Pitani ku nkhani yake

Kodi Zinangochitika Zokha?

Dongosolo la M'chilengedwe

Zamoyo Zimagwiritsa Ntchito Bwino Mphamvu​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi luso lachibadwa la zamoyo zina zomwe zimatha kugwiritsa ntchito bwino mphamvu, limatithandiza kumvetsa zotani zokhudza mmene moyo unayambira?

Zamoyo Zotulutsa Kuwala​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Sikuti zinyama zina zimangotulutsa kuwala basi, koma zimagwiritsa ntchito bwino mphamvu kuposa kuwala kulikonse kopangidwa ndi anthu. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Thupi la Munthu

Thupi Lathu Limatha Kudzichiza Lokha

Kodi asayansi akupanga zotani potengera zimene thupi lathu limachita tikavulala?

Nyama Zapamtunda

Ubongo Wodabwitsa wa Gologolo wa ku Arctic​​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Onani luso lake lapadera lomwe limamuthandiza kuti akhale bwinobwino pambuyo pogona nyengo yonse yozizira.

Ubweya wa Katumbu

Nyama zambiri zam’madzi zimakhala ndi mafuta ambiri pansi pa khungu lake, omwe amathandiza kuti zizimva kutentha. Koma katumbu ali ndi ubweya wambiri womwe umamuthandiza kuti azimva kutentha.

Lilime la Mphaka​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Amphaka oweta amathera 24 peresenti ya nthawi yomwe ali maso, akudzikonzakonza. Kodi zimatheka bwanji kuti azidzinyambita mpaka kuyera?

Tindevu ta Mphaka

N’chifukwa chiyani asayansi akupanga maloboti okhala ndi zinthu zogwira ntchito ngati tindevu ta mphaka?

Luso la Galu Lotha Kununkhiza Zinthu

Kodi chochititsa chidwi ndi mphuno ya galu n’chiyani, zomwenso zachititsa asayansi kufuna kutengera mmene imagwirira ntchito, popanga zipangizo zawo?

Miyendo ya Hatchi

N’chifukwa chiyani akatswiri sangathe kutengera miyendo yake?

Luso la Mleme Loona Zinthu Ndi Makutu​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi zingatheke bwanji kuti nyama “ione” zinthu popanda kugwiritsa ntchito maso ake?

Timadzi Tomata Kwambiri ta Nkhono

Zikuoneka kuti madokotala ambiri akhoza kuyamba kugwiritsa ntchito zomatira zomwe zapangidwa potengera timadzi ta nkhono, m’malo mochita kusoka mabala a mkati mwa thupi.

Zamoyo Zam'madzi

Khungu la Shaki​​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi n’chiyani chimathandiza kuti tizilombo tisamamamatire pakhungu la shaki?

Zipsepse za Nangumi

Werengani kuti mudziwe mmene anthufe timapindulira chifukwa cha kapangidwe ka chipsepse cha nangumi.

Khungu la Nangumi Lotha Kudziyeretsa Lokha

N’chifukwa chiyani makampani a sitima za pamadzi akuchita chidwi ndi zimene khungu la nsombayi limachita?

Luso la Dolphin Lozindikira Zinthu Mosavuta

Asayansi akuyesetsa kutengera luso la nyamazi kuti apange zipangizo zowathandiza kufufuza ndiponso kuzindikira zimene zili m’madzi.

Zonanda za Nsomba Yangati Mlamba​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Adani ake akaigwira amaisiya ndipo amakhala kuti alibenso nayo ntchito koma asayansi amagoma nayo. Chifukwa chiyani?

Khungu la Kanyama Kooneka Ngati Chipwete

Kodi ndi ndani amene anapanga khungu la kanyama ka m’madzi lomwe limasintha mochititsa chidwi?

Mmene Mano a Nkhono ya M’madzi Anapangidwira

N’chiyani chimene chimachititsa kuti mano a nkhonoyi akhale olimba kwambiri kuposa ulusi wa kangaude?

Guluu wa Kanyama Kotchedwa Barnacle

Guluu wa kanyamaka amamata mwamphamvu kwambiri kuposa guluu aliyense wopangidwa ndi anthu. Posachedwapa, asayansi atulukira zimene zimathandiza kuti azimata kwambiri pamalo pamene pali madzi.

Ulusi wa Nkhono Yam’madzi

Nkhono zinazake zam’madzi zimamata kuzinthu pogwiritsa ntchito timaulusi. Kumvetsa mmene zimenezi zimathekera kungathandize anthu kupeza njira yabwino yomatira zinthu pakhoma kapena yolumikizira minyewa kumafupa.

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Zigobazi zimakhala zolimba kwambiri moti zimatha kuteteza nkhono zomwe zili mkati mwake.

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamasinthasintha Mtundu

Akatswiri akutengera kanyamaka kuti apange zovala zotha kusinthasintha mitundu mofulumira kwambiri.

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamawala Pofuna Kudziteteza

Kanyamaka kamawala osati n’cholinga choti kazioneka, koma pofuna kudziteteza.

Manja a Octopus Ndi Ogometsa Kwambiri

Akatswiri apanga makina ogwira ntchito ngati manja, omwe amachita zinthu zodabwitsa kwambiri, potengera octopus.

Chigoba Chomwenso Chimaona

Werengani kuti mudziwe zambiri za kachilombo ka m’madzi kameneka.

Mchira wa Kahatchi Kam’madzi

Onani chifukwa chake zinthu zochititsa chidwi zimene mchira wa kahatchi kam’madzi umachita, zingathandizire akatswiri opanga maloboti m’tsogolo muno.

Mutu Wogometsa wa Nsomba Yotchedwa Remora​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi n’chiyani chomwe chimathandiza kuti nsombayi isamagwe ikamatirira kuzamoyo zina zam’madzi?

Mbalame

Mbalame za Nthenga Zosasintha Mtundu

Kodi zimene zimachitika ndi nthenga za mbalamezi zithandiza bwanji akatswiri kupanga penti komanso zovala zosasuluka?

Mapiko a Kadzidzi

Asayansi akuona kuti mmene mapiko a kadzidzi anapangidwira, angawathandize kwambiri popanga zipangizo zoyendera mphepo kuti zisamachite phokoso zikamazungulira.

Mapiko a Mbalame Opindikira M’mwamba

Potengera mapiko a mbalame, akatswiri apanga ndege zabwino kwambiri. Zimenezi zinathandiza kupulumutsa malita okwana 7,600 miliyoni a mafuta padziko lonse m’chaka chimodzi chokha.

Nthenga za Mbalame Zochititsa Chidwi Kwambiri

Kodi akatswiri ofufuza nyama za m’madzi apeza zotani zokhudza nthenga za mbalame zimenezi?

Mbalame ya Albatross Yosatopa ndi Kuuluka

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chomwe chimathandiza mbalame zina kumauluka m’mwamba kwambiri komanso kwa nthawi yaitali koma osakupiza mapiko ake olo kamodzi.

Mbalame Yotha Kuuluka Ulendo Wautali

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe za mbalame inayake yogometsa kwambiri imene imayenda ulendo wautali masiku 8 okha.

Nyama Zokwawa

Gulo Wakhungu Lodabwitsa Kwambiri

Kodi zimatheka bwanji kuti guloyu azimwa madzi pongogunditsa mchira kapena miyendo yake m’madzi?

Mchira wa Gulo

Kodi gulo amatha bwanji kudumpha kuchoka pansi kupita pakhoma?

Nsagwada za Ng’ona

Ng’ona ikaluma, mphamvu zake tingaziyerekezere ndi mphamvu za kuluma kwa mkango ndiyeno n’kuziwirikiza katatu. Koma nsagwada za ng’ona zikakhudzidwa ndi zinazake ng’onayo imamva mwamsanga kuposa mmene munthu amamvera chala chikakhudzidwa. Kodi izi zimatheka bwanji?

Khungu la Njoka

N’chiyani chimapangitsa kuti khungu la njoka likhale lolimba kwambiri moti njokayo imatha kukwera mtengo waminga komanso kuyenda pa mchenga ukuluukulu?

Achule Amene Amaswa Modabwitsa Kwambiri

N’chifukwa chiyani anthu ena amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amanena kuti mfundo yakuti achulewa anachita kusintha mwa pang’onopang’ono ndi yosamveka?

Tizilombo

Kodi Zinangochitika Zokha? Mmene Njuchi Imaulukira

Kodi njuchi yaing’ono chonchiyi imatha bwanji kuuluka bwinobwino kuposa ndege yomwe oyendetsa ake ndi aluso kwambiri?

Njuchi Zimatera Mochititsa Chidwi

Kodi kudziwa zimene njuchi imachita ikamatera kungathandize bwanji popanga maloboti otha kuwaulutsa ndi kumawawongolera? Kodi akatswiri opanga maloboti otha kuuluka angaphunzire chiyani poona zimene njuchi imachita ikamatera?

Chisa cha Njuchi

Kodi njuchi zakhala zikudziwa zinthu zotani zokhudza kugwiritsa ntchito malo mosamala zomwe akatswiri a masamu azitulukira posachedwapa mu 1999?

Mmene Nyerere Zimapewera Kutchingirana Njira

Nyerere zimapewa kutchingirana njira. Kodi zimatheka bwanji?

Khosi la Nyerere

Kodi zimatheka bwanji kuti nyerere izinyamula zinthu zolemera kwambiri?

Luso la Nyerere Lopukuta Tinyanga Take

Kanyerere kameneka kamafunika kupukuta tinyanga take kuti kasafe. Kodi kamapukuta bwanji?

Nyerere Yokhala ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa

Nyerereyi ndi imodzi mwa nyama zimene zimatha kukhala m’malo otentha kwambiri omwe nyama zina sizingakhale. Kodi n’chiyani chimaithandiza kukhala m’malo oterewa?

Nyenje za Moyo Wautali

Nyenjezi ndi zodabwitsa kwambiri chifukwa zimaonekera kunja kwa milungu yochepa yokha pambuyo pa zaka 13 kapena 17.

Magiya a Kachilombo Kofanana ndi Nyenje

Magiyawo amathandiza kachilomboka kuti kazilumpha bwinobwino.

Chimene Chimachititsa Kuti Dzombe Lisamawombane Pouluka

Kodi n’chiyani chimathandiza dzombe kuti lisawombane likamauluka?

Khutu Lamphamvu la Bwamnoni

Bwamnoniyu ali ndi kakhutu kakang’ono kwambiri koma kamagwira ntchito ngati khutu la munthu. Kodi zimene akatswiri apeza zokhudza khutu la bwamnoniyu zingathandize bwanji asayansi komanso akatswiri opanga zinthu?

Luso la Agulugufe a Monarch Loyenda Ulendo Wautali​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi luso la agulugufe a monarch loyenda ulendo wovuta komanso wautali kwambiri limasonyeza kuti anachita kulengedwa?

Mapiko a Gulugufe

Pamwamba pa mapiko a gulugufe ameneyu pamaoneka posalala koma pali tizinthu tomwe mungathe kutiona mutagwiritsa ntchito chipangizo choonera zinthu zing’onozing’ono. Kodi tinthu timeneti n’chiyani?

Mapiko a Gulugufe Ndi Odabwitsa Zedi

Agulugufe ena ali ndi mapiko akuda amene amawathandiza kuti azimva kutentha. Koma palinso chinthu china chimene chimawathandiza

Luso la Gulugufe Woyera Lotha Kuimitsa Mapiko Ake Ngati V

Kodi ndi luso liti la gulugufe woyera limene lathandiza akatswiri pokonza mapanelo a sola abwino kwambiri?

Akadziwotche Omwe Amamva Kwambiri

Akadziwotchewa ali ndi timakutu tating’ono koma amamva kwambiri kuposa nyama ina iliyonse.

Tim’guza Ndowe Timachita Zogometsa

Kodi tim’guza ndowe tili ndi luso lotani? Kodi anthu angaphunzire chiyani kwa tizilomboti?

Kuwala kwa Ziphaniphani za Mtundu Winawake

Kodi tizilombo timeneti tathandiza bwanji asayansi kuganiza zopanga zipangizo zowala bwino?

Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche

Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche

Akangaude

Maso a Kangaude

Kodi kangaude ameneyu amatha bwanji kudziwa kutalika kwa mtunda umene akufuna kudumpha? N’chifukwa chiyani akatswiri akufuna kupanga zinthu potengera kangaudeyu?

Kangaude Wam’nyumba Amachita Zogometsa Kwambiri

Kangaude wam’nyumba amatulutsa ulusi umene umakhala womata kwambiri komanso wosamata kwambiri. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene zimenezi zimachitikira komanso chifukwa chake.

Zomera

Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo​—Kodi Zinangochitika Zokha?

Kodi asayansi akuganiza kuti angatani kuti atengere mmene chipatso cha pomelo chinapangidwira?

Tizipatso Tokongola Kwambiri ta Buluu

Tizipatso ta Pollia tilibe madzi alionse a buluu mkati mwake, koma timaoneka ta buluu wowala kwambiri ndipo palibenso zomera zina zomwe zimaoneka choncho. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti tizipatsoti tizioneka motere?

Zomera Nazonso Zimadziwa Masamu

Asayansi anachita kafukufuku pa zomera zinazake ndipo anapeza kuti zomerazi zimadziwa masamu kwambiri.

Tinthu Tosaoneka Ndi Maso

Kuchuluka kwa Zinthu Zimene DNA Imasunga

Werengani kuti mudziwe mmene DNA ilili chipangizo chapamwamba kwambiri chosungira zinthu.

Tizilombo Tomwe Timachotsa Mafuta

Kodi mabakiteriyawa angathandize bwanji kuchotsa mafuta poyerekeza ndi njira zamakono za asayansi