Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mapiko a Gulugufe

Mapiko a Gulugufe

MAPIKO a gulugufe ndi osalimba moti ngakhale zinthu ngati fumbi kapena mame zikhoza kupangitsa kuti gulugufe azivutika kuuluka. Komabe nthawi zonse mapiko a gulugufe amakhala opanda fumbi komanso ouma. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Timamba tosanjikizana ta mapiko a gulugufe

Taganizirani izi: Akatswiri ofufuza zinthu a payunivesite ya ku Ohio anafufuza zokhudza agulugufe a mtundu winawake (Morpho didius). Iwo anapeza zoti ngakhale kuti mapiko a agulugufewa amaoneka osalala, ali ndi timamba tosanjikizana tofanana ndi matailosi apadenga. Timambati timachititsa kuti pamapikowa pakagwera zinthu monga fumbi kapena madzi, zizichoka mosavuta. Akatswiri opanga zinthu akufuna kutengera kapangidwe ka mapikowa n’cholinga choti apange mabandeji komanso zinthu zina zogwiritsa ntchito kuchipatala zoti zisamade komanso kunyowa ndi madzi.

Mapiko a gulugufe ndi chinthu chimodzi mwa zinthu zachilengedwe zimene asayansi akuyesetsa kutengera kapangidwe kake. Katswiri wina wofufuza zinthu, dzina lake Bharat Bhushan, ananena kuti: “M’chilengedwechi muli zinthu zambiri, zazikulu ndi zazing’ono zomwe, zimene asayansi angatengere kapangidwe kake.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mapiko a gulugufe anangokhalako okha kapena pali winawake amene anawapanga?