Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Linaneneratu Zimene Zichitike Posachedwapa

Linaneneratu Zimene Zichitike Posachedwapa

 Linaneneratu Zimene Zichitike Posachedwapa

PONENA za tsogolo la anthu ndiponso la dzikoli, mtumwi Petulo analemba kuti: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake [la Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Lonjezo lakuti padzakhala “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” linali litaperekedwa kale kudzera mwa mneneri Yesaya. (Yesaya 65:17; 66:22) Ponena ulosi umenewu, Petulo  anasonyeza kuti panthawiyo unali usanakwaniritsidwe.

Ndiyeno m’chaka cha 96 C.E., masomphenya amene Yohane anaona anasonyeza kuti ‘m’dziko latsopanoli,’ Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ambiri. (Chivumbulutso 21:1-4) Masiku ano tikuona zinthu zimene Yesu komanso mtumwi Paulo ananena kuti zidzachitika padziko pano Ufumu wa Mulungu usanayambe kulamulira. Motero tiyenera kuyembekezera kuti posachedwapa Ufumuwo udzabweretsa dziko lapansi latsopano. Kodi dziko latsopano limeneli lidzakhala lotani? Buku la Yesaya limayankha funso limeneli.

Madalitso M’dziko Latsopano

Mtendere Padziko Lonse Ndiponso Kulambira Mogwirizana. “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:2-4.

Mtendere Pakati pa Anthu ndi Nyama. “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. . . . Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:6-9.

Chakudya Chokwanira Anthu Onse. “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.”​—Yesaya 25:6.

Imfa Sidzakhalaponso. “Iye [Mulungu] wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.”​—Yesaya 25:8.

Akufa Adzaukitsidwa. “Akufa anu adzakhala ndi moyo, mitembo yawo idzauka. Amene akugona m’nthaka adzadzuka ndi kufuula mosangalala . . . Anthu amene anafa kalekale adzabadwanso padziko lapansi.”​—Yesaya 26:19, The New English Bible.

Mesiya Adzaweruza Mwachilungamo. “Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera; koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka.”​—Yesaya 11:3, 4.

 Akhungu ndi Ogontha Adzachiritsidwa. “Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.”​—Yesaya 35:5.

Malo Opanda Chonde Adzakhala Achonde. “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba.”​—Yesaya 35:1, 2.

Dziko Lapansi Latsopano. “Ndilenga kumwamba kwatsopano [boma latsopano la kumwamba] ndi dziko lapansi latsopano [mtundu wa anthu olungama watsopano] ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ichi ndichilenga. . . . Iwo [anthu okhala m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza] adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku amtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo. Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.” “Monga m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.”​—Yesaya 65:17-25; 66:22.

Kuneneratu za Tsogolo Labwino Kwambiri

Sikuti ndi buku la Yesaya lokha limene limaneneratu za tsogolo labwino. Baibulo lili ndi maulosi osiyanasiyana ofotokoza zinthu zabwino kwambiri zimene Mulungu adzachite kudzera mu Ufumu wake, wolamuliridwa ndi Khristu. * Kodi inuyo mumafuna kudzakhala nawo m’paradaiso ameneyu? Ndiyetu yesetsani kudziwa zimene Baibulo limanena za cholinga cha Mulungu chokhudza tsogolo lathu. Komanso fufuzani zimene mungachite kuti mudzakhalepo panthawiyi. Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani kudziwa zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzachite, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? patsamba 76 mpaka 85.

[Chithunzi patsamba 8]

Anthu adzakhala ogwirizana ndipo padzakhalanso mtendere pakati pa anthu ndi nyama

[Chithunzi patsamba 9]

Akufa adzakhalanso ndi moyo

[Chithunzi patsamba 10]

Dziko lonse lidzakhala paradaiso