Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa

Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa

 Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa

ADAMU ndi Hava ali m’Paradaiso, Mulungu anawalamula kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”​—Genesis 1:28.

Kugonjetsa dziko lapansi sikuti kunangotanthauza kulima kapena kusamalira kadera kakang’ono chabe ka dzikoli ayi. Adamu ndi Hava limodzi ndi ana awo anafunika kukulitsa Paradaiso mpaka kufika padziko lonse lapansi. Komabe, anthu awiri oyambirirawa anachimwa ndipo anatulutsidwa m’munda wa Edene. (Genesis 3:23, 24) Komatu izi sizinatanthauze kuti dziko lapansi silidzagonjetsedwa ayi.

Mulungu adzadalitsa anthu omvera, motero iwo adzagonjetsa dziko lapansi. Mulungu atadalitsa anthu a mu Israyeli wakale, minda yawo ndiponso mitengo yawo ya zipatso inali kubereka bwino kwambiri. Umu ndi mmenenso zinthu zidzakhalire dziko lathuli likamadzasintha pang’onopang’ono n’kukhala paradaiso. Mogwirizana ndi lonjezo la m’Mawu ouziridwa a Mulungu, omwe ndi Baibulo, ‘dziko lapansi lidzapereka zipatso  zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.’ (Salmo 67:6) Zikadzatero, madambo a dziko lapansili ndiponso mapiri, mitengo ndi maluwa, limodzinso ndi mitsinje ndi nyanja zidzasangalala. (Salmo 96:11-13; 98:7-9) Dziko lathuli lidzadzaza ndi zomera zosangalala, mbalame ndi nyama zokongola, ndiponso anthu abwino.

Dziko Latsopano Layandikira

Tsopano tatsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano limene Yehova Mulungu analonjeza. “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano,” analemba motero mtumwi Petro, “m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Anthu ena atawerenga mawu a Petro amenewa, anganene kuti dzikoli silidzakhala paradaiso. Mwina angaganize kuti miyamba ndi dziko limene timaonali zidzalowedwa m’malo ndi zina. Kodi ndi momwemo?

Kodi “miyamba yatsopano” n’chiyani? Sikuti ndi miyamba yomwe timaonayi, imene inalengedwa ndi Mulungu, ayi. (Salmo 19:1, 2) Asananene mawu amenewa Petro anali atangonena kumene za “miyamba” yophiphiritsa, yomwe ndi maboma a anthu amene ali ndi mphamvu pa anthu awo. (2 Petro 3:10-12) “Miyamba” imeneyi yalephera kuwalamulira bwino anthu ndipo ikupita. (Yeremiya 10:23; Danieli 2:44) “Miyamba yatsopano” yomwe idzalowe m’malo mwa miyamba imeneyi ndi Ufumu wa Mulungu, wolamulidwa ndi Mfumu Yesu Kristu ndi olamulira anzake a 144,000 oukitsidwa kukakhala kumwamba.​—Aroma 8:16, 17; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.

Pamene Petro anatchula za “dziko latsopano” sikuti anali kuganiza za dziko lina losiyana ndi limene timakhalapoli ayi. Yehova anakonza dzikoli moyenerana ndi kuti anthu akhalepo kwamuyaya. (Salmo 104:5) Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko lapansi” ponena za anthu. (Genesis 11:1) Dziko limene lidzawonongedwe posachedwapa ndi anthu omwe ali mbali ya dziko loipali. Zikufanana ndi zimene zinachitika pamene dziko lapansi la anthu osapembedza linawonongedwa ndi Chigumula m’masiku a Nowa. (2 Petro 3:5-7) Ndiyeno kodi “dziko latsopano” ndi chiyani? Ili ndi gulu la anthu amakhalidwe atsopano, olambira Mulungu oona, “oongoka mumtima mwawo.” (Salmo 125:4; 1 Yohane 2:17) Malamulo onse a ‘m’dziko latsopano’ adzachokera ku “miyamba yatsopano.” Amuna okhulupirika padziko lapansi pano adzaonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa.

Zinthu Zatsopano ndi Zosangalatsa

Kunena zoona Yehova anatipatsa malo abwino oti tikhalemo pamene anakonza dziko lapansili moti lizitha kuchirikiza moyo. Iye ananena yekha kuti ntchito yomwe anagwira pokonza dziko lapansi inali ‘yabwino ndithu.’ (Genesis 1:31) Satana Mdyerekezi anachititsa kuti Adamu ndi Hava apanduke. (Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9) Koma posachedwapa, Mulungu adzaonetsetsa kuti anthu olungama ali ndi “moyo weniweniwo.” Izi zikutanthauza “moyo wosatha” m’Paradaiso wangwiro. (1 Timoteo 6:12, 19) Tsopano tiyeni tione ena mwa madalitso amene anthu adzapeze nthawi imeneyo.

Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, Satana adzamangidwa ndipo sadzatha kubweretsera anthu mavuto. Mtumwi Yohane anati: “Ndinaona mngelo [mkulu wa angelo Mikayeli, kapena kuti Yesu Kristu] anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi, nam’ponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:1-3; 12:12) Kuwonjezera pa kumasulidwa ku zochita za Satana panthawi yomwe  iye adzakhale atamangidwa, anthu adzapezanso madalitso ena ambiri Ufumu umenewu ukadzayamba kulamulira dziko.

Sikudzakhalanso kuipa, ziwawa, ndi nkhondo. Baibulo limalonjeza kuti: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:10, 11, 29) Yehova Mulungu ‘adzaletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.’ (Salmo 46:9) Ilitu ndi lonjezo losangalatsa loti kudzakhala chitetezo ndi mtendere!

Kudzakhala chakudya chochuluka, chopatsa thanzi ndiponso chokoma. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri,” anaimba motero wamasalmo. (Salmo 72:16) Nthawi imeneyi kulibe amene adzazunzike ndi njala.

Sipadzapezeka munthu wodwala. Inde, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Yesu Kristu ali padziko lapansi pano, anachiritsa akhate, opuwala ndi akhungu. (Mateyu 9:35; Marko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Ndiye taganizirani zomwe adzachite m’dziko lapansi latsopano! Taganizirani za chisangalalo chomwe chidzakhalepo ogontha, opuwala, ndiponso osalankhula akadzachiritsidwa.

Anthu omvera akamadzakhala angwiro, sikudzakhalanso mavuto a ukalamba. Sikudzakhalanso magalasi a maso, ndodo zoyendera, njinga za olumala, zipatala, ndiponso mankhwala. Zinthu zidzasintha kwambiri tikadzabwerera ku unyamata wathu! (Yobu 33:25) Podzuka m’mawa uliwonse, tizidzakhala titapuma mokwanira ndiponso okonzeka kugwira ntchito zosangalatsa.

Tidzasangalala ndi kuuka kwa akufa amene tinali kuwakonda ndiponso anthu ena. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kulandira Abele, Nowa, Abrahamu, Sara, Yobu, Mose, Rute, Davide, Eliya, Estere, ndi ena ambiri! Anthu enanso mamiliyoni ambirimbiri adzaukitsidwa kwa akufa. Ambiri mwa anthu amenewo sanaphunzirepo za Yehova, koma adzalandiridwa ndi anthu okonzeka kuwaphunzitsa za Mulungu, zolinga zake, ndiponso zokhudza Mwana wake, Yesu Kristu. Oukitsidwawo akadzayamba kudziwa Mlengi wawo, dziko lapansi lidzadzazadi ndi anthu odziwa Yehova.

Koposa zonse, tidzatha kulambira Mulungu woona yekha kwamuyaya. Tidzakhala ndi mwayi ‘wotumikira Yehova ndi chikondwerero,’ ndipo tizidzagwira limodzi ntchito pamene tikumanga nyumba zokongola, kulima mbewu, ndipo m’kupita kwa nthawi kugonjetsa dziko lonse lapansi. (Salmo 100:1-3; Yesaya 65:21-24) Kunena zoona, zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala kwamuyaya m’paradaiso wopindulitsa, wamtendere, ndiponso wokongola amene adzapangitse kuti dzina loyera la Yehova lilemekezedwe.​—Salmo 145:21; Yohane 17:3.

Anthu Adzayesedwa Komaliza

Mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000, Yesu adzagwiritsa ntchito phindu la nsembe yake ya dipo kwa munthu aliyense womvera. Motero, m’kupita kwa nthawi, uchimo wonse udzachotsedwa, ndipo anthu adzafika pokhala angwiro. (1 Yohane 2:2; Chivumbulutso 21:1-4) Popeza sikudzakhalanso uchimo wa Adamu ndi mavuto ake, anthu angwiro adzatha kutsatira bwinobwino miyezo ya Mulungu mwakuthupi, mwamaganizo, mwamakhalidwe, ndiponso mwauzimu. Motero ‘adzakhala ndi moyo’ weniweni akadzakhaliratu angwiro, opanda uchimo.  (Chivumbulutso 20:5) Zimenezi komanso dziko la Paradaiso zidzapangitsa kuti Yehova alemekezedwe.

Kwa nthawi yochepa, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu utatha, Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake, kapena kuti angelo oipa, adzamasulidwa m’phompho limene adzakhalemo zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:1-3) Adzaloledwa kuti ayese anthu ndi kuwapatutsa kuchoka kwa Mulungu. Ngakhale kuti anthu ena adzagonjera zilakolako zoipa, kupanduka kumeneku sikudzapita patali. Yehova adzapha anthu adyera amenewo limodzi ndi Satana ndiponso ziwanda zake. Zikadzatero sikudzakhalanso kuipa. Anthu onse ochita zoipa sadzakhalakonso, ndipo olungama adzalandira moyo wosatha.​—Chivumbulutso 20:7-10.

Kodi Mudzakhalako?

Anthu okonda Yehova Mulungu akuyembekezera tsogolo lamuyaya ndi lachimwemwe. M’moyo wosatha m’Paradaiso, chinthu chilichonse chidzakhala chosangalatsa. Ndipotu moyo uzidzakhala wosangalatsa kwambiri m’kupita kwa nthawi, chifukwa chakuti kuphunzira za Yehova Mulungu kulibe malire. (Aroma 11:33) Nthawi iliyonse mudzakhala ndi kenakake katsopano koti muphunzire, ndipo mudzakhala ndi nthawi yambirimbiri yochitira zimenezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti simudzakhala zaka 70 kapena 80 zokha, koma kwamuyaya.​—Salmo 22:26; 90:10; Mlaliki 3:11.

Ngati mumakonda Mulungu, mudzakhala wosangalala nthawi zonse kuchita chifuniro chake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Motero, musalole chilichonse kukulepheretsani kukondweretsa Yehova Mulungu mwa kuchita zolungama. Muzikumbukira chiyembekezo chosangalatsa chomwe timapeza m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Khalani ndi mtima wofuna kuchita chifuniro cha Yehova, ndipo musasiye kuchita zimenezo. Mukatero, mudzakhalako pamene cholinga cha Mulungu pa dziko lapansili chidzakwaniritsidwe, dziko lathuli n’kukhala paradaiso kwamuyaya.

[Chithunzi patsamba 4]

Minda ya ku Israyeli inkabereka bwino chifukwa cha madalitso a Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi inu mukuyembekezera madalitso ati m’Paradaiso?