NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) November 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa December 25, 2017 mpaka January 28, 2018.

Tiziimba Mosangalala

Kodi tingatani ngati timachita manyazi kuimbira Yehova mokweza pamisonkhano?

Kodi Mumathawira kwa Yehova?

Mizinda yothawirako imasonyeza kuti Mulungu amakhululuka ndi mtima wonse.

Tsanzirani Chilungamo ndi Chifundo cha Yehova

Kodi mizinda yothawirako imasonyeza bwanji chifundo cha Yehova? Nanga imasonyeza kuti iye amaona bwanji moyo wa munthu? Kodi imasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wachilungamo kwambiri?

Munthu Wopatsa Adzadalitsidwa

Tikhoza kugwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu komanso ndalama zathu pothandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu.

Pewani Kutengera Maganizo a M’dzikoli

Tonsefe tiyenera kusamala kuti maganizo a m’dzikoli asatisokoneze. Onani zitsanzo 5 za maganizo a m’dzikoli.

Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto

Paulo anakumbutsa Akhristu anzake za madalitso amene akuyembekezera, kenako anawachenjeza za zinthu zimene zingawalepheretse kupeza madalitsowo.

Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mpingo Wanu Watsopano?

Ngati mwasamukira mumpingo watsopano, mukhoza kuvutika kuti muzolowere. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni?