Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto

Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto

‘Musalole kuti munthu aliyense akumanitseni mphoto.’​—AKOL. 2:18.

NYIMBO: 122, 139

1, 2. (a) Kodi atumiki a Yehova akuyembekezera mphoto iti? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisalephere kudzalandira mphotoyo? (Onani chithunzi choyambirira.)

MOFANANA ndi mtumwi Paulo, odzozedwa akuyembekezera kulandira “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba.” (Afil. 3:14) Iwo akuyembekezera kukalamulira limodzi ndi Yesu Khristu kumwamba komanso kudzagwira nawo ntchito yothandiza anthu kuti akhalenso angwiro. (Chiv. 20:6) Kunena zoona, Yehova wawapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri. Koma nawonso a nkhosa zina akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Iwo akuyembekezera mphoto ya moyo wosatha padziko lapansi.​—2 Pet. 3:13.

2 Pofuna kuthandiza odzozedwa anzake kuti akhalebe okhulupirika n’kukalandira mphoto yawo, Paulo anawauza kuti: “Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba.” (Akol. 3:2) Iwo anafunika kuganizira nthawi zonse zinthu zamtengo wapatali zimene akuyembekezera kumwamba. (Akol. 1:4, 5) Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba  kapena kudzakhala padzikoli, kuganizira kwambiri madalitso amene Yehova watilonjeza kungatithandize kuti chilichonse chisatilepheretse kudzalandira mphotoyo.​—1 Akor. 9:24.

3. Kodi Paulo anachenjeza Akhristu anzake za zinthu ziti?

3 Paulo anachenjezanso Akhristu anzake zinthu zimene zikanawalepheretsa kulandira mphoto yawo. Mwachitsanzo, analembera mpingo wa ku Kolose kuti usamale ndi Akhristu achinyengo amene ankaganiza kuti akhoza kusangalatsa Mulungu chifukwa chotsatira Chilamulo osati kukhulupirira Khristu. (Akol. 2:16-18) Paulo anatchulanso zinthu zina zimene zikusokoneza anthu mpaka pano, zomwe zingatilepheretse kudzalandira mphoto. Mwachitsanzo, anatchula zimene tingachite kuti tipewe kulakalaka zinthu zoipa, zimene tingachite ngati tasemphana maganizo ndi Akhristu anzathu komanso mmene tingathetsere mavuto a m’banja. Malangizo amene anapereka pa nkhani zimenezi ndi othandiza kwambiri masiku ano. Choncho tiyeni tikambirane malangizo achikondi amene Paulo analembera Akhristu a ku Kolose.

PEWANI ZIMENE ZINGAKUCHITITSENI KULAKALAKA ZOIPA

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulakalaka zoipa kungatilepheretse kulandira mphoto?

4 Paulo atakumbutsa abale ake zinthu zosangalatsa zimene akuyembekezera, analemba kuti: “Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.” (Akol. 3:5) Nthawi zina kulakalaka zinthu zoipa kungakhale kwamphamvu kwambiri ndipo kungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, m’bale wina amene anatengeka ndi zinthu zoipa kenako n’kubwerera mumpingo anati: “Chilakolako changa chinali champhamvu kwambiri moti ndinangozindikira kuti ndachita kale zoipazo.”

5. Kodi tingatani kuti tipewe kuchita zinthu zoipa?

5 Tiyenera kusamala kwambiri tikakumana ndi zinthu zimene zingatichititse kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za Yehova. Mwachitsanzo, anthu akakhala pa chibwenzi angachite bwino kuikiratu malire pa zinthu monga kugwirana, kukisana kapena kukhala awiriwiri. (Miy. 22:3) Mkhristu akhoza kukumananso ndi zinthu zimene zingamugwetsere mumsampha akapita kukagwira ntchito kutali kapena akamagwira ntchito ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. (Miy. 2:10-12, 16) Mukakumana ndi zinthu ngati zimenezi, ndi bwino kuuza anthu kuti ndinu wa Mboni za Yehova, kuchita zinthu mwaulemu komanso kukumbukira kuti kukopana ndi koopsa kwambiri. Pamene tikuda nkhawa kapena kusowa wocheza naye m’pamene tiyenera kusamala kwambiri. Zili choncho chifukwa chakuti pa nthawi imeneyi m’pamene timafunitsitsa kuti munthu wina atichezetse ndipo tikhoza kulolera kuchezetsedwa ndi aliyense amene angapezeke. Choncho ngati muli ndi nkhawa kapena mukusowa wocheza naye, muyenera kudalira Yehova komanso anthu ake kuti akuthandizeni n’cholinga choti musalephere kudzalandira mphoto.​—Werengani Salimo 34:18; Miyambo 13:20.

6. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani posankha zosangalatsa?

6 Kuti tipewe kulakalaka zinthu zoipa, tiyenera kupewa zosangalatsa zimene zimalimbikitsa zoipazo. Masiku ano, zinthu zambiri zimene zimapezeka m’mafilimu, pa TV kapena m’nyimbo zikufanana ndi zimene zinkachitika m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora. (Yuda 7) Anthu opanga mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV amaonetsa zinthuzo ngati kuti ndi zimene anthu onse amachita ndipo sizingabweretse vuto lililonse. Choncho tiyenera kusamala kwambiri posankha zimene timaonera kapena kumvetsera. Tiyenera kusankha zosangalatsa zomwe sizingatilepheretse kulandira mphoto yathu.​—Miy. 4:23.

 “VALANI” CHIKONDI NDI KUKOMA MTIMA

7. Kodi tingakumane ndi mavuto otani mumpingo wachikhristu?

7 Tonsefe timadziwa kuti ndi mwayi waukulu kukhala mumpingo wachikhristu. Tikamaphunzira limodzi Mawu a Mulungu kumisonkhano komanso kulimbikitsana timathandizidwa kuika maganizo athu pa mphoto imene tikuyembekezera. Koma nthawi zina tingakumane ndi mavuto chifukwa chosemphana maganizo ndi Akhristu anzathu. Tikapanda kuthetsa mwamsanga mavuto oterewa tikhoza kuyamba kusungirana chakukhosi.​—Werengani 1 Petulo 3:8, 9.

8, 9. (a) Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kuti tidzalandire mphoto? (b) Ngati Mkhristu wina watikhumudwitsa, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhalabe naye mwamtendere?

8 Kodi tingatani kuti kusemphana maganizo ndi Akhristu anzathu kusadzatilepheretse kulandira mphoto? Paulo anauza Akhristu a ku Kolose kuti: “Monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu, oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni. Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”​—Akol. 3:12-14.

9 Chikondi komanso kukoma mtima, zingatithandize kuti tizikhululukirana. Mwachitsanzo, ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, tizikumbukira nthawi zimene ifeyo tinachitanso zinthu zokhumudwitsa ena. Mosakayikira tinayamikira kwambiri chikondi ndi kukoma mtima zimene abale ndi alongowo anatisonyeza potikhululukira. (Werengani Mlaliki 7:21, 22.) Timayamikiranso kwambiri kukoma mtima kumene Khristu wasonyeza potithandiza kuti tizilambira Yehova mogwirizana. (Akol. 3:15) Tonsefe timakonda Mulungu mmodzi, timalalikira uthenga wofanana ndipo mavuto ambiri amene timakumana nawo ndi ofanananso. Tikamasonyeza chikondi ndiponso kukoma mtima pokhululukirana, timakhala ogwirizana ndipo timapewa zinthu zimene zingatilepheretse kudzalandira mphoto.

10, 11. (a) Kodi nsanje ndi yoopsa bwanji? (b) Kodi tingatani kuti nsanje isatilepheretse kupeza mphoto?

10 M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kuti nsanje ingatilepheretse kulandira mphoto. Mwachitsanzo, Kaini anachitira nsanje m’bale wake Abele ndipo anamupha. Kora, Datani ndi Abiramu anachitira nsanje Mose ndipo anayamba kutsutsana naye. Nayenso Sauli anachita nsanje kwambiri ataona zinthu zabwino zimene Davide anachita moti ankafuna kumupha. M’pake kuti Mawu a Mulungu amanena kuti: “Pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.”​—Yak. 3:16.

11 Tikamayesetsa kukhala achikondi ndiponso okoma mtima, sitidzachitira ena nsanje. Paja Baibulo limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje.” (1 Akor. 13:4) Kuti tisamachite nsanje tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Tiyenera kuona kuti ndife thupi limodzi ndi abale ndi alongo athu. Maganizo amenewa angatithandize kuti tizikondana mogwirizana ndi malangizo akuti: “Chiwalo chimodzi chikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalira nacho limodzi.” (1 Akor. 12:16-18, 26) Choncho m’malo mochita nsanje mnzathu akadalitsidwa, tiyenera kusangalala naye. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mwana wa Mfumu Sauli dzina lake Yonatani. M’malo mochitira nsanje Davide atasankhidwa kuti alowe ufumu wa Sauli, anamulimbikitsa. (1 Sam. 23:16-18) Nafenso tiyenera kuyesetsa kukhala achikondi komanso okoma mtima ngati Yonatani.

 YESETSANI KUTI BANJA LANU LONSE LIDZALANDIRE MPHOTO

12. Kodi tiyenera kutsatira malangizo ati kuti banja lathu lonse lidzalandire mphoto?

12 Kutsatira mfundo za m’Baibulo kungathandize banja kuti likhale lamtendere, losangalala komanso kuti lidzalandire mphoto. Kodi ndi malangizo ati okhudza mabanja amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Kolose? Iye anati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. Inu amuna, musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri. Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye. Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.” (Akol. 3:18-21) Inunso mungavomereze kuti malangizo amene Paulo anaperekawa ndi othandizadi kwa amuna, akazi komanso ana.

13. Kodi mlongo angathandize bwanji mwamuna wake yemwe si Mboni?

13 Ngati ndinu mlongo ndipo mukuona kuti mwamuna wanu yemwe si Mboni sachita bwino zinthu, kodi mungatani? Kodi kukangana naye pa nkhani zimene amalakwitsa kungathandize kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino? Ngakhale zitatheka kuti asinthe n’kumachita zimene inuyo mumafuna, n’zokayikitsa kuti angayambe kuphunzira Baibulo. Koma mukamayesetsa kumulemekeza, mudzathandiza kuti m’banja mwanu mukhale mtendere ndipo mudzalemekeza kwambiri Yehova. N’kuthekanso kuti mwamunayo akhoza  kuyamba kuphunzira ndipo pamapeto pake nonse mudzalandira mphoto.​—Werengani 1 Petulo 3:1, 2.

14. Kodi mwamuna ayenera kuchita chiyani ngati mkazi wake yemwe si wa Mboni samulemekeza?

14 Ngati ndinu m’bale ndipo mukuona kuti mkazi wanu yemwe si Mboni sakulemekezani, kodi mungatani? Kodi kumukalipira kuti adziwe zoti ndinu mutu kungathandize kuti ayambe kukulemekezani? Yankho ndi lakuti ayi. Paja Mulungu amanena kuti amuna ayenera kutsanzira Yesu n’kumatsogolera banja lawo mwachikondi. (Aef. 5:23) Yesu amatsogolera mpingo mwachikondi komanso moleza mtima. (Luka 9:46-48) Mwamuna akamatsanzira Yesu akhoza kuthandiza mkazi wake kuti nayenso ayambe kulambira Yehova.

15. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amakonda mkazi wake?

15 Baibulo limalangiza amuna kuti: “Inu amuna, musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.” (Akol. 3:19) Mwamuna wachikondi amalemekeza mkazi wake pomvetsera maganizo ake komanso kumutsimikizira kuti amaona kuti maganizo akewo ndi ofunika. (1 Pet. 3:7) N’zoona kuti si nthawi zonse pamene angachite zimene mkaziyo wanena, koma kumva maganizo ake kumathandiza kuti asankhe zinthu mwanzeru. (Miy. 15:22) Mwamuna wachikondi amayesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize mkazi wake kuti azimulemekeza, osati kungomulamula kuti azimulemekeza. Mwamuna amene amakonda mkazi wake ndiponso ana ake, amathandiza banja lake kuti lizitumikira Yehova mosangalala komanso kuti lidzalandire mphoto.

Kodi tingatani kuti mavuto a m’banja asatilepheretse kudzalandira mphoto yathu? (Onani ndime 13-15)

ACHINYAMATA, YESETSANI KUTI MUDZALANDIRE MPHOTO

16, 17. Ngati ndinu wachinyamata, kodi mungatani kuti musamakwiye ndi malangizo a makolo anu?

16 Ngati ndinu wachinyamata ndipo mumaona kuti makolo anu sakumvetsani komanso amakupanikizani, kodi mungatani? Maganizo amenewa akhoza kukuchititsani kuganiza kuti si nzeru kutumikira Yehova ndipo ngati maganizo amenewa atakula mukhoza kusiyadi kumutumikira. Koma dziwani kuti mukasiya, mudzaona nokha kuti palibenso anthu ena amene amakukondani ndi mtima wonse ngati mmene amachitira makolo anu komanso abale ndi alongo.

17 Ndipo ngati makolo anu sakulangizani, zingakhale zokayikitsa kuti amakukondani ndi mtima wonse. (Aheb. 12:8) Mwina njira imene makolowo amakulangizirani ndi imene sikusangalatsani. Koma m’malo mongoipidwa ndi mmene amaperekera malangizo, muyenera kuganizira chimene chimawapangitsa kuchita zimenezo. Choncho muyenera kukhala odekha ndipo muziyesetsa kuti musamakwiye msanga akamakudzudzulani. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti: “Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.” (Miy. 17:27) Yesetsani kuchita zinthu ngati wozindikira ndipo mukamalangizidwa muzimvetsera mofatsa. Muziyesetsa kuona mmene mungagwiritsire ntchito malangizowo popanda kuganizira kwambiri mmene akuwaperekera. (Miy. 1:8) Dziwani kuti ndi dalitso lalikulu kukhala ndi makolo amene amakonda Yehova ndi mtima wonse. Iwo amafunitsitsa kukuthandizani kuti mudzapeze mphoto ya moyo wosatha.

18. N’chifukwa chiyani inuyo simudzasiya kuganizira mphoto yanu?

18 Kaya tikuyembekezera mphoto yopita kumwamba kapena yokhala ndi moyo wosatha padziko lapansili, tiyenera kuganizira kwambiri mphoto yathuyo. Tizikumbukira kuti Mlengi wathu ndi amene watilonjeza mphotoyo ndipo sizingalephereke. Ponena za dziko latsopano, Mulungu anati: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yes. 11:9) Pa nthawi imeneyo, aliyense amene adzakhale padzikoli azidzaphunzitsidwa ndi Yehova. Nkhani imeneyinso ndi yosangalatsa kwambiri. Choncho tiyeni tonse tiziganizira kwambiri zimene Yehova watilonjeza ndipo tisalole chilichonse kutilepheretsa kudzalandira mphoto yathu.