Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Ubweya wa Katumbu

Ubweya wa Katumbu

NYAMA zambiri zomwe zimakhala m’madzi ozizira kwambiri, zimakhala ndi mafuta ambiri pansi pa khungu lake, omwe amathandiza kuti zizimva kutentha. Koma pali katumbu wamtundu winawake yemwe sakhala ndi mafuta ambiri koma amadalira chikopa chake chomwe chimakhala ndi ubweya wambiri.

Taganizirani izi: Ubweya wa katumbuyu umakhala wambiri kusiyana ndi wanyama zina moti pakamalo ka 1 sentimita mulitali ndi mulifupi, pamatha kukhala ubweya wokwana 155,000. Akamasambira, ubweyawu umasungira mpweya womwe umathandiza kuti madzi ozizira asagunde khungu lake.

Akatswiri asayansi amaona kuti akhoza kupanga zinthu zambiri potengera mmene ubweya wa kanyamaka umagwirira ntchito. Mwachitsanzo, anapangapo zovala zingapo zokhala ndi ubweya wosiyana katalikidwe komanso kuchuluka kwake. Akatswiriwa anapeza kuti zovala zimene zinali ndi ubweya wochuluka komanso wautali sizinkalowa madzi mwachisawawa. Komabe zovala zimene akatswiriwa anapanga sizingafanane ndi ubweya wa katumbuyu.

Akatswiri asayansiwa akukhulupirira kuti kafukufuku amene anachitayu angawathandize kupanga zovala zatsopano zomwe sizingamalowe madzi. Anthu ena akukhulupirira kuti zovalazi zikhoza kuthandiza kuti akatswiri osambira azitha kusambira m’madzi ozizira kwambiri.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti katumbu akhale ndi ubweya wotere? Kapena pali winawake amene anamupanga?