova Mulungu, yemwe anayambitsa banja. (Aefeso 3:14, 15) Ngati ndinu bambo mungachite bwino kwambiri kuona zimene Baibulo limanena pankhani ya kulera ana. *

Ana amafunika kukhala ndi bambo wabwino kuti akule bwino, aziganiza bwino, komanso kuti azikonda Mulungu. Mwana amene amagwirizana komanso kukondana kwambiri ndi bambo ake sangavutikenso kukondana kwambiri ndi Mulungu. Ndipotu Baibulo limanena kuti Mlengi wathu Yehova, ndi Atate wathu. (Yesaya 64:8) Tsopano tiyeni tikambirane zinthu 6 zimene bambo ayenera kuchitira ana ake. Tiona mmene kutsatira mfundo za m’Baibulo kungathandizire bambo kuchita chilichonse mwa zinthu 6 zimenezi.

1 Bambo Ayenera Kukonda Ana Ake

Yehova ndiye chitsanzo cha Tate wabwino kuposa Tate wina aliyense. Posonyeza kuti Yehova amakonda Yesu, yemwe ndi Mwana wake woyamba kubadwa, Baibulo limati: “Atate amakonda Mwana wake.” (Yohane 3:35; Akolose 1:15) Yehova ananena maulendo angapo kuti amakonda Mwana wake ndiponso amakondwera naye. Pamene Yesu anali kubatizidwa, Yehova analankhula kuchokera kumwamba kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.” (Luka 3:22) Yesu sanakayikirepo zoti Atate wake amamukonda. Kodi abambo angaphunzirepo chiyani pa chitsanzo chimene Mulungu anaperekachi?

Musamaume pakamwa kuuza ana anu kuti mumawakonda. Kelvin, yemwe ali ndi ana asanu anati: “Ndakhala ndikuyesetsa kuwasonyeza ana anga chikondi powauza kuti ndimawakonda komanso pokhala ndi nthawi yothandiza mwana aliyense payekha. Ndinkathandiza kuwasintha matewera ndiponso kuwasambitsa.” Ana anu ayeneranso kudziwa kuti mumakondwera nawo. Choncho musamakonde kumangowakalipira zilizonse. M’malomwake muzikonda kuwayamikira. Donizete, amene ali ndi ana awiri aakazi, a zaka 14 ndi 16, anati: “Bambo ayenera kukhala maso ndi zochita za ana ake kuti apeze mpata wowayamikira.” Ana akamadziwa kuti mumakondwera nawo amadziona kuti ndi ofunika. Ndiyeno zimenezi zingawathandize kuti ayambe kukonda kwambiri Mulungu.

2 Bambo Azipereka Chitsanzo kwa Ana Ake

Lemba la Yohane 5:19 limati Yesu amachita “chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.” Taonani kuti lembali likusonyeza kuti Yesu anaona ndiponso kuchita zimene Atate wake ‘anali kuchita.’ Nthawi zambiri ana amachitanso chimodzimodzi. Mwachitsanzo, ngati bambo amalemekeza kwambiri mkazi wake, ana ake akakula amalemekezanso akazi. Si maganizo a anyamata okha amene amakhudzidwa ndi zochita za bambo awo. Atsikananso akamaona zochita za bambo awo amangoti n’zimene amuna onse amachita.

Kodi ana anu sakonda kupepesa akalakwa? Pankhani imeneyi chitsanzo chanunso n’chofunika kwambiri. Kelvin amakumbukira kuti nthawi ina ana ake awiri aamuna anawononga kamera yake, yomwe inali yodula kwambiri. Chifukwa chaukali, iye anamenya tebulo mwamphamvu mpaka kuliwaza pakati. Pambuyo pa zimenezi, Kelvin anadzimvera chisoni kwambiri ndipo anapepesa kwa aliyense, kuphatikizaponso mkazi wake, chifukwa chochita zinthu mopsa mtima. Iye amaona kuti ana ake anaphunzirapo kanthu pa kupepesa kwake, chifukwa nawonso akalakwitsa zinazake nthawi zonse amapepesa.

3 Bambo Azionetsetsa Kuti Ana Akusangalala Pakhomo

Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo.” (1 Timoteyo 1:11) N’zosadabwitsa kuti Mwana wake, Yesu, ankasangalala kwambiri kukhala ndi Atate wake. Lemba la Miyambo 8:30 limatithandiza kumvetsa ubwenzi umene unalipo pakati pa Yesu ndi Atate wake: “Ndinali pa mbali [pa Atate] ngati mmisiri; . . . ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse.” Apatu tingaone kuti Atate ndi Mwanayu ankakondana kwabasi.

Muzionetsetsa kuti ana anu akusangalala pakhomopo. Chimene chingakuthandizeni ndicho kupeza nthawi yosewera nawo. Kusewera nawo kumathandiza kuti muzikondana kwambiri. Felix, ali ndi mwana wachinyamata ndipo anavomereza mfundo imeneyi. Iye anati: “Kupeza nthawi yocheza ndi mwana wanga kwathandiza kwambiri kuti tizigwirizana. Timasewera limodzi, kuchezera limodzi ndi anzathu, komanso kuyendera limodzi pokaona malo. Zimenezi zathandiza kuti banja lathu likhale logwirizana kwambiri.”

4 Bambo Aziphunzitsa Ana Ake Kukonda Mulungu

Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Zimene ndinamva kwa iye [Atate], zomwezo ndikuzilankhula m’dzikoli.” (Yohane 8:26) Mulungu amaona kuti bambo ndiye ali ndi udindo wophunzitsa ana ake kuti azichita zinthu zabwino ndiponso kuti azikonda Mulungu. Udindo umodzi wa abambo ndiwo kukhomereza mfundo za makhalidwe olungama m’mitima ya ana awo. Ayenera kuyamba kuwaphunzitsa zimenezi adakali aang’ono. (2 Timoteyo 3:14, 15) Felix anayamba kuwerengera mwana wake nkhani za m’Baibulo kuyambira ali wamng’ono. Iye ankagwiritsa ntchito nkhani zosiyanasiyana zokhala ndi zithunzi zokongola, monga zimene zili mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Mwana wake atakula pang’ono, iye anayamba kumuwerengera mabuku ena ofotokoza Baibulo, mogwirizana ndi msinkhu wake.

Donizete anati: “Sizophweka kuchititsa phunziro la Baibulo pa banja m’njira yosangalatsa. Ndi bwino kuti makolo azisonyeza kuti amakonda zinthu zauzimu, chifukwa ana sachedwa kuzindikira ngati makolo awo sachita zimene amanena.” Carlos, amene ali ndi ana atatu aamuna, anati: “Mlungu uliwonse banja lathu lonse limakhala pansi kuti tikambirane zinthu zimene tikufunikira pabanjapo. Aliyense amapatsidwa mpata woti anene zoti tidzakambirane.” Nthawi zonse Kelvin ankayesetsa kupeza mpata wolankhula za Mulungu kwa ana ake kulikonse kumene ali komanso pochita china chilichonse. Zimenezi zikutikumbutsa mawu a Mose akuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”​—Deuteronomo 6:6, 7.

5 Bambo Azilangiza ndi Kulanga Ana ake

Ana amafunika kulangizidwa ndi kulangidwa kuti adzakhale anthu olongosoka ndiponso odalirika. Makolo ena amaganiza kuti zimenezi zimatanthauza kukhaulitsa, kuopseza, kapena kunyoza anawo. Koma Baibulo limasonyeza kuti kulangiza ndiponso kulanga ana sikutanthauza kuwachitira nkhanza. Limati makolo azilanga ana awo mwachikondi, monga mmene Yehova amachitira. (Aheberi 12:4-11) Baibulo limati: “Atate, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.”​—Aefeso 6:4.

Inde, nthawi zina ana angafunike kuwalanga. Koma nthawi zonse muyenera kumuuza mwanayo chifukwa chimene mukumulangira. Musamalange mwana m’njira yoti aziona ngati kuti simukumufuna. Baibulo sililimbikitsa kumenya mwana kwambiri, mpaka kumuvulaza. (Miyambo 16:32) Kelvin anati: “Nthawi zonse ndikafuna kulanga ana anga akalakwa kwambiri, ndinkayesetsa kuwathandiza kuona kuti ndikuwalanga chifukwa choti ndimawakonda.”

6 Bambo Aziteteza Ana Ake

Ana amafunika kuwateteza kuti asasokonezedwe ndi zinthu zosiyanasiyana komanso kuti asamacheze ndi anthu amene angawononge khalidwe lawo. N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano kuli “anthu oipa” amene cholinga chawo ndicho kupezerera ana, chifukwa sadziwa zambiri. (2 Timoteyo 3:1-5, 13) Kodi ana anu mungawateteze bwanji kwa anthu otere? Baibulo limapereka malangizo anzeru otsatirawa: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Kuti muteteze ana anu ku zinthu zoopsa, muyenera kukhala maso ndi zinthu zotere. Muzikhala tcheru kuona zinthu zimene zingalowetse ana anu m’mavuto, ndipo muzipezeratu njira zopewera zinthuzo. Mwachitsanzo, ngati mumalola ana anu kugwiritsira ntchito Intaneti, onetsetsani kuti akudziwa kuigwiritsa ntchito m’njira yosawalowetsa m’mavuto. Zingakhale bwino kuika kompyuta poyera kuti muzitha kuona zimene anawo akuchita pa Intaneti.

Bambo aziwathandiza ana ake kukhala okonzeka kuthana ndi zoopsa zimene angakumane nazo m’dzikoli, lomwe ladzaza ndi anthu ofuna kupezerera ana. Kodi ana anu amadziwa zimene angachite ngati munthu wina atafuna kuwachita zachipongwe inuyo kulibe? * Ana anu amafunika kudziwa njira yoyenera ndiponso yosayenera yogwiritsira ntchito ziwalo zawo. Kelvin anati: “Sindinkalola kusiyira anthu ena ntchito imeneyi, ngakhale aphunzitsi awo. Ndinkaona kuti ndi udindo wanga kuphunzitsa anawo nkhani zokhudza kugonana ndiponso zokhudza achidyamakanda.” Ana onse a Kelvin anakula bwinobwino ndipo panopo ali m’mabanja olongosoka.

Pemphani Mulungu Kuti Akuthandizeni

Mphatso yaikulu kwambiri imene bambo angapereke kwa ana ake ndiyo kuwathandiza kukhala ndi ubwenzi wolimba kwambiri ndi Mulungu. Pankhani imeneyi, chitsanzo cha bamboyo n’chofunika kwambiri. Donizete anati: “Bambo azisonyeza kuti iyeyo payekha amaona kuti ubwenzi wake ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri. Zimenezi zizionekera kwambiri bamboyo akakumana ndi mavuto enaake. Panthawi ngati zimenezi, m’pamene pamaonekera kuti iye amadalira kwambiri Yehova. Ana angaphunzire kufunika kokhala paubwenzi ndi Yehova akamamva bamboyo akupemphera limodzi ndi banjalo, n’kumayamikira Mulungu nthawi zonse chifukwa cha zabwino zimene amawachitira.”

Ndiyeno kodi tingati chofunika kwambiri n’chiyani kuti munthu akhale bambo wabwino? Funani malangizo kwa Yehova Mulungu, amene amadziwa kulera ana kuposa wina aliyense. Mukamaphunzitsa ana anu mogwirizana ndi malangizo a m’Mawu a Mulungu, mudzaona zimene lemba la Miyambo 22:6 limanena, zakuti: “Angakhale atakalamba sadzachokamo.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Ngakhale kuti malangizo a m’Malemba m’nkhani ino akukhudza makamaka udindo wa abambo, mfundo zake zambiri zingagwirenso ntchito kwa amayi.

^ ndime 18 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 25 Kuti mudziwe zambiri za mmene mungatetezere ana anu kwa anthu omwe angawachite zachipongwe, onani Galamukani! ya October 2007, tsamba 3 mpaka 11, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 19]

Bambo azipereka chitsanzo chabwino kwa ana ake

[Chithunzi patsamba 20]

Bambo azithandiza ana ake mwauzimu

[Chithunzi patsamba 21]

Bambo azilangiza ndi kulanga ana ake mwachikondi