Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro Chinandithandiza Kupirira Mavuto

Chikhulupiriro Chinandithandiza Kupirira Mavuto

 Chikhulupiriro Chinandithandiza Kupirira Mavuto

Yosimbidwa ndi Soledad Castillo

Mwamuna wanga anamwalira ndili ndi zaka 34. Patangotha zaka 6, bambo anganso anamwalira. Nthawi zina ndikanatha kusokonezeka maganizo kwambiri chifukwa chotsala ndekha. Ndipotu bambowo atamwalira panangodutsa miyezi 8 kenako mwana wanga anapezeka ndi matenda osachiritsika. Komabe sindinataye mtima pa mavuto onsewa.

DZINA langa ndi Soledad ndipo limatanthauza kuti “Kalikokha.” Koma mungadabwe kumva kuti pamoyo wanga wonse sindinamvepo kuti ndatsala ndekha. Pamavuto onse amene ndakumana nawo ndinkakhulupirira kuti Yehova Mulungu anali nane ndipo ‘anagwira dzanja langa lamanja n’kundithandiza kuti ndisaope.’ (Yesaya 41:13) Talekani ndikuuzeni mavuto amene ndakumana nawo ndi mmene andithandizira kuyandikira Yehova.

Moyo Wopanda Mavuto Ambiri

Ndinabadwira mu mzinda wa Barcelona, m’dziko la Spain pa May 3, 1961, ndipo m’banja mwathu ndilipo ndekha. Mayi anga dzina lawo ndi Soledad ndipo bambo anga anali a José. Ineyo ndili ndi zaka 9, mayi anga anaphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu. Iwo anali ndi mafunso ambiri okhudza Mawu a Mulungu koma tchalitchi chawo sichinawathandize kuyankha mafunsowo. Tsiku lina anthu awiri a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu ndipo pogwiritsira ntchito Baibulo, anayankha mafunso onse amene mayi anali nawo. Choncho anavomereza kuti anthuwo aziwaphunzitsa Baibulo.

Posakhalitsa mayi anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Patapita zaka zingapo nawonso bambo anawatsatira. Munthu yemwe ankaphunzira ndi mayi anga anali Eliana ndipo sizinam’tengere nthawi kuona kuti inenso ndili ndi chidwi chofuna kudziwa Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, Eliana ananena kuti ndi bwino kuti azindiphunzitsa Baibulo pandekha. Iyeyo anandithandiza ndipo mayi anga anandilimbikitsa moti ndinabatizidwa ndili ndi zaka 13.

Ndili mtsikana, nthawi zonse ndinkapemphera kwa Yehova ndikafuna kusankha zochita. Kunena zoona panthawiyo ndinalibe mavuto ambiri. Ndinali ndi anzanga ambirimbiri mumpingo komanso ndinkagwirizana kwambiri ndi makolo anga. Mu 1982, ndinakwatiwa ndi mnyamata wa Mboni za Yehova dzina lake Felipe. Iye anali ndi zolinga zotumikira Yehova zofanana ndi zanga.

Kuphunzitsa Mwana Wathu Kukonda Yehova

Patapita zaka zisanu ndinabereka mwana wamwamuna wokongola ndipo tinam’patsa dzina lakuti Saúl. Mwanayu atabadwa ine ndi Felipe tinasangalala kwambiri. Tinkafuna kum’samalira bwino kwambiri kuti akhale wathanzi komanso wokonda Mulungu. Motero nthawi zonse tinkamuphunzitsa  za Yehova, kudyera naye limodzi, kupita naye kumalo osiyanasiyana okongola, ndiponso kusewera naye. Saúl ankakonda kuyenda ndi Felipe pokauza ena choonadi ndipo anamuyambitsa msanga ntchito yolalikira. Anamuphunzitsa kugogoda m’makomo ndi kugawira timapepala tofotokoza Baibulo.

Mwanayu anapindula kwambiri ndi chikondi chimene tinkamusonyeza ndiponso zimene tinkamuphunzitsa moti mmene amakwanitsa zaka 6 n’kuti atayamba kale kulalikira nafe limodzi nthawi zonse. Iye ankakonda kumvetsera nkhani za m’Baibulo ndipo ankasangalala kwambiri tikamaphunzira limodzi Baibulo monga banja. Atangoyamba kupita ku sukulu, ankachita zinthu mwanzeru pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo zimene anaphunzira.

Koma mwana wathuyu atakwanitsa zaka 7, zinthu zinasintha kwambiri m’banja lathu. Mwamuna wanga anadwala matenda enaake a m’mapapo. Kwa miyezi 11, nthawi zambiri iye ankakhala chigonere ndipo sankathanso kugwira ntchito. Kenako anamwalira ali ndi zaka 36.

Mpaka pano ndimalirabe ndikakumbukira chaka chovuta chimenechi. Ndimakumbukira mmene iye ankavutikira ndi matendawo koma palibe chimene ndikanachita kuti ndim’pulumutse. Panthawi yonseyi ndinkayesetsa kumulimbikitsa ngakhale kuti mumtimamu ndinkadandaula kwambiri podziwa kuti tsogolo langa lasokonezeka basi. Ndinkamuwerengera nkhani zofotokoza Baibulo ndipo zimenezi zinkatilimbikitsa panthawi imene tinkalephera kupita ku misonkhano yachikhristu. N’zovuta kufotokoza mmene imfa yake inandikhudzira.

Komabe Yehova anali nane. Nthawi zonse ndinkamupempha kuti andipatse mzimu wake. Ndinkamuthokozanso kuti ine ndi Felipe tinali osangalala zaka zonse zimene tinali limodzi ndiponso kuti ndili ndi chiyembekezo chodzamuonanso akadzauka. Ndinkamupemphanso kuti andithandize kukhala wosangalala poganizira zabwino zonse zimene ine ndi mwamuna wanga tinachitira limodzi ndiponso kuti andipatse nzeru zolerera mwana wanga kuti adzakhale Mkhristu weniweni. Motero, ndinalimba mtima ngakhale kuti imfa imeneyi inandikhudza mosaneneka.

Makolo anga pamodzi ndi abale a mumpingo ankandithandiza kwambiri. Komabe ndinaona kuti unali udindo wanga kuphunzitsa Saúl Baibulo komanso kutumikira Yehova. Bwana wanga wakale anandipatsa ntchito ya muofesi. Koma ndinasankha kugwira ntchito yokolopa n’cholinga choti ndizipeza nthawi yosamalira bwino mwana wanga akaweruka kusukulu.

Pali lemba limodzi limene linandithandiza kwambiri kuzindikira kuti kuphunzitsa mwana wanga kukonda Mulungu n’kumene kuli kofunika kwambiri. Lembalo limati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Lembali linandithandiza kuona kuti ngati nditachita khama kuphunzitsa mwana wanga mfundo za m’Baibulo, Yehova angathe kudalitsa khama langalo. N’zoona kuti zimenezi zinachititsa kuti ndisamapeze ndalama zokwanira koma ndinaona kuti kusamalira mwana wanga n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi chuma.

Saúl ali ndi zaka 14, bambo anga anamwalira. Imfa yawo inam’khudza kwambiri chifukwa  inamukumbutsa za imfa ya bambo ake. Bambo anga anasonyezanso chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yokonda Yehova. Ndiye atamwalira, mwana wanga Saúl ananena kuti iyeyo ndiye avale zilimbe monga mwamuna m’banja lathu ndipo azisamalira mayi wakene ndiponso agogo ake aakazi.

Kulimbana ndi Khansa ya M’magazi

Patatha miyezi 8 bambo wanga atamwalira, dokotala anandiuza kuti ndim’pititse mwana wanga kuchipatala kuti akamuunike pofuna kudziwa chimene chinkachititsa kuti nthawi zonse azikhala wotopa kwambiri. Ndiye atamuunikaunika, anapeza kuti ali ndi khansa ya m’magazi. *

Motero, kwa zaka ziwiri ndi theka Saúl sankati wagonekedwa liti m’chipatala chifukwa cha matendawa komanso mavuto obwera chifukwa cha mankhwala ake. Atalandira chithandizo kwa miyezi 6 yoyambirira anakhala bwino ndithu kwa chaka chimodzi ndi theka. Koma khansayo inayambiranso ndipo anam’patsanso mankhwala ena amene anam’fooketsa kwambiri. Atangokhala kwa nthawi yochepa, khansayo inayambiranso koma Saúl analephera kupitiriza kulandira mankhwala aja chifukwa ankamufoola kwambiri. Panthawiyi n’kuti iye atadzipereka kwa Mulungu ndipo anali atanena kale kuti akufuna kubatizidwa kuti akhale wa Mboni za Yehova, koma atangokwanitsa zaka 17 anamwalira.

Nthawi zambiri madokotala amati ndi bwino kuti munthu akamalandira chithandizo cha matenda a khansa aziikidwa magazi. Komatu kuikidwa magazi sikuchiritsa matendawa ayi. Mmene madokotalawo ankatiuza kuti Saúl amupeza ndi matenda a khansa, ineyo ndi Saúl tinawauza momveka bwino kuti sitingalole chithandizo chimenechi chifukwa timamvera lamulo la Yehova lakuti ‘tipewe magazi.’ (Machitidwe 15:19, 20) Nthawi zingapo Saúl ankakambirana ndi madokotalawo ali yekhayekha powauza kuti wachita kusankha yekha kukana kulandira magazi. (Onani bokosi patsamba 31.)

Mpaka madokotalawo anafika poona kuti iye anali ndi nzeru za munthu wamkulu ndipo ankadziwa bwino kuopsa kwa matenda ake. Chifukwa cha zimenezi, madokotalawo anavomereza kusamuika magazi ndipo anam’patsa chithandizo china. Komabe panthawi yonseyi, ambiri sanasiye kutiuza kuti tisinthe maganizo athu. Ndinanyadira kwambiri kuona mwana wanga akufotokozera madokotala za chikhulupiriro chake pankhaniyi. Zinali zoonekeratu kuti iye anali paubwenzi wolimba ndi Yehova.

Pamsonkhano wachigawo, womwe unachitikira ku Barcelona panatulutsidwa buku la kuti Yandikirani kwa Yehova. Zimenezi zinachitika Saúl atangopezeka ndi matendawa. Buku labwino kwambiri limeneli linatithandiza kuti tisataye mtima kwambiri poganizira mavuto amene tikumane nawo m’tsogolo. Saúl akagonekedwa m’chipatala, tinkawerengera limodzi bukuli. Ndiye pambuyo pake tinkakumbutsana zimene tinawerengazo kuti tipirire mavuto amene tinali kukumana nawo. Apa m’pamene mawu a pa Yesaya 41:13, omwe anatchulidwa m’mawu oyamba a bukuli anatithandiza kwambiri. Mawu ake ndi akuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usawope ndidzakuthandiza iwe.”

Chikhulupiriro Chake Chinalimbikitsa Ena

Saúl anagometsa kwambiri madokotala ndi manesi a pa chipatala cha Vall d’Hebrón chifukwa choti anali ndi nzeru za munthu wamkulu komanso anali wolimba mtima. Anthu onse amene ankamusamalira kuchipatalako ankamukonda kwambiri. Mwachitsanzo, kuchokera panthawiyi, dokotala wamkulu wa khansa ya m’magazi wakhala akuthandiza bwino kwambiri ana ena a Mboni za Yehova amene akudwala matenda amenewa ndipo amamvera zofuna zawo. Iye amakumbukira kuti Saúl sanafune kusintha chikhulupiriro chake ndipo sankaopa imfa moti nthawi  zonse ankayesetsa kukhala wosangalala. Gulu la manesi amene ankamusamalira anamuuza kuti sanasamalirepo wodwala wosavuta ngati iyeyo. Anam’yamikira kwambiri chifukwa akuti sankakonda kudandaula, m’malo mwake anali munthu wokonda kuseka, ngakhale pamene anatsala pang’ono kumwalira.

Dokotala wina anandiuza kuti ana ambiri akadwala matenda oti afa nawo amavutitsa kwambiri madokotala ndiponso makolo awo chifukwa cha ululu komanso kutaya mtima. Saúl sanachite zimenezi, ndipo dokotalayu ananena kuti anadabwa kwambiri kumuona ali phee, osasonyeza kuti akuda nkhawa. Pamenepa, ine ndi Saúl tinapezerapo mwayi womulalikira dokotalayo.

Ndikukumbukiranso kuti Saúl anathandiza m’bale wina mumpingo wathu. M’baleyo anakhala akudwala matenda a maganizo kwa zaka 6, ndipo achipatala anakanika kuthetseratu vuto lakelo. M’bale ameneyu anabwerapo nthawi zingapo kuchipatala kudzam’samalira Saúl usiku wonse. Ndiye anandiuza kuti anagoma kwambiri kuona kulimba mtima kwa Saúl. Anaona kuti ngakhale kuti matendawa anam’foola, Saúl ankayesetsa kulimbikitsa aliyense amene anabwera kudzamuona. M’baleyu anati: “Chitsanzo cha Saúl chandithandiza kulimbana ndi matenda anga a maganizo.”

Tsopano patha zaka zitatu Saúl atamwalira koma imfa yake imandipwetekabe mpaka pano. Inde, ndine wofooka koma Mulungu wandipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akorinto 4:7) Ndaphunzirapo kuti ngakhale vuto litakula bwanji pali chinachake chimene munthu ungaphunzirepo. Kupirira imfa ya mwamuna wanga, bambo anga, ndi mwana wanga kwandithandiza kukhala munthu wosadzikonda komanso womvetsa mavuto a ena. Koma chachikulu n’chakuti kwandithandiza kuyandikira kwambiri Yehova. Ndimalimba mtima kwambiri poganizira zam’tsogolo chifukwa Atate wanga wakumwamba amandithandiza. Iye amandigwirabe dzanja.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Imeneyi ndi khansa yoopsa yomwe imawononga maselo oyera a m’magazi.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 31]

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

N’kutheka kuti munamvapo kuti Amboni za Yehova salola kuikidwa magazi. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani?

Anthu ambiri samvetsa mmene Mboni za Yehova zimaonera lamulo la m’Malemba lopewa magazi. Anthu ena amaganiza kuti Amboni za Yehova amakana mankhwala alionse ndipo ena amati salemekeza moyo. Zimenezi si zoona ngakhale pang’ono. Amboni za Yehova amafuna kuti iwowo komanso mabanja awo azilandira chithandizo chamankhwala chabwino kwambiri chimene angapeze. Koma amafuna kuti chithandizocho chisakhale chokhudza kulandira magazi. N’chifukwa chiyani safuna chithandizo chotere?

N’chifukwa choti amamvera lamulo lofunika limene Mulungu anapereka kwa anthu. Chigumula cha Nowa chitangochitika, Mulungu anauza Nowa ndi banja lake kuti angathe kuyamba kudya nyama. Koma anawaletsa chinthu chimodzi. Chinthu chake chinali chakuti asamadye magazi. (Genesis 9:3, 4) Anthu a mitundu yonse anachokera kwa Nowa, motero lamulo limeneli limagwira ntchito kwa anthu a mafuko onse. Silinathe ayi. Patatha zaka 800, Mulungu anabwerezanso lamulo limeneli kwa mtundu wa Isiraeli ndipo anawalongosolera kuti magazi ndi opatulika, chifukwa choti amaimira moyo wa chinthucho. (Levitiko 17:14) Kenaka, patatha zaka zoposa 1,500, atumwi achikhristu analamula Akhristu onse kuti ‘apitirize kupewa magazi.’​—Machitidwe 15:29

Mboni za Yehova zimaona kuti n’zosatheka kunena kuti tikupewa magazi ngati timalola kuikidwa magazi tikadwala. N’chifukwa chake zimafuna kulandira chithandizo popanda kuikidwa magazi. Ndipotu nthawi zambiri iwo amalandira chithandizo chabwino kwambiri chifukwa chotsatira lamulo la m’Malemba limeneli. N’zosakayikitsa kuti izi n’zimene zimachititsa kuti anthu ambiri amene si Amboni za Yehova azifunanso kulandira chithandizo popanda kuikidwa magazi.

[Chithunzi patsamba 29]

Ine, mwamuna wanga Felipe, ndi mwana wathu Saúl

[Chithunzi patsamba 29]

Makolo anga, José ndi Soledad

[Chithunzi patsamba 30]

Mwana wanga Saúl kutangotsala mwezi umodzi kuti amwalire