Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zinangochitika Zokha?

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

NKHONO zam’madzi zimakhala m’malo ovuta kwambiri pansi panyanja koma zimakhala motetezeka chifukwa cha zigoba zake zolimba. Izi zachititsa kuti akatswiri ena afufuze bwinobwino mmene zigobazi zinapangidwira n’cholinga choti apange magalimoto ndiponso nyumba m’njira yoti zizitha kuteteza anthu amene ali mkati mwake.

Taganizirani izi: Akatswiri anafufuza mitundu iwiri ya zigoba za nkhonozi kuti aone mmene zinapangidwira.

Mtundu woyamba wa zigobazi umaoneka ngati ambulela. Akatswiriwa anapeza kuti zigoba zake ndi zolimba kwambiri pamwamba komanso mphepete mwake. Zigoba za mtundu wachiwiri ndi zolimba pakati ndi kukamwa kwake. Mbali zolimba kwambiri za mitundu iwiri yonseyi zimathandiza kuti zigobazi zisamasweke mwachisawawa ndipo nkhono zimakhala motetezeka.

Akatswiri ena anachitanso kafukufuku kuti asiyanitse kulimba kwa zigoba za nkhonozi ndi zipangizo zina zofanana ndi zigobazi zomwe anthu anapanga pogwiritsa ntchito makina otchedwa 3-D printer. Koma anapeza kuti zigobazi ndi zolimba kwambiri moti sizingaphwanyike mwansanga kuyerekeza ndi zipangizo zomwe anapangazo.

Ponena za kafukufuku amene anachitikayo magazini ina inati: “Ngati anthu atapanga galimoto potengera zigoba za nkhonozi, galimotoyo idzakhala yokongola kwambiri komanso izidzathandiza kuti anthu omwe akwera akhale otetezeka.”​—Scientific American.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti zigoba za nkhonozi zikhale zolimba? Kapena pali winawake amene anazilenga?