GALAMUKANI! April 2014 | Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?
Kodi munaganizapo zodzipha, kapena pali winawake amene mukumudziwa yemwe anaganizapo zodzipha? Kudziwa zifukwa zokhalira ndi moyo kungathandize kwambiri.
Zochitika Padzikoli
Nkhani zake: mzinda umene maloboti ake awakonza moti azionetsa mtundu wofanana pa nthawi imodzi, vuto la kunenepa lomwe lalowa m’malo mwa vuto la kusowa zakudya m’thupi ndi mbalame ya zaka zoposa 60 yomwe yaswanso mwana wina.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?
Kodi zingatheke bwanji kuti malangizo owawa kwambiri akhale othandiza kwambiri?
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?
N’chiyani chingachititse munthu kumaona kuti imfa si mdani?
NKHANI YAPACHIKUTO
Zinthu Zimasintha pa Moyo
Ngakhale zinthu zitakhala kuti sizingasinthe pa moyo wanu, koma pali zimene mungasinthe.
NKHANI YAPACHIKUTO
Pali Zimene Zingakuthandizeni
Pali zifukwa zitatu zokuchititsani kukhalabe ndi moyo.
NKHANI YAPACHIKUTO
Pali Chiyembekezo Choti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo
Chiyembekezo chingakuthandizeni kuiwala mavuto anu.
KUCHEZA NDI ANTHU
Wochita Kafukufuku Wazamankhwala Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Frédéric Dumoulin ankadana ndi chipembedzo choncho anasiya kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Kodi kuphunzira Baibulo komanso kufufuza mmene zamoyo zimagwirira ntchito kunamuthandiza bwanji kuti ayambe kukhulupirira zoti kuli Mlengi?
ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Cambodia
N’chifukwa chiyani anthu oti angokumana koyamba amatchulana kuti achimwene, chemwali, azakhali, amalume kapena agogo?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Kusankhana Mitundu
Kodi anthu a mitundu yonse ndi ofanana? Kodi kusankhana mitundu kudzatha?
KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Mapiko a Gulugufe
Pamwamba pa mapiko a gulugufe ameneyu pamaoneka posalala koma pali tizinthu tomwe mungathe kutiona mutagwiritsa ntchito chipangizo choonera zinthu zing’onozing’ono. Kodi tinthu timeneti n’chiyani?
Zina zimene zili pawebusaiti
Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?
Kodi munthu wina amakukakamizani kuti mumutumizire zolaula? Kodi kutumizirana zolaula kuli ndi mavuto otani? Kodi ndi kukopana basi?
Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?
Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.
Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji?
N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?
Yesefe Anapulumutsa Anthu Ambiri
Nonse monga banja werengani Genesis chaputala 41 mpaka 50 pogwiritsa ntchito zithunzi za nkhani za m’Baibulo.