Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sankhani Kutumikira Yehova Mudakali Achinyamata

Sankhani Kutumikira Yehova Mudakali Achinyamata

Sankhani Kutumikira Yehova Mudakali Achinyamata

“Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira utakhutira nazo.”​—2 TIM. 3:14.

1. Kodi Yehova amauona bwanji utumiki wa Mboni zake zachinyamata?

UTUMIKI wopatulika umene achinyamata amachita ndi wofunika kwambiri kwa Yehova, motero kuti anauzira wamasalmo kulemba ulosi wokhudza achinyamata. Iye anati: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M’moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nawo mame a ubwana wanu.” (Sal. 110:3) Zoonadi, Yehova amaona kuti achinyamata amene amamutumikira ndi amtengo wapatali.

2. Kodi dzikoli limalimbikitsa achinyamata kuchita zotani pamoyo wawo?

2 Inu achinyamata a mumpingo wachikhristu, kodi mwadzipereka kwa Yehova? Achinyamata ambiri zimawavuta kuti asankhe kutumikira Mulungu. Anthu azamalonda, aphunzitsi, ndipo nthawi zinanso achibale ndi mabwenzi, amalimbikitsa achinyamata kufunafuna chuma. Achinyamata akakhala ndi zolinga zauzimu, anthu ambiri amawanyoza. Koma zoona zake n’zakuti palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kutumikira Mulungu woona. (Sal. 27:4) Taganizirani mafunso atatu awa: N’chifukwa chiyani muyenera kutumikira Mulungu? Mutakhala kuti mwadzipereka kwa Mulungu, kodi mungachite chiyani kuti zikuyendereni bwino pomutumikira ngakhale ngati anthu atamanena ndi kuchita zina ndi zina? Utumiki wopatulika umaphatikizapo ntchito zosiyanasiyana zimene munthu angachite. Kodi inu mungagwire ntchito iti?

Ndi Bwino Kutumikira Yehova

3. Kodi tiyenera kumva bwanji tikamaona chilengedwe cha Yehova?

3 N’chifukwa chiyani muyenera kutumikira Mulungu woona ndiponso wamoyo? Lemba la Chivumbulutso 4:11 limafotokoza chifukwa chake kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.” Yehova ndiye Mlengi wamkulu wa chilengedwe chonse. Dziko lapansili ndi lokongola kwabasi. Yehova anapanga zonse zimene zilimo monga, mitengo, maluwa, nyama, nyanja, mapiri ndi mathithi. Lemba la Salmo 104:24 limati: “Dziko lapansi lidzala nacho chuma [cha Mulungu].” Ndife othokoza kwambiri kuti Yehova watipatsa moyo umene umatichititsa kuti tizisangalala ndi dziko lapansi ndi zinthu zake. Kodi kuzindikira kwathu kuti iye ndiye analenga zinthu zodabwitsa zonsezi, sikuyenera kutipangitsa kuti tizimutumikira?

4, 5. Kodi Yehova anachita zotani zimene zinachititsa Yoswa kumuyandikira?

4 Chinthu china chimene chingatipangitse kutumikira Yehova ndi chimene Yoswa, mtsogoleri wa Aisiraeli ananena. Kumapeto kwa moyo wake, Yoswa anauza anthu a Mulungu kuti: “Mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.” N’chifukwa chiyani Yoswa ananena zimenezi?​—Yos. 23:14.

5 Yoswa anakulira ku Iguputo, ndipo ayenera kuti anadziwa zoti Yehova analonjeza Aisiraeli kuti adzawapatsa dziko lawolawo. (Gen. 12:7; 50:24, 25; Eks. 3:8) Kenako Yoswa anaona Yehova akukwaniritsa lonjezo lake mwa kubweretsa Miliri Khumi pa Aiguputo ndi kuchititsa Farao kulola Aisiraeli kupita. Yoswa anali m’gulu la anthu amene anapulumutsidwa pa Nyanja Yofiira, ndipo anaona Farao ndi gulu lake la nkhondo akumira. Paulendo wautali umene anayenda wodutsa “m’chipululu chachikulu ndi choopsacho” cha Sinai, Yoswa anaona Yehova akupatsa Aisiraeli zonse zimene anafunikira. Palibe ngakhale mmodzi amene anafa ndi njala kapena ludzu. (Deut. 8:3-5, 14-16; Yos. 24:5-7) Nthawi itafika kuti Aisiraeli agonjetse mitundu yamphamvu ya ku Kanani n’cholinga cholanda Dziko Lolonjezedwalo, Yoswa anaona Mulungu akumuthandiza iye pamodzi ndi Aisiraeli anzake pantchito yogonjetsa adani awo.​—Yos. 10:14, 42.

6. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu?

6 Yoswa anadziwa kuti Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza. N’chifukwa chake Yoswa ananena kuti: “Ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” (Yos. 24:15) Nanga bwanji inuyo? Mukaganizira malonjezo amene Mulungu woona wawakwaniritsa ndi enanso amene adzakwaniritse, kodi mumafuna kumutumikira ngati mmene Yoswa anachitira?

7. Kodi ubatizo wa m’madzi ndi wofunika chifukwa chiyani?

7 Kuganizira za chilengedwe cha Yehova ndiponso malonjezo ake osangalatsa ndi odalirika, kuyenera kukuchititsani kudzipereka kwa Yehova ndi kusonyeza kudziperekako pobatizidwa. Ubatizo ndi wofunika kwambiri ngati mukufuna kuyamba kutumikira Mulungu. Zimene anachita Yesu ndi chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Atangotsala pang’ono kuyamba ntchito yake monga Mesiya, Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi kuti am’batize. N’chifukwa chiyani Yesu anachita zimenezo? Yesu mwiniwake anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.” (Yoh. 6:38) Ubatizo wa Yesu unali chizindikiro chakuti waonekera kwa Atate wake kuti ayambe kuchita chifuniro Chake.​—Mat. 3:13-17.

8. N’Chifukwa chiyani Timoteyo anasankha kulambira Mulungu, ndipo n’chiyani chimene inuyo muyenera kuchita?

8 Taganizirani za Timoteyo, Mkhristu wachinyamata yemwe Yehova anam’patsa ntchito yambiri ndi utumiki wosiyanasiyana. N’chifukwa chiyani Timoteyo anasankha kulambira Mulungu woona? Baibulo limatiuza kuti ‘anaphunzira ndipo anakhulupirira atakhutira nazo.’ (2 Tim. 3:14) Ngati mwaphunzira Mawu a Mulungu ndipo mwakhulupirira kuti amanena zoona, ndiye kuti muli ngati Timoteyo. Tsopano muyenera kusankha zochita. Bwanji osawauza makolo anu zimene mukufuna kuchita? Mothandizana ndi akulu, iwo angakuuzeni mfundo za m’Malemba zimene zingakuthandizeni kuti muyenerere ubatizo.​—Werengani Machitidwe 8:12.

9. Kodi anthu ena angamve bwanji mutasankha kubatizidwa?

9 Kubatizidwa ndi chiyambi chabwino kwambiri potumikira Mulungu woona. Mukabatizidwa mumayamba mpikisano wothamanga umene mphoto yake ndi moyo wosatha komanso chimwemwe chimene mumapeza chifukwa chochita chifuniro cha Mulungu. (Aheb. 12:2, 3) Ndiponso mumasangalatsa abale anu amene ayamba kale mpikisano umenewu, komanso anzanu mumpingo wachikhristu. Koma koposa zonse, mumakondweretsa mtima wa Yehova. (Werengani Miyambo 23:15.) Ndi zoona kuti ena sangamvetse chifukwa chimene mwasankhira kulambira Yehova, ndipo angamanene kuti simunachite bwino. Mwinanso angakutsutseni. Koma mungathane ndi mavuto amenewa.

Ngati Ena Sakumvetsa Kapena Akukutsutsani

10, 11. (a) Kodi ndi mafunso otani amene anthu angafunse mutasankha kutumikira Mulungu? (b) Kodi mungaphunzire chiyani kwa Yesu pankhani yoyankha mafunso okhudza kulambira koona?

10 Anzanu a kusukulu, anthu a kumene mumakhala, ndi achibale sangamvetse chifukwa chimene mwasankhira kutumikira Yehova. Angakufunseni chifukwa chimene mwasankhira kuchita zimenezo ndipo angafune kudziwa zimene mumakhulupirira. Kodi mungawayankhe chiyani? Muyenera kuganiza mozama kuti mufotokoze bwino zosankha zanu. Pofotokozera anthu amenewa za chikhulupiriro chanu, mungachite bwino kutsatira chitsanzo cha Yesu.

11 Atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda atafunsa Yesu za kuuka kwa akufa, iye anawakumbutsa za lemba limene iwo sanaliganizire n’komwe. (Eks. 3:6; Mat. 22:23, 31-33) Pamene mlembi wina anafunsa Yesu kuti amuuze lamulo lalikulu, Yesu anangotchula malemba oyenerera a m’Baibulo. Munthuyo anayamikira Yesu chifukwa cha yankholo. (Lev. 19:18; Deut. 6:5; Maliko 12:28-34) Mmene Yesu ankagwiritsira ntchito Malemba ndi kalankhulidwe kake, zinachititsa kuti ‘khamu la anthulo ligawikane pankhani ya iye,’ ndipo adani akewo sanamuchite chilichonse. (Yoh. 7:32-46) Mukamayankha mafunso okhudza chikhulupiriro chanu, muzigwiritsa ntchito Baibulo ndipo muziyankha ‘ndi mtima wofatsa ndi ulemu waukulu.’ (1 Pet. 3:15) Ngati mwafunsidwa funso limene simukudziwa yankho lake, ndi bwino kunena kuti simukudziwa ndipo auzeni kuti mukafufuze kaye. Kenako mungakafufuze nkhaniyo mu Watch Tower Publications Index kapena mu Watchtower Library ngati ilipo mu chinenero chanu. Mutakonzekera bwino, ‘mungadziwe mmene mungayankhire.’​—Akol. 4:6.

12. Kodi n’chifukwa chiyani simuyenera kufooka ndi chizunzo?

12 N’zoona kuti anthu angakufunseni zimene mumakhulupirira ndi chifukwa chimene mwasankhira kutumikira Mulungu, koma si zokhazo. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wa Mulungu, ndiye akulamulira dziko. (Werengani 1 Yohane 5:19.) Musayembekezere kuti anthu onse angakulimbikitseni kapena kukuyamikirani, nthawi zina angakutsutseni. Anthu ena ‘angakunyozeni,’ ndipo angapitirizebe kuchita zimenezi. (1 Pet. 4:4) Koma kumbukirani kuti zimenezi sizikuchitikira inu nokha. Yesu Khristu nayenso anazunzidwa. Mtumwi Petulo anakumananso ndi zomwezi ndipo analemba kuti: “Okondedwa, musadabwe ndi moto [chizunzo] umene ukuyaka pakati panu, ngati kuti mukukumana ndi chinthu chachilendo. Motowo ukuyaka pofuna kukuyesani. Koma muzikondwera pamene mukugawana nawo masautso a Khristu.”​—1 Pet. 4:12, 13.

13. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusangalala akamazunzidwa?

13 Akhristu ayenera kusangalala akamapirira chizunzo kapena chitsutso. Chifukwa chiyani? Chifukwa ngati simukumana ndi zimenezi ndiye kuti mukuchita zinthu mogwirizana ndi dziko la Satanali osati ndi Mulungu. Yesu anachenjeza kuti: “Muli ndi tsoka, anthu onse akamanena zabwino za inu, pakuti zoterezi n’zimene makolo awo akale anachitira aneneri onyenga.” (Luka 6:26) Mukamazunzidwa ndiye kuti Satana ndi dziko lake sakusangalala nanu chifukwa chotumikira Yehova. (Werengani Mateyo 5:11, 12.) Ndipo ‘kunyozedwa chifukwa cha dzina la Khristu’ ndi chinthu chosangalatsa.​—1 Pet. 4:14.

14. Kodi ubwino wokhalabe wokhulupirika kwa Yehova pozunzidwa ndi wotani?

14 Mukakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale potsutsidwa, zotsatira zake zimakhala zabwino. Zina mwa zotsatirazo ndi izi: Choyamba, mumachitira umboni Mulungu ndi Mwana wake. Chachiwiri, kupirira kwanu kumalimbikitsa abale ndi alongo anu achikhristu. Chachitatu, anthu ena amene sadziwa Yehova angayambe kum’funafuna. (Werengani Afilipi 1:12-14.) Ndipo chachinayi, mumayamba kukonda kwambiri Yehova mukazindikira kuti akukupatsani mphamvu kuti mupirire ziyeso.

‘Khomo Lalikulu’ Lakutsegukirani

15. Kodi ndi ‘khomo lalikulu’ lotani limene linatsegukira mtumwi Paulo?

15 Ponena za utumiki wake ku Efeso, mtumwi Paulo analemba kuti: “Khomo la ntchito yaikulu landitsegukira.” (1 Akor. 16:8, 9) Limeneli linali khomo la ntchito yaikulu yolalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira mumzindawo. Mwa kulowa pa khomo limeneli, Paulo anathandiza anthu ambiri kuphunzira za Yehova ndi kuyamba kumulambira.

16. Kodi otsalira odzozedwa analowa bwanji ‘pa khomo limene linawatsegukira’ mu 1919?

16 Mu 1919, Yesu Khristu ‘anatsegulira khomo’ otsalira odzozedwa. (Chiv. 3:8) Iwo analowa pa khomo limeneli ndi kuyamba kulalikira uthenga wabwino ndiponso kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo mwakhama kuposa kale. Kodi zotsatira zake zakhala zotani? Uthenga wabwino wafika padziko lonse lapansi, ndipo anthu pafupifupi 7 miliyoni ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.

17. Kodi mungalowe bwanji pa “khomo la ntchito yaikulu”?

17 “Khomo la ntchito yaikulu” lili chitsegukire kwa atumiki onse a Yehova. Anthu amene amalowa pa khomo limeneli amasangalala chifukwa cha ntchito yaikulu yolalikira uthenga wabwino imene amagwira. Inu atumiki a Yehova achinyamata, kodi mumaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza ena ‘kukhulupirira uthenga wabwino’? (Maliko 1:14, 15) Kodi mwaganizapo zochita upainiya wokhazikika kapena wothandiza? Ambirinu mungathenso kugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, kutumikira pa Beteli, kapena kuchita umishonale. Popeza kuti dziko la Satana loipali latsala pang’ono kutha, kuchita utumiki umenewu wa Ufumu n’kofunika kwambiri kuposa kale. Kodi mulowa pa ‘khomo lalikulu’ limeneli pamene nthawi ilipobe?

“Talawani, Ndipo Onani Kuti Yehova Ndiye Wabwino”

18, 19. (a) Kodi ndi chiyani chinathandiza Davide kukhala wofunitsitsa kutumikira Yehova? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Davide sanadandaule chifukwa chosankha kutumikira Mulungu?

18 Mouziridwa, wamasalmo analimbikitsa ena kuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” (Sal. 34:8) Pamene Mfumu Davide ya Isiraeli inali m’busa wachinyamata, Yehova anaipulumutsa ku zilombo zolusa. Mulungu anathandiza Davide pomenyana ndi Goliati ndipo anam’pulumutsanso ku mavuto ena ambiri. (1 Sam. 17:32-51; Sal. 18, timawu tapamwamba) Chifukwa cha chikondi ndi kukoma mtima kwa Mulungu, Davide analemba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera inu.”​—Sal. 40:5.

19 Davide anayamba kukonda Yehova kwambiri ndipo ankafuna kum’tamanda ndi mtima ndiponso maganizo ake onse. (Werengani Salmo 40:8-10.) Ngakhale patapita zaka zambiri, Davide sanadandaule chifukwa chosankha kulambira Mulungu woona pamoyo wake. Kudzipereka kwa Mulungu kunali kofunika kwambiri kwa iye, ndipo kunam’patsa chimwemwe chosayerekezeka. Atakalamba, Davide anati: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu.” (Sal. 71:5, 18) Chidaliro chake mwa Yehova ndiponso ubwenzi wake ndi iye zinalimba, ngakhale kuti mphamvu zake zinali zitatha.

20. N’chifukwa chiyani kutumikira Mulungu ndi chinthu chabwino kwambiri chimene mungachite pamoyo wanu?

20 Moyo wa Yoswa, Davide ndi Timoteyo, ndi umboni wakuti kutumikira Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri chimene mungachite pamoyo wanu. Phindu la nthawi yochepa limene mungapeze m’dzikoli, silingafanane ndi phindu losatha limene mungapeze chifukwa ‘chotumikira Yehova ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.’ (Yos. 22:5) Ngati simunadziperekebe kwa Yehova mwa pemphero, mudzifunse kuti, ‘Kodi chikundiletsa n’chiyani kukhala wa Mboni za Yehova?’ Ngati ndinu wolambira Yehova ndipo munabatizidwa kale, kodi mukufuna kukhala ndi chimwemwe chowonjezereka? Ngati ndi choncho, wonjezerani utumiki wanu, ndipo pitani patsogolo mwauzimu. Nkhani yotsatira idzafotokoza mmene mungakulire mwauzimu potsatira chitsanzo cha mtumwi Paulo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Perekani zifukwa ziwiri zotipangitsa kutumikira Mulungu.

• Kodi n’chiyani chinathandiza Timoteyo kusankha kutumikira Mulungu?

• Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kupirirabe mukamazunzidwa?

• Kodi ndi utumiki wotani umene ungakutsegukireni?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kutumikira Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri pamoyo

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi mungayankhe mafunso okhudza chikhulupiriro chanu?