Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?

Pali Chiyembekezo Choti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

Pali Chiyembekezo Choti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

“Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—SALIMO 37:11.

Baibulo limavomereza kuti moyo wa munthu ndi “waufupi, wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Masiku ano aliyense amakumana ndi mavuto. Koma anthu ena alibe chiyembekezo chilichonse ndipo saganiza n’komwe zoti mavuto awowo angadzathe m’tsogolo. Ngati inunso mumaona choncho, dziwani kuti Baibulo limaphunzitsa kuti inuyo komanso anthu ena onse, mungathe kukhala ndi tsogolo labwino. Mwachitsanzo:

  • Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu amafuna kuti anthufe tizisangalala.—Genesis 1:28.

  • Yehova Mulungu amatilonjeza kuti dziko lapansili lidzakhala paradaiso.—Yesaya 65:21-25.

  • N’zosakayikitsa kuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo limeneli. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limanena kuti:

    “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

Zimenezi si nkhambakamwa chabe. Yehova Mulungu akufunitsitsa kudzakwaniritsa lonjezo limeneli ndipo ali ndi mphamvu yochitira zimenezi. Zimene Baibulo limanena zokhudza tsogolo la anthu zidzachitikadi. Choncho Baibulo limatithandizanso kudziwa kuti pali zifukwa zabwino zokhalirabe ndi moyo ngakhale mukukumana ndi mavuto.

MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Ngakhale kuti mungaone kuti mavuto amene mukukumana nawo ndi ofanana ndi mafunde apanyanja, zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza tsogolo la anthu zili ngati nangula amene angakulimbitseni kwambiri.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Phunzirani Baibulo mozama kuti mudziwe zimene limaphunzitsa zokhudza zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolo. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kuchita zimenezi. Mungalankhule ndi a Mboni a m’dera lanu kapena mungapite pa webusaiti ya jw.org/ny. *

^ ndime 11 Zimene mungachite: Pitani pa webusaiti ya jw.org/ny ndipo muyang’ane pamene palembedwa kuti, MABUKU > LAIBULALE YA PA INTANETI. Kenako fufuzani mawu akuti, “kuvutika maganizo” kapena “kudzipha” kuti mudziwe zambiri.