Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tizipatso Tokongola Kwambiri ta Buluu

Tizipatso Tokongola Kwambiri ta Buluu

TIZIPATSO tina totchedwa Pollia tomwe timapezeka kwambiri ku Africa, timaoneka ta buluu wowala kwambiri ndipo palibenso zomera zina zomwe zimaoneka choncho. Chodabwitsa n’chakuti mkati mwa tizipatsoti mulibe timadzi tilitonse ta buluu. Ndiye kodi n’chiyani chimachititsa kuti tizipatsoti tizioneka ta mtundu umenewu?

Taganizirani izi: Maselo a khungu la tizipatsoti ali ndi tinthu ting’onoting’ono tooneka ngati timaulusi, tomwe tinayalidwa ngati timitengo tamacheso ndipo tinasanjikizana mochititsa chidwi. Timaulusiti si ta buluu ayi, koma kunyezimira kwa mtunduwu kumachitika chifukwa cha mmene timaulusiti tinasanjidwira. Tizipatsoti timaoneka ta buluu, koma kutionera m’mbali zosiyanasiyana, pena timaoneka ngati tobiriwira, tapinki kapenanso tachikasu. Komanso kutionera pafupi kwambiri, timaoneka ndi mitundu yosiyanasiyana pa nthawi imodzi.

Popeza kuti tizipatsoti sitikhala ndi madzi a buluu mkati mwake, timaonekabe tamtunduwu ngakhale tigwe pansi. Tizipatso tina tomwe tinatoledwa zaka 100 zapitazo timaonekabe towala ngati angotithyola kumene. Ofufuza anapeza kuti tizipatsoti timakopa mbalame zambiri chifukwa cha mtundu wake ngakhale kuti ndi tolimba moti mbalamezo sizingadye.

Asayansi akukhulupirira kuti potengera tizipatsoti, angathe kupanga nsalu zoti zisamasuluke komanso mapepala apamwamba opangira zinthu ngati ndalama.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tizipatsoti tizioneka ta mtundu wa buluu wokongola chonchi, kapena pali winawake amene anatilenga?