Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Cambodia

Dziko la Cambodia

M’DZIKO la Cambodia muli nyumba, misika komanso misewu yambiri zimene anazimanga pamwamba pa madzi. M’misewuyi mumadzadza njinga zamoto zimene zimanyamula zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo nkhuku komanso mafiriji kuchoka nazo kwina kupita kwina.

Anthu a ku Cambodia amadziwika kuti ndi ansangala, okonda kucheza komanso amakonda kuchitira limodzi zinthu. Amakonda kutchulana kuti achimwene, chemwali, azakhali, amalume kapena agogo, ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa munthu amene angokumana naye koyamba.

Anthu ena a ku Cambodia amakhala m’nyumba zangati maboti ndipo ena amakhala m’nyumba zomwe anazimanga pamathandala akuluakulu. M’dzikoli mumapezekanso sukulu, zipatala, misika komanso malo othirira mafuta, zomangidwa pamathandala

Zipatso zimene zimapezeka zambiri ku Cambodia

Anthu a m’dzikoli amakonda mpunga. Nthawi zambiri pa chakudya pamakhala mpunga, ndiwo zamitundu iwiri ndi msuzi. Ndiwo zimene amakonda kwambiri ndi nsomba. Kawirikawiri, amadya zakudya zophikidwa mosiyanasiyana zingapo, pa nthawi imodzi.

 Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, amalonda a ku India komanso anthu oyendera zachipembedzo ochokera ku China, anayamba kubwera ku Cambodia kudzachita malonda osinthanitsa nsalu komanso zitsulo, ndipo ankazisinthanitsa ndi matabwa, minyanga ya njovu komanso golide. Patapita nthawi, anthu a ku Cambodia anayamba kutengera zikhalidwe za anthu a ku India ndi a ku China. Chifukwa cha zimenezi ambiri anakhala Ahindu ndi Abuda. Masiku ano anthu ambiri a ku Cambodia ndi Abuda.

A Mboni za Yehova amalalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu a ku Cambodia. Athandiza anthu ambiri pogwiritsa ntchito buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli likupezeka m’zinenero pafupifupi 250, kuphatikizapo Chikambodiya.

Anthu oposa 1,500 akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo zimenezi zawathandiza kupeza mayankho a mafunso monga akuti, “Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?” Komanso “Kodi Mulungu analengeranji dzikoli?”

Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova likupezekanso m’Chikambodiya ndipo ndi limene likuoneka apali.