Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Titsatire Zinthu Zodzetsa Mtendere”

“Titsatire Zinthu Zodzetsa Mtendere”

 “Titsatire Zinthu Zodzetsa Mtendere”

MSEWU ukangokonzedwa kumene umaoneka wolimba kwambiri, ngati kuti sungawonongeke. Koma pakapita nthawi umayamba ming’alu ndi timayenje n’kufika poipa. Zikatere, pofuna kupewa ngozi ndiponso pofuna kuti usapitirire kuwonongeka, msewuwo umafunika kuukonza.

Umu ndi mmenenso zilili ndi ubwenzi wathu ndi ena. Tingati nawonso nthawi zina umatha kukhala ndi ming’alu mwinanso kufika poipa kumene. Mtumwi Paulo sanabise zoti panali kusamvana pakati pa Akhristu ena ku Roma. Iye analangiza Akhristu anzake kuti: “Tiyeni titsatire zinthu zodzetsa mtendere ndi zinthu zolimbikitsana wina ndi mnzake.” (Aroma 14:13, 19) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera ‘kutsatira zinthu zodzetsa mtendere’? Kodi tingalimbe mtima bwanji kuchita zimenezi?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mtendere?

Popanda kuchitapo kanthu, ming’alu ing’onoing’ono ya m’mphepete mwa msewu imatha kukula n’kukhala maenje ochititsa ngozi. Tingati umu ndi mmenenso zingakhalire tikapanda kuthetsa kusamvana pa nkhani zinazake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ngati wina anena kuti: ‘Ndimakonda Mulungu,’ koma amada m’bale wake, ndi wonama. Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Kulephera kuthetsa kusamvana pa nkhani inayake kungachititse kuti Mkhristu afike podana ndi m’bale wake?

Yesu Khristu anasonyeza kuti tikapanda kukhazikitsa mtendere ndi anzathu, Yehova sangakondwere kuti tizimulambira. Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Chotero ngati wabweretsa mphatso yako paguwa la nsembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.” (Mat. 5:23, 24) Motero, chifukwa chachikulu kwambiri chimene tiyenera kukhazikitsira mtendere n’chakuti timafuna kusangalatsa Yehova Mulungu. *

Nkhani ina imene inachitika mumpingo wa ku Filipi imatithandiza kuona chifukwa china chimene tiyenera kukhazikitsira mtendere. Alongo awiri achikhristu, Eodiya ndi Suntuke sanamvane pankhani inayake. Baibulo silitchula kuti anakangana pankhani yotani. Komabe, kusamvana kwawoko kukanatha kusokoneza mtendere wa  mpingo wonse. (Afil. 4:2, 3) Anthu akapanda kuthetsa nkhani mwamsanga, posakhalitsa nkhaniyo imatha kudziwika ndi aliyense. N’chifukwa chake pofuna kuti chikondi ndiponso mgwirizano upitirire mumpingo, timayesetsa kukhazikitsa mtendere mwamsanga ndi Akhristu anzathu.

Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene adzetsa mtendere.” (Mat. 5:9) Munthu wokonda mtendere amakhala wosangalala. Mtendere umathandizanso munthu kukhala wathanzi, chifukwa “mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miy. 14:30) Koma mtima wokonda kusungira ena zifukwa umachititsa kuti munthu azidwaladwala.

Monga Akhristu ambiri, n’zosakayikitsa kuti mumavomereza kuti ndi bwinodi kukhazikitsa mtendere, komabe mwina simungadziwe chochita ngati mwasiyana maganizo ndi winawake. Tiyeni tione mfundo za m’Malemba zimene zingatithandize pothetsa kusamvana.

Kukambirana Modekha Kumabwezeretsa Mtendere

Timing’alu ting’onoting’ono m’misewu tingathe kukonzedwa potikwirira bwinobwino. Nanga kodi ifeyo sitingathe kukwirira zinthu zambirimbiri zimene abale athu amatilakwira powakhululukira? Nthawi zambiri, njira imeneyi ingatithandize pothetsa kusamvana pakati pa ifeyo ndi abale athu, chifukwatu mtumwi Petulo analemba kuti “chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”​—1 Pet. 4:8.

Komabe nthawi zina tingaone kuti nkhaniyo ndi yaikulu kwambiri moti sitingathe kungoiiwala. Taganizirani zimene zinawachitikira Aisiraeli atangolowa kumene m’Dziko Lolonjezedwa. Asanawoloke mtsinje wa Yordano, “ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati” anamanga “guwa lalikulu mawonekedwe ake.” Mafuko ena a Isiraeli anaganiza kuti guwalo ankaligwiritsa ntchito polambira mafano moti anafuna kuchitapo kanthu, ndipo anakonza zokamenyana nawo.​—Yos. 22:9-12.

N’kutheka kuti iwo anaona kuti panali umboni wokwanira woti anzawowo akuchita zolakwa. Motero anakonza zoti akawagonjetse mowadzidzimutsa kuti adaniwo asakakule mphamvu n’kuwaphera asilikali ambiri. Koma mafuko a kumadzulo kwa Yordano sanachite zinthu mopupuluma, m’malomwake anatumiza nthumwi kuti zikakambirane kaye nkhaniyi ndi abale awowo. Iwo anafunsa kuti: “Cholakwa ichi n’chiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israyeli, ndi kum’tembenukira Yehova lerolino?” Komatu mafuko amene anamanga guwalo sankaligwiritsa ntchito pa kulambira mafano. Koma kodi iwo anayankha bwanji poimbidwa mlandu umenewu, womwe sunali woona n’komwe? Kodi anapsa mtima n’kuwakalipira kwambiri anzawowo kapena kodi anakana kulankhula nawo? Ayi, sanatero. M’malomwake mafukowo anayankha modekha, n’kufotokoza bwinobwino kuti anachita zimenezo ndi cholinga chotumikira Yehova. Mayankhidwe awowo anathandiza kuti asakhumudwitse Yehova komanso kuti pasafe munthu. Chifukwa chokambirana mitima ili m’malo nkhaniyo anaithetsa mwamtendere.​—Yos. 22:13-34.

 Aisiraeli enawo anasonyeza nzeru chifukwa sanafulumire kukamenyana ndi anzawowo asanakambirane nawo bwinobwino nkhaniyo. Mawu a Mulungu amati: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.” (Mlal. 7:9) Njira ya m’Malemba yothetsera kusamvana ndi ena pa nkhani zikuluzikulu ndiyo kulankhulana modekha ndiponso moona mtima. Kodi Yehova angatidalitse tikamakonda kusungira ena zifukwa popanda kuyesetsa kukambirana nawo nkhaniyo n’kuithetsa?

Komano tingatani Mkhristu mnzathu akabwera kudzatifunsa zinazake, mwinanso zoti sitinazichite n’komwe? Baibulo limati: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miy. 15:1) Aisiraeli amene ankaganiziridwa zoipa aja anafotokoza mbali yawo modekha, koma momveka bwino, n’chifukwa chake nkhani yovutayo inatha bwinobwino, popanda mapokoso. Ngati tapita kwa m’bale wathu kuti tikathetse nkhani inayake kapena iyeyo ndiye wabwera kwa ifeyo, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kuti pakhale mtendere, kodi m’pofunika kulankhula mawu otani, kuwalankhula motani, ndiponso kusonyeza mtima wotani?’

Gwiritsirani Ntchito Lilime Mwanzeru

Mwachibadwa anthufe timafuna kuti ena adziwe mmene tikumvera mumtima mwathu ndipo ngakhale Yehova amadziwa zimenezi. Motero tikalephera kuthetsa nkhani inayake, tingavutike kudzigwira pakamwa. Koma tiyenera kudziwa kuti tikayamba kuuza anthu ena nkhani yokhudza munthu amene tili naye chifukwa, m’posavuta kuyamba kunena zinthu zonyoza munthuyo. Lemba la Miyambo 11:11 limanena mawu otsatirawa, pankhani ya yogwiritsira ntchito lilime molakwika. Mawu ake ndi akuti: ‘M’kamwa mwa oipa mupasula mudzi.’ Mtendere wa mpingo ungathenso kuwonongeka tikamalankhula mosadziletsa za Mkhristu mnzathu.

Komabe, sikuti zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa kulankhula chilichonse chokhudza abale athu. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Osalola mawu alionse oipa kutuluka pakamwa panu.” Koma anawonjezera kuti: “Muzilankhula zabwino zokhazokha, zofunika kuti anthu amve, zinthu zimene zingawathandizedi. . . . Muzikomerana mtima, kuchitirana chifundo, ndiponso muzikhululukirana.” (Aef. 4:29-32, The New American Bible) Ngati m’bale wina amene anakhumudwa ndi zinazake zimene munanena kapena kuchita wakufikirani, kodi zingakhale zovuta kwa inuyo kumupepesa ngati mukudziwa kuti m’mbuyomo ananenapo zabwino za inuyo kwa ena? Zimenezitu zikusonyeza kuti kukonda kunena zabwino za Akhristu anzathu kungachititse kuti zikhale zosavuta kukhazikitsa mtendere ndi iwowo pakachitika nkhani zinazake.​—Luka 6:31.

Tumikirani Mulungu ‘ndi Mtima Umodzi’

Chifukwa cha uchimo, tikayambana ndi munthu sitifuna kuti tizionana naye, ndipo nthawi zina timadzipatula. Koma kuchita zimenezi n’kosathandiza. (Miy. 18:1) Poti ndife anthu ogwirizana, oitana pa dzina la Yehova, timayesetsa “kum’tumikira ndi mtima umodzi.”​—Zef. 3:9.

Tisasiye kulambira koona chifukwa cha zolankhula kapena zochita za ena. Taganizirani zimene zinachitika kutangotsala masiku ochepa kuti Yesu apereke nsembe yake imene inalowa m’malo mwa nsembe za ziweto zoperekedwa kukachisi. Iye anapita ku kachisi ndipo ali kumeneko anadzudzula alembi. Koma ataona mayi wamasiye wosauka akupereka ndalama “zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake,” sanam’letse. M’malomwake anamuyamikira chifukwa cha kukhulupirika kwake pothandiza mpingo wa Yehova wa panthawiyo. (Luka 21:1-4) Mayiyo anachirikiza kulambira Yehova ngakhale kuti panali anthu ena okonda kudyera anzawo masuku pamutu.

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngakhale titaona kuti m’bale kapena mlongo sanachite bwino, ndipo mwina watichenjerera? Kodi m’pomveka kuti tisiye kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse, chifukwa cha zimenezi? Kapena tingayesetse kuthetsa kusamvana kumene kulipo n’cholinga choti mumpingo wa Mulungu wa masiku ano mupitirizebe kukhala mtendere?

Malemba amatilangiza kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) Tiyeni titsimikize mtima kuchita zimenezi kuti tikhalebe pa njira yopita ku moyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Nkhani yofotokoza malangizo a Yesu pa Mateyo 18:15-17 ili mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999, tsamba 17 mpaka 22.

[Chithunzi patsamba 17]

Eodiya ndi Suntuke anafunikira kutsatira mtendere

[Chithunzi patsamba 18]

Kuti pakhale mtendere, kodi m’pofunika kulankhula mawu otani, kuwalankhula motani, ndiponso kusonyeza mtima wotani?