Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?

Zinthu Zimasintha pa Moyo

Zinthu Zimasintha pa Moyo

“Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”—2 AKORINTO 4:8.

Kudzipha kuli ngati kuwotcha nyumba chifukwa choti m’nyumbamo muli makoswe, m’malo mongopha makoswewo. Ngakhale munthu atakumana ndi mavuto aakulu ooneka ngati sangathe, m’kupita kwa nthawi akhoza kutha. Ndipotu zinthu zikhoza kusintha n’kuyamba kuyenda bwino.—Onani bokosi lakuti  “Zinthu Zinasintha pa Moyo Wawo.”

Ngakhale zitakhala kuti zinthu sizingasinthe pa moyo wanu, ndi bwino kumathana ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa, m’malo momada nkhawa ndi mavuto amene angabwere m’tsogolo. Yesu ananena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

Nanga kodi mungatani zitakhala kuti vuto lanu ndi loti silingathe? Mwachitsanzo, mwina muli ndi matenda okhalitsa. Kapenanso mukuvutika maganizo chifukwa cha zinthu zoti sizingasinthe, monga kutha kwa ukwati kapena imfa ya munthu amene munkamukonda?

Dziwani kuti ngakhale pa zochitika zoterezi, mungathebe kusintha zinazake. Mungasinthe mmene mukuonera nkhaniyo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera. (Miyambo 15:15) Zingakuthandizeninso kuti mupirire vuto lanulo m’malo momaganiza zoti ndi bwino kungofa. Zotsatira zake zingakhale zoti ngakhale kuti simungathetse vutolo, mungayambe kuliona moyenera.—Yobu 2:10.

MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Simungathe kukwera phiri mwa kungoyenda sitepe imodzi yokha, koma mutayenda masitepe ambirimbiri mungapezeke muli pamwamba pa phirilo. N’chimodzimodzinso ndi mavuto anu amene mwina mungamawaone kuti ndi aakulu ngati phiri. Muyenera kumathana nawo pang’onopang’ono.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Uzani mnzanu kapena wachibale za vuto lanulo. Munthu ameneyo angakuthandizeni kuti muyambe kuona vutolo moyenera.—Miyambo 11:14.