Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pewani Kutengera Maganizo a M’dzikoli

Pewani Kutengera Maganizo a M’dzikoli

“Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake . . . [cha] m’dzikoli.”​—AKOL. 2:8.

NYIMBO: 38, 31

1. Kodi Paulo anapereka malangizo otani kwa Akhristu anzake? (Onani chithunzi choyambirira.)

ZIKUONEKA kuti mtumwi Paulo analemba kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose nthawi yoyamba imene anali m’ndende ku Roma koma atatsala pang’ono kutuluka mu 60 kapena 61 C.E. Iye anawafotokozera ubwino womvetsa “zinthu zauzimu.” (Akol. 1:9) Kenako Paulo ananena kuti: “Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa. Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:4, 8) Paulo anapitiriza kufotokoza chifukwa chake maganizo ena ofala pa nthawiyo anali olakwika komanso zimene zikanachititsa kuti anthu akopeke nawo. Mwachitsanzo, maganizo amenewa angachititse anthu kudziona kuti ndi anzeru komanso apamwamba kuposa ena. Choncho cholinga cha kalata yake chinali kuthandiza abale kuti apewe maganizo a m’dzikoli komanso makhalidwe oipa.​—Akol. 2:16, 17, 23.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukambirana zitsanzo za maganizo a m’dzikoli?

2 Maganizo a m’dzikoli amachititsa anthu kuona kuti malangizo a Yehova ndi osathandiza ndipo zimenezi zikhoza kufooketsa chikhulupiriro cha munthu. Masiku ano maganizo amenewa ali paliponse ndipo amalimbikitsidwa pa TV, pa intaneti, kuntchito komanso kusukulu. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti maganizowa asatisokoneze. Tikambirana zitsanzo 5 za maganizowa komanso mmene tingawapewere.

KODI NDI NZERU KUKHULUPIRIRA KUTI KULI MULUNGU?

3. Kodi anthu ambiri amakhala ndi maganizo ati, ndipo n’chifukwa chiyani?

3 “Ndikhoza kukhala munthu wabwino popanda kukhulupirira kuti kuli Mulungu.” M’mayiko ena anthu ambiri sakhulupirira Mulungu ndipo amanena kuti sangalowe chipembedzo chilichonse. N’kutheka kuti sanafufuze kuti adziwe ngati kuli Mulungu kapena ayi. Chimene amangofuna n’kukhala ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. (Werengani Salimo 10:4.) Anthu ena amaona ngati ndi nzeru kunena kuti, “Ndikhoza kukhala ndi makhalidwe abwino popanda kukhulupirira Mulungu.”

4. Kodi tingakambirane bwanji ndi munthu amene amanena kuti kulibe Mulungu?

4 Kodi pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti kulibe Mulungu? Munthu akafufuza zimene asayansi amanena kuti adziwe ngati zamoyo zinachita kulengedwa kapena ayi, akhoza kusokonezedwa ndi mfundo zambirimbiri. Koma kunena zoona, kupeza yankho lake n’kosavuta. Kuti nyumba ikhalepo pamafunika munthu woti aimange, ndiye kuli bwanji zinthu zamoyo? Koma ngakhale kupanga maselo aang’ono a zinthu zamoyo kungakhale kovuta kwambiri kuposa nyumba iliyonse chifukwa amatha kuchulukana, pomwe nyumba singachite zimenezi. Maselowa amatha kusunga komanso kukopera malangizo owathandiza kuti azichulukana. Ndiye kodi malangizo a m’maselowa amachokera kuti? Baibulo limanena kuti: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”​—Aheb. 3:4.

5. Kodi tingakambirane bwanji ndi munthu amene amanena kuti tikhoza kukhala ndi makhalidwe abwino popanda kukhulupirira Mulungu?

5 Nanga tingakambirane bwanji ndi munthu amene amanena kuti anthufe tikhoza kukhala ndi makhalidwe abwino popanda kukhulupirira Mulungu? Mawu a Mulungu amavomereza kuti anthu osakhulupirira amatha kukhala ndi makhalidwe ena abwino. (Aroma 2:14, 15) Mwachitsanzo, amatha kukonda komanso kulemekeza makolo awo. Koma kodi munthu amene savomereza kuti pali Mulungu amene ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika angamasankhe zochita mwanzeru nthawi zonse? (Yes. 33:22) Anthu ambiri oganiza bwino amavomereza kuti kusokonekera kwa zinthu padzikoli kukusonyeza kuti anthu amafunika kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Werengani Yeremiya 10:23.) Choncho si nzeru kuganiza kuti munthu akhoza kusiyanitsa bwinobwino zoyenera ndi zolakwika popanda kukhulupirira kuti kuli Mulungu komanso kutsatira mfundo zake.​—Sal. 146:3.

KODI CHIPEMBEDZO CHINGATITHANDIZE?

6. Kodi anthu ambiri amaona bwanji chipembedzo?

6 “Munthu akhoza kukhala wosangalala popanda kukhala m’chipembedzo chilichonse.” Anthu ambiri amakopeka ndi maganizo amenewa chifukwa amaona kuti chipembedzo n’chosasangalatsa komanso chosathandiza. Vuto lina ndi lakuti zipembedzo zambiri zimalakwitsa pophunzitsa kuti Mulungu amaotcha anthu, pokakamiza anthu kuti azipereka ndalama komanso polimbikitsa zandale. M’pake kuti anthu ambiri amaona kuti akhoza kukhala osangalala popanda kukhala m’chipembedzo chilichonse. Anthu oterewa akhoza kumanena kuti: “Ine ndimakonda Mulungu koma sindifuna kukhala m’chipembedzo chilichonse.”

7. Kodi chipembedzo choona chimathandiza bwanji anthu kukhala osangalala?

7 Koma kodi n’zoona kuti munthu akhoza kukhala wosangalala popanda kukhala m’chipembedzo chilichonse? N’zoona kuti munthu akhoza kukhala wosangalala popanda kukhala m’chipembedzo chonyenga, koma n’zosatheka kukhala wosangalala ngati sali pa ubwenzi ndi Yehova yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Chilichonse chimene Mulungu amachita chimakhala chothandiza kwa ena. Atumiki ake amasangalalanso chifukwa choti amakonda kuthandiza anzawo. (Mac. 20:35) Mwachitsanzo, taganizirani mmene chipembedzo choona chimathandizira mabanja kuti akhale osangalala. Paja chimaphunzitsa anthu okwatirana kuti azilemekezana, aziona kuti ukwati ndi wopatulika, azipewa chigololo, aziphunzitsa ana awo kuti akhale aulemu komanso kuti azikonda anzawo ndi mtima wonse. Zonsezi zimathandiza kuti atumiki a Yehova azikhala osangalala ndiponso ogwirizana m’mipingo yawo komanso padziko lonse.​—Werengani Yesaya 65:13, 14.

8. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Mateyu 5:3 pofotokoza zimene zimathandiza anthu kukhala osangalala?

8 Koma kodi tingakambirane bwanji ndi anthu amene amaganiza kuti tikhoza kukhala osangalala popanda kutumikira Mulungu? Taganizirani funso ili: Kodi n’chiyani chimathandiza anthu kuti azisangalala? Anthu ena amasangalala ndi zinthu monga ntchito yawo kapena masewera enaake. Ena amamva bwino akamasamalira achibale awo kapena anzawo. N’zoona kuti zinthu zimenezi zimasangalatsa, koma pali chinthu china chofunika pa moyo chimene chingatithandize kukhala osangalala mpaka kalekale. Mosiyana ndi nyama, anthufe tikhoza kuphunzira za Mlengi wathu n’kumamutumikira mokhulupirika. Ndipo tinalengedwa m’njira yoti tizisangalala tikamachita zimenezi. (Werengani Mateyu 5:3.) Mwachitsanzo, atumiki a Mulungu amasangalala komanso kulimbikitsidwa akamasonkhana kuti alambire Yehova limodzi. (Sal. 133:1) Amasangalalanso ndi zinthu monga ubale wapadziko lonse, makhalidwe abwino amene ali nawo komanso chiyembekezo chawo.

KODI TIYENERA KUTSATIRA MFUNDO ZA MAKHALIDWE ABWINO?

9. (a) Kodi anthu ambiri amakhala ndi maganizo otani pa nkhani ya kugonana? (b) N’chifukwa chiyani Mawu a Mulungu amaletsa kuti anthu amene sali pa banja azigonana?

9 “Cholakwika n’chiyani ngati anthu amene sali pa banja atagonana?” Anthu akhoza kutiuza kuti: “Anthufe timafunika kusangalala ndi moyo. Ndiye cholakwika n’chiyani ngati anthu amene sali pa banja atagonana?” Si nzeru kuganiza kuti zimenezi zilibe vuto lililonse. Tikutero chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amaletsa chiwerewere. * (Werengani 1 Atesalonika 4:3-8.) Yehova ndi amene anatilenga, choncho ali ndi ufulu wotipatsa malamulo. Malamulo a Mulungu amanena kuti mwamuna ndi mkazi akhoza kugonana pokhapokha ngati ali pa banja. Mulungu amatipatsa malamulo chifukwa chotikonda ndipo amadziwa kuti malamulowo ndi othandiza. Mabanja amene amatsatira malamulowa amakhala okondana, aulemu komanso otetezeka. Mulungu salekerera anthu amene satsatira mwadala malamulo ake.​—Aheb. 13:4.

10. Kodi Mkhristu angapewe bwanji chiwerewere?

10 Mawu a Mulungu amatipatsa malangizo othandiza kuti tizipewa chiwerewere. Njira imodzi yofunika kwambiri ndi kusamala ndi zimene timaona. Paja Yesu ananena kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mat. 5:28, 29) Choncho Akhristu amapewa kuonera zolaula kapena kumvetsera nyimbo zolimbikitsa chiwerewere. Nayenso mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama.” (Akol. 3:5) Tiyenera kusamalanso ndi zimene timaganiza komanso kulankhula.​—Aef. 5:3-5.

KODI TIZIYESETSA KUPEZA NTCHITO YAPAMBWAMBA?

11. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amafuna kupeza ntchito yapamwamba?

11 “Mukhoza kukhala osangalala mukapeza ntchito yapamwamba.” Anthu ambiri amatilimbikitsa kuti cholinga chathu pa moyo chikhale kupeza ntchito yapamwamba. Amanena kuti tikapeza ntchito yotereyi tikhoza kukhala otchuka, olemekezeka komanso achuma. Popeza anthu ambiri amaona kuti kupeza ntchito yapamwamba n’kofunika kwambiri, Mkhristu akhoza kutengeranso maganizowa.

12. Kodi kukhala ndi ntchito yapamwamba kumathandizadi munthu kukhala wosangalala?

12 Kodi n’zoona kuti munthu akapeza ntchito yapamwamba amakhaladi wosangalala? Ayi. Kumbukirani kuti zimene zinachititsa Satana kuti ayambe kuchita zoipa ndi kulakalaka kuti azilamulira ena komanso kuti azilemekezedwa. Koma m’malo mokhala wosangalala iye ndi wokwiya kwambiri. (Mat. 4:8, 9; Chiv. 12:12) Mwina munthu angasangalale akapeza ntchito yapamwamba. Koma sangasangalale kwambiri ngati mmene angachitire akamathandiza anthu ena kuti azitsatira nzeru ya Mulungu n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha. Tisaiwalenso kuti anthu a m’dzikoli amakhala ndi mtima wopikisana ndipo amachitirana nsanje koma pamapeto pake amakhala ngati ‘amangothamangitsa mphepo.’​—Mlal. 4:4.

13. (a) Kodi tiyenera kuona bwanji ntchito? (b) Malinga ndi kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Tesalonika, kodi iye ankasangalala kwambiri ndi chiyani?

13 N’zoona kuti tiyenera kugwira ntchito kuti tizipeza zofunika pa moyo ndipo si kulakwa kusankha ntchito imene imatisangalatsa. Komabe ntchitoyo siyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Paja Yesu anati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Tikamaika pamalo oyamba kutumikira Yehova ndiponso kuphunzitsa ena Mawu ake, timakhala osangalala kwambiri. Mtumwi Paulo ankadziwa bwino zimenezi. Asanakhale Mkhristu anali ndi udindo waukulu m’chipembedzo chachiyuda koma anayamba kukhala wosangalala kwambiri atayamba kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu n’kumaona mmene Mawuwo akuwathandizira. (Werengani 1 Atesalonika 2:13, 19, 20.) Palibe ntchito ina imene ingasangalatse munthu kuposa imeneyi.

Tikamathandiza anthu kuti azitsatira nzeru ya Mulungu timakhala osangalala (Onani ndime 12 ndi 13)

KODI TIKHOZA KUTHETSA MAVUTO A M’DZIKOLI?

14. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakopeka ndi maganizo akuti anthu akhoza kuthetsa mavuto a m’dzikoli?

14 “Anthu akhoza kuthetsa mavuto a m’dzikoli.” Anthu ambiri amakopeka ndi maganizo amenewa. Zili choncho chifukwa chakuti ngati maganizowa atakhala oona, ndiye kuti anthu sangafunike kutsogoleredwa ndi Mulungu komanso akhoza kumangochita zimene akufuna. Anthu ena amakhulupirira maganizo amenewa chifukwa chakuti ochita kafukufuku ena anapeza kuti nkhondo, uchigawenga, matenda komanso umphawi zikuchepa masiku ano. Lipoti lina linanena kuti: “Anthu ambiri ayamba kukhala ndi makhalidwe abwino chifukwa akufuna kuti zinthu ziziyenda bwino m’dzikoli.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu ayamba kutulukira njira zothetsera mavuto amene akhala akuwasowetsa mtendere? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione bwinobwino mavuto amenewa.

15. N’chiyani chikusonyeza kuti mavuto a anthu akuchulukirachulukira?

15 Nkhondo: Nkhondo ziwiri zapadziko lonse zinapha anthu oposa 60 miliyoni. Koma chichitikireni nkhondozi, anthu sanasiyebe kumenyana. Mwachitsanzo, pofika mu 2015, anthu oposa 65 miliyoni anali atathawa kwawo chifukwa cha nkhondo kapena kuzunzidwa. Ndipo mu chaka cha 2015 chokha anthu pafupifupi 12.4 miliyoni anathawa kwawo. Uchigawenga: N’zoona kuti uchigawenga wa mitundu ina ukuchepa koma uchigawenga wina monga wa pa intaneti, nkhanza za m’banja komanso zinthu zina zaupandu zikuchulukirachulukira. Anthu ambiri amanenanso kuti chinyengo chikuwonjezereka kwambiri padziko lonse. Choncho zikuonekeratu kuti anthu sangathetseretu uchigawenga. Matenda: N’zoona kuti pali matenda ena amene achepa masiku ano. Koma lipoti lina la mu 2013 linanena kuti chaka chilichonse anthu okwana 9 miliyoni amene sanakwanitse zaka 60 amafa ndi matenda a mtima, sitiroko, khansa, chifuwa komanso matenda a shuga. Umphawi: Malinga ndi lipoti la World Bank, anthu ovutika ndi umphawi ku Africa kokha anawonjezereka kuchoka pa 280 miliyoni mu 1990 kufika pa 330 miliyoni mu 2012.

16. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto a anthu? (b) Kodi Yesaya komanso wolemba masalimo analosera kuti Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ati?

16 Masiku ano anthu ambiri amene ali ndi maudindo m’boma kapena pa nkhani zamalonda ndi odzikonda. Choncho sangathetse nkhondo, uchigawenga, matenda komanso umphawi. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto amenewa. Taganizirani zimene Yehova adzachitire anthu. Nkhondo: Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu zimene zimayambitsa nkhondo monga kudzikonda, chinyengo, mtima wokonda dziko lako, chipembedzo chonyenga komanso Satana weniweniyo. (Sal. 46:8, 9) Uchigawenga: Ufumu wa Mulungu wayamba kale kuphunzitsa anthu kuti azikondana komanso kukhulupirirana ndipo palibe boma lina lililonse limene lingachite zimenezi. (Yes. 11:9) Matenda: Yehova adzathandiza anthu ake kuti asamadwale. (Yes. 35:5, 6) Umphawi: Yehova adzathetsa umphawi ndipo adzapereka zinthu zonse zofunika kwa anthu ake. Pa nthawiyo, moyo wawo udzakhala wabwino kuposa wa anthu achuma a masiku ano ndipo adzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.​—Sal. 72:12, 13.

“MUDZIWE MMENE MUNGAYANKHIRE”

17. Kodi mungapewe bwanji maganizo a m’dzikoli?

17 Ngati mwamva maganizo a m’dziko amene akhoza kukusokonezani, muyenera kufufuza zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhaniyo komanso kukambirana ndi Mkhristu wina amene amadziwa zambiri. Ganizirani chifukwa chake mukhoza kukopeka ndi maganizowo, chifukwa chake ndi olakwika komanso zimene munganene pokambirana ndi munthu amene ali ndi maganizowo. Tonsefe tikhoza kupewa kutengera maganizo a m’dzikoli tikamatsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa anthu amumpingo wa ku Kolose akuti: “Pitirizani kuyenda mwanzeru pochita zinthu ndi anthu akunja . . . Mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”​—Akol. 4:5, 6.

^ ndime 9 Anthu ambiri sazindikira kuti mawu opezeka pa Yohane 7:53 ndi 8:1-11 sapezeka m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo koma anthu anachita kuwonjezera. Anthu ena akawerenga nkhaniyi amaganiza kuti munthu amene sanachimwepo ndi amene ayenera kuweruza munthu amene wachita chigololo. Koma lamulo limene Yehova anapereka kwa Aisiraeli linali lakuti: “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifera pamodzi.”​—Deut. 22:22.