Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizani Osochera Kubwerera M’gulu la Nkhosa

Thandizani Osochera Kubwerera M’gulu la Nkhosa

Thandizani Osochera Kubwerera M’gulu la Nkhosa

“Sangalalani nane pamodzi, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inatayika ija.”​—LUKA 15:6.

1. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi m’busa wachikondi?

MWANA wa Yehova wobadwa yekha, Yesu Khristu, amatchedwa “m’busa wa nkhosa wamkuluyo.” (Aheb. 13:20) Maulosi a m’Baibulo anali ataneneratu zoti kudzabwera m’busa wapadera ndiponso kuti adzayesetsa kufunafuna “nkhosa zotayika” za Isiraeli. (Mat. 2:1-6; 15:24) Mofanana ndi m’busa weniweni, Yesu analolera kufera nkhosa zake, kapena kuti anthu okhala ngati nkhosa, amene amakhulupirira nsembe ya dipo imene Iye anapereka.​—Yoh. 10: 11, 15; 1 Yoh. 2:1, 2.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu ena anabwerera m’mbuyo?

2 Koma n’zomvetsa chisoni kuti ena mwa anthu amene ankaoneka kuti akukhulupirira nsembe ya Yesu mpaka kufika podzipereka kwa Mulungu, anasiya kusonkhana ndi mpingo wachikhristu. N’kutheka kuti iwowa anabwerera m’mbuyo, mwina chifukwa chokhumudwa, matenda, kapena zifukwa zina. Komabe, angapeze chimwemwe chimene Davide anafotokoza mu Salmo 23 ngati atabwereranso m’gulu la nkhosa la Mulungu. Mwachitsanzo iye anati: “Yehova ndiye m’busa wanga; sindidzasowa.” (Sal. 23:1) Anthu amene ali m’gulu la nkhosa la Mulungu, sasowa chilichonse mwauzimu, koma nkhosa zimene zasochera zimavutika kwambiri. Kodi ndani angathandize nkhosazi? Nanga angazithandize bwanji? Kodi n’chiyani makamaka chimene tingachite pothandiza anthu amenewa kuti abwerere m’gulu la nkhosa?

Kodi Ndani Angawathandize?

3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji zoyenera kuchita kuti tipulumutse nkhosa zosochera za m’khola la Mulungu?

3 Kupulumutsa nkhosa zosochera za m’khola la Mulungu kumafuna khama. (Sal. 100:3) Pofuna kuti anthu amvetse mfundo imeneyi, Yesu anapereka chitsanzo chakuti: “Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? Ndipo akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi 99 zosasochera zija. Mofananamo Atate wanga wa kumwamba sakufuna kuti mmodzi wa aang’ono awa akawonongeke.” (Mat. 18:12-14) Kodi ndani angathandize anthu onga nkhosa zosochera?

4, 5. Kodi akulu ayenera kuliona motani gulu la nkhosa za Mulungu?

4 Pothandiza nkhosa zosochera, akulu ayenera kukumbukira kuti, gulu la nkhosa la Mulungu kwenikweni ndi mpingo wa anthu amene adzipereka kwa Yehova. Motero iwo ndi ‘nkhosa za Mulungu’ zamtengo wapatali. (Sal. 79:13) Nkhosa zimenezi zimafunika kuzisamalira mwachikondi, choncho abusawo ayenera kuganizira nkhosa iliyonse payokha. Pochita maulendo aubusa olimbikitsa, iwo angathandize kwambiri nkhosazi. Kuthandiza nkhosazo mwachikondi kungazilimbikitse mwauzimu n’kuzipatsa mtima wofunitsitsa kubwerera m’gulu la nkhosa.​—1 Akor. 8:1.

5 Abusa a gulu la nkhosa za Mulungu ali ndi udindo wofufuza nkhosa zosochera n’kuzithandiza kuti zibwerere. Mtumwi Paulo anakumbutsa akulu a ku Efeso kuti asaiwale udindo wawo wa ubusa. Iye anati: “Mudziyang’anire nokha ndi gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake wa iye mwini.” (Mac. 20:28) Nayenso mtumwi Petulo analimbikitsa akulu odzozedwa kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse; osati mochita ufumu pa aja ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”​—1 Pet. 5:1-3.

6. N’chifukwa chiyani abusa ayenera kusamalira kwambiri nkhosa za Mulungu, makamaka masiku ano?

6 Abusa achikhristu ayenera kutengera chitsanzo cha Yesu, yemwe ndi “m’busa wabwino.” (Yoh. 10:11) Iye ankaganizira kwambiri nkhosa za Mulungu ndipo anasonyeza kuti kusamalira nkhosazi n’kofunika kwambiri. Anatero pomuuza Simoni Petulo kuti “weta tiana tankhosa tanga.” (Werengani Yohane 21:15-17.) Masiku ano nkhosa ziyenera kusamaliridwa bwino kwambiri chifukwa Mdyerekezi akuchita khama kwabasi pofuna kusokoneza anthu onse odzipereka kwa Mulungu, kuti asakhale okhulupirika. Satana amapezerapo mwayi pa zofooka zathu komanso amagwiritsira ntchito dzikoli pofuna kusocheretsa nkhosa za Yehova kuti zizichita zinthu zoipa. (1 Yoh. 2:15-17; 5:19) Anthu amene abwerera m’mbuyo ali pangozi yaikulu, motero ayenera kuthandizidwa kuti ayambenso kutsatira malangizo akuti ‘ayende mwa mzimu.’ (Agal. 5:16-21, 25) Kuti tithandize nkhosa zimenezi m’pofunika kupemphera kwambiri kuti Mulungu atithandize ndi kutitsogolera ndi mzimu woyera. M’pofunikanso kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu mwaluso.​—Miy. 3:5, 6; Luka 11:13; Aheb. 4:12.

7. Kodi n’chifukwa chiyani akulu ayenera kusamalira nkhosa zimene zaikidwa m’manja mwawo?

7 Kalelo, ku Isiraeli m’busa ankakhala ndi ndodo yaitali yokhota kumapeto, yomwe ankakusira nkhosa zake. Nkhosazo zikamalowa kapena kutuluka m’khola, ‘zinkadutsa pansi pa ndodoyo’ ndipo m’busayo ankaziwerenga. (Lev. 27:32; Mika 2:12; 7:14) Abusa achikhristu nawonso ayenera kudziwa bwino gulu la nkhosa za Mulungu n’kumaonetsetsa kuti nkhosa iliyonse ilipo ndipo ili bwino. (Yerekezerani ndi Miyambo 27:23.) N’chifukwa chake imodzi mwa nkhani zofunika kwambiri zimene mabungwe a akulu amakambirana ndiyo kuchita maulendo a ubusa. Pankhaniyi amakambirananso zimene angachite kuti athandize nkhosa zimene zasochera. Ngakhale Yehova ananena kuti amafufuza ndi kusamalira nkhosa zake. (Ezek. 34:11) Motero Mulungu amasangalala akulu akamachitanso zoterezi pofuna kuthandiza nkhosa zosochera, kubwerera ku gulu la nkhosa.

8. Tchulani zinthu zina zimene akulu angachite pothandiza nkhosa inayake.

8 M’bale kapena mlongo akadwala amasangalala ndi kulimbikitsidwa kwambiri akazondedwa ndi abusa a nkhosa za Mulungu. Umu ndi mmenenso nkhosa imene ikudwala mwauzimu imamvera. Akulu akapita kwa munthu amene wabwerera m’mbuyo angathe kuchita zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, angathe kumuwerengera malemba, kukambirana naye nkhani inayake ya m’magazini kapena mfundo zina zimene aphunzira kumisonkhano ndipo angathenso kupemphera naye. Iwo angamuuze kuti abale ndi alongo angasangalale kwambiri kumuona ku misonkhano yampingo. (2 Akor. 1:3-7; Yak. 5:13-15) Munthuyo angalimbikitsidwe kwambiri ngakhale kungom’chezera, kumuimbira foni kapena kumulembera kalata. Abusa achikhristu achifundo amasangalala kwambiri akathandiza mwakuthupi nkhosa zosochera.

Ndi Udindo wa Mpingo Wonse

9, 10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiyira akulu okha udindo wonse wosamalira nkhosa zimene zasochera?

9 Tikukhala m’nthawi yovuta kwambiri ndipo anthu ambiri ndi otanganidwa. Choncho n’zotheka kuti sitingathe kudziwa kuti m’bale wathu wayamba kubwerera m’mbuyo mwapang’onopang’ono. (Aheb. 2:1) Komatu Yehova amaona kuti nkhosa zake ndi zamtengo wapatali kwabasi. Aliyense mumpingo ali ngati chiwalo cha thupi la munthu ndipo ndi wofunika kwambiri. Choncho abale ndi alongo tonsefe tiyenera kumaganizirana komanso tizikondana ndi mtima wonse. (1 Akor. 12:25) Kodi inuyo mumachita zimenezi?

10 Ngakhale kuti akulu ndi amene amatsogolera pa ntchito yofufuza ndi kuthandiza nkhosa zimene zasochera, tonsefe tiyenera kudera nkhawa okhulupirira anzathu amene ayamba kusowa. Tonse tingathe kuthandiza abusawa polimbikitsa abale ndi alongo athu amene akufunika thandizo kuti abwerere m’gulu la nkhosa, ndipotu tisaganize kuti siife ololedwa kuchita zimenezi. Komano kodi tingazichite bwanji?

11, 12. Kodi ndi mwayi wotani umene mungapatsidwe pofuna kuthandiza anthu amene akufunika thandizo lauzimu?

11 Nthawi zina akulu angapemphe wofalitsa waluso kuti azichita phunziro la Baibulo ndi munthu wofooka amene wapempha thandizo. Amachita zimenezi pofuna kuthandiza munthuyo kuti akhalenso ndi ‘chikondi chimene anali nacho poyamba.’ (Chiv. 2:1, 4) Abale ndi alongo amenewa angalimbikitsidwe mwauzimu ngati mutakambirana nawo mfundo zina zimene zinakambidwa ku misonkhano imene akhala akuphonya.

12 Akulu akakupemphani kuti muziphunzira ndi m’bale kapena mlongo amene akufunika thandizo lauzimu, muzipempha Yehova kuti akutsogolereni ndi kudalitsa khama lanu. Tiyenera kutsatira malangizo akuti: “Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.” (Miy. 16:3) Ganizirani malemba ndiponso mfundo zolimbitsa chikhulupiriro zimene mungagwiritsire ntchito pokambirana ndi anthu amene akufunikira thandizo lauzimu. Ganiziraninso chitsanzo chabwino kwambiri chimene mtumwi Paulo anapereka. (Werengani Aroma 1:11, 12.) Paulo ankafunitsitsa kuona Akhristu a ku Roma n’cholinga choti awagawire mphatso yauzimu yowathandiza kuti akhale olimba. Iye ankadziwanso kuti akatero akawalimbikitsa ndipo iwonso akamulimbikitsa. Nafenso tizikhala ndi maganizo amenewa tikamathandiza nkhosa zimene zasochera m’gulu la Mulungu.

13. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungakambirane ndi munthu amene wabwerera m’mbuyo?

13 Mukamakambirana ndi anthu oterewa mungawafunse kuti: “Kodi munaphunzira bwanji choonadi?” Athandizeni kukumbukira mmene ankasangalalira kale powalimbikitsa kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo kumisonkhano yampingo, pa ntchito yolalikira komanso pamisonkhano yaikulu. Ngati munatumikirapo limodzi ndi munthuyo m’mbuyomo, m’kumbutseni zinthu zosangalatsa zimene munakumana nazo panthawiyo. Muuzeni mmene inuyo mukusangalalira chifukwa choyandikira Yehova. (Yak. 4:8) M’sonyezeni kuti mumayamikira Mulungu chifukwa chakuti amatisamalira anthu akefe makamaka potilimbikitsa ndi kutipatsa chiyembekezo tikakumana ndi mavuto.​—Aroma 15:4; 2 Akor. 1:3, 4.

14, 15. Kodi ndi madalitso ati amene mungakumbutse anthu amene abwerera m’mbuyo?

14 N’zosakayikitsa kuti kum’kumbutsa munthuyo madalitso amene ankapeza chifukwa chosonkhana mokhazikika ndi mpingo, kungamulimbikitse kwambiri. Mwachitsanzo, munthuyo ankapita patsogolo kwambiri pankhani yodziwa molondola Mawu a Mulungu komanso zolinga Zake. (Miy. 4:18) N’zodziwikiratu kuti zinali zosavuta kwa munthuyo kupewa mayesero panthawi imene ‘ankayenda mwa mzimu.’ (Agal. 5:22-26) Ndipo chikumbumtima choyera n’chimene chinkamuthandiza kupemphera kwa Yehova n’kumapeza ‘mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, womwe umateteza mitima yathu ndi maganizo athu.’ (Afil. 4:6, 7) Nthawi zonse mukamathandiza anthu ofooka muzikumbukira mfundo zimenezi. Asonyezeni chidwi chenicheni ndipo yesetsani mmene mungathere kulimbikitsa mwachikondi m’bale kapena mlongo wanuyo kuti abwerere m’gulu la nkhosa.​—Werengani Afilipi 2:4.

15 Ngati ndinu mkulu ndipo muli pa ulendo waubusa, mungathandize banja limene labwerera m’mbuyo, polikumbutsa nthawi imene linali litangophunzira choonadi cha Mawu a Mulungu. Panthawiyo banjalo linkaona kuti choonadi n’chosangalatsa, chosavuta kukhulupirira, chomveka bwino komanso chomasula munthu mwauzimu. (Yoh. 8:32) Ayenera kuti anasangalala kwambiri kuphunzira za Yehova, za chikondi chake ndiponso za cholinga chake. (Yerekezerani ndi Luka 24:32.) Akumbutseni kuti Akhristu amene anapereka moyo wawo kwa Mulungu amakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso amalankhula naye momasuka m’pemphero. Alimbikitseni kuti ayambenso kumvetsera mosamala “uthenga wabwino wa ulemerero wa Mulungu wa chisangalalo.”​—1 Tim. 1:11.

Musasiye Kuwasonyeza Chikondi

16. Perekani chitsanzo chotsimikizira kuti kulimbikitsa munthu amene wabwerera m’mbuyo kumathandizadi.

16 Kodi mfundo zimene tatchulazi n’zothandizadi? Inde. Mwachitsanzo wachinyamata wina anakhala wofalitsa Ufumu ali ndi zaka 12, koma pofika zaka 15 anabwerera m’mbuyo. Komano kenako anayambiranso kulimbikira ndipo wakhala muutumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 30. Iye anayambanso kulimbikira makamaka chifukwa chothandizidwa ndi mkulu wachikhristu. Iye anayamikira kwambiri thandizo limene mkuluyo anamupatsa.

17, 18. Kodi ndi makhalidwe ena ati amene mukufunika kukhala nawo kuti muthandize munthu amene wasochera, kubwerera m’gulu la nkhosa la Mulungu?

17 Chikondi n’chimene chimalimbikitsa Akhristu kuti athandize anthu ofooka, kubwerera mu mpingo. Polankhula ndi otsatira ake, Yesu anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:34, 35) Inde, chikondi ndi chizindikiro chosonyeza kuti ndife Akhristu enieni. Motero tiyenera kusonyeza chikondi chimenechi kwa Akhristu obatizidwa amene anabwerera m’mbuyo. Komabe kuti tithandize anthu oterewa tiyenera kukhala ndi makhalidwe enanso abwino.

18 Ndiyeno funso ndi lakuti, kodi ndi makhalidwe ena ati amene muyenera kukhala nawo kuti muthandize munthu amene wasochera, kuti abwerere m’gulu la nkhosa la Mulungu? Kuwonjezera pa chikondi, muyenera kusonyeza chifundo, kukoma mtima, kufatsa ndiponso kuleza mtima. Ngati munthuyo munali naye chifukwa, mungafunikenso kum’khululukira. Paulo analemba kuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso. Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.”​—Akol. 3:12-14.

19. Fotokozani chifukwa chimene tinganenere kuti mpake kuyesetsa kuthandiza nkhosa zimene zasochera kuti zibwerere m’khola lachikhristu.

19 Nkhani yotsatira ifotokoza zinthu zimene zimachititsa kuti anthu ena m’gulu la nkhosa la Mulungu asochere. Iyankhanso funso lakuti, kodi anthu amenewa ayenera kuyembekezera kudzalandiridwa motani? Pokumbukira mfundo zimene takambirana m’nkhani ino, komanso zimene tikambirane m’nkhani yotsatirayi, yesetsani kuchita chilichonse chimene mungathe kuti muthandize nkhosa zosochera, kubwerera m’khola lachikhristu. M’dongosolo lino la zinthu anthu ambiri amangokhalira kufunafuna chuma pa moyo wawo wonse. Koma dziwani kuti moyo wa munthu mmodzi ndi wamtengo wapatali kwambiri kuposa ndalama zonse zimene zili pa dziko lonse lapansi. Yesu anatsindika mfundo imeneyi m’fanizo la nkhosa yosochera. (Mat. 18:12-14) Muzikumbukira mfundo imeneyi pamene mukuyesetsa mwakhama komanso mwachangu kuthandiza nkhosa zosochera kuti zibwerere m’gulu. Anthu a Yehova amenewa ndi amtengo wapatali kwambiri kwa iye.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi abusa achikhristu ali ndi udindo wotani pankhani yothandiza anthu onga nkhosa zosochera kuti abwerere m’gulu la nkhosa la Mulungu?

• Kodi inuyo mungathandize bwanji anthu amene asiya kusonkhana ndi mpingo?

• Tchulani makhalidwe amene tiyenera kukhala nawo kuti tithandize anthu amene asochera, kubwerera m’gulu la nkhosa.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Abusa achikhristu amayesetsa mwachikondi kuthandiza anthu amene asochera kuti abwerere m’gulu la nkhosa la Mulungu