Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Unabadwa kwa Makolo Oyera Kuposa Onse”

“Unabadwa kwa Makolo Oyera Kuposa Onse”

“Unabadwa kwa Makolo Oyera Kuposa Onse”

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU BRAZIL

MCHERE umatchulidwa kuti “unabadwa kwa makolo oyera kuposa onse, omwe ndi dzuwa ndi nyanja.” Indedi, mchere kawirikawiri umapangidwa kuchokera kumadzi a m’nyanja ya mchere omwe auma ndi kutentha kwa dzuwa.

Mzinda wa ku Brazil wotchedwa Rio Grande do Norte, womwe uli kumpoto chakum’mawa kwa dzikolo, n’ngotchuka chifukwa cha malo ake opangira mchere. Ndipo nyengo yotentha kwambiri, mvula yochepa, ndi mphepo yomwe imaomba nthawi zonse kuderalo, zimathandiza kuti anthu azipanga mchere poumitsa madzi ndi kutentha kwa dzuwa. Ndipotu 95 peresenti ya mchere wonse wa ku Brazil, wosayengedwa ndi woyengedwa womwe, umachokera kudera limeneli. Amodzi mwa malo opangira mcherewa ali ku Areia Branca, womwe ndi mzinda waung’ono wa mphepete mwa nyanja.

Kukaona Malo Opangira Mchere

Malo opangira mchere nthawi zambiri amakhala aakulu ndithu, monga mmene zilili ndi ku Areia Branca. Alendo akamadutsa mumsewu waukulu n’kumayandikira Areia Branca, amadabwa kwambiri ndi kukula kwa malo opangirako mcherewa. Ndipo m’mawa dzuwa likamatuluka kumene, madzi opangira mchere omwe amakhala m’maiwe ambirimbiri, amathobwa m’maso. Maiwewa alipo ambirimbiri moti amaoneka ngati pamene anathera sipakuoneka. Pafupifupi 90 peresenti ya malo amenewa kuli maiwe oumitsira madzi, ndipo malo otsalawo amawagwiritsa ntchito pokonza mcherewo kuti ukhale mibulu.

Malo onsewo ndi okutidwa ndi mchere wokhawokha, womwe umathobwa m’maso kwambiri. N’chifukwa chake muyenera kuvala magalasi oteteza ku dzuwa mukamapita kumalo amenewa. Popanga mcherewu, choyamba amapatutsa madzi a m’nyanja n’kuwadutsitsa m’maiwe angapo osaya, amene amalekanitsidwa ndi ziunda zokhala ndi makomo olowera ndi kutulukira madzi, ndipo makomowo amatsekedwa ndi zitseko zamatabwa. Kumalo amenewa kuli maiwe okwana 67. Ndipo madzi okwana malita 650 amaphwera pa sekondi iliyonse m’maiwe amenewa chifukwa cha kutentha kwa dzuwa ndiponso mphepo! Komabe, zimatenga masiku 90 mpaka 100 kuti madzi onse aphwere.

Ngakhale kuti madziwo akamaphwera amasiya mchere umene timadya m’maiwemo, madzi a m’nyanja amakhalanso ndi michere ina ya mitundumitundu. Michere imeneyi imachoka m’madziwo panthawi zosiyanasiyana, ndipo imaunjikana m’mizeremizere pansi pa maiwe.

Kuchokera m’maiwe amenewa, madzi amcherewo amawapatutsira ku maiwe ena okwana 20 oumitsira mchere. Ndipo mu ena mwa maiwe amenewa, madziwo amaphwereratu n’kusiya thanthwe lalikulu la mchere. Ndiyeno amagwiritsa ntchito thalakitala yaikulu pophwanya mcherewo ndi kuupakira m’galimoto zikuluzikulu. Galimoto zimenezi zimakakhuthula mcherewo kunyumba zazitali zooneka ngati nkhokwe zachimanga. Kumalo amenewa n’kumene amatsukira mcherewo, ndipo ukauma, amautsukuluza ndi madzi abwino opanda mchere.

Kenaka, mcherewo amautenga pa mabwato ang’onoang’ono n’kupita nawo kudoko la pachilumba chochita kupanga cha ku Areia Branca. Pali makilomita 12 kuchokera kumtunda kukafika pa chilumba chimenechi. Chilumbachi ndi chamakona anayi, ndipo n’chotalika mamita 166 m’litali, ndi mamita 92 m’lifupi, ndipotu pangasungidwe mchere wokwana matani 100,000. Ndiyeno mcherewo amaunyamula pa makina onyamulira katundu n’kuupititsa panyanja, n’kukaupakira mu sitima zapanyanja n’kupita nawo ku madera osiyanasiyana a ku Brazil.

Umagwira Ntchito Zambiri Zofunika

Ngakhale kuti matupi athu amafuna mchere wochepa kwambiri, komabe mchere n’ngofunika kuti thanzi lathu komanso la zinyama likhale labwino. Mwina mchere timangowuona ngati zinthu zoyera zimene zimakometsa zakudya basi. Komatu mchere umathandiza pantchito zopanga mankhwala, nsalu, ndi zitsulo. Mchere umagwiritsidwanso ntchito popanga sopo, vanishi, ndi penti ya ziwiya zadothi. Masiku ano, akuti pali ntchito zodziwika zoposa 14,000 zimene mchere umagwira!

Zikuoneka kuti mchere sungathe m’nyanja. Madzi olemera makilogalamu 100 amakhala ndi mchere wolemera makilogalamu atatu. Komabe, m’nthawi ya m’mbuyomu, mchere sunkapezeka wamba. Mwachitsanzo, kale kwambiri ku China, chinthu chodula kuposa mchere chinali golide yekha basi. Baibulo limatchulanso za mchere nthawi zambirimbiri ndiponso limasonyeza ntchito zake zosiyanasiyana.

Nthawi zina ana obadwa kumene ankawasisita ndi mchere, mwina pofuna kuwateteza ku tizilombo toyambitsa matenda. (Ezekieli 16:4) Baibulo limanenanso za mchere m’njira yophiphiritsa. Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake kuti iwo ndi “mchere wa dziko lapansi.” Iye anatero chifukwa ophunzira akewo anali ndi udindo wothandiza anthu ena ndi uthenga wopatsa moyo umene ankalalikira. (Mateyo 5:13) Mchere unalinso chizindikiro cha zinthu zokhazikika ndi zosasunthika. Choncho “pangano lamchere” linali pangano losasweka.—Numeri 18:19.

Ulendo wathu wokacheza kumalo opangira mchere a Areia Branca, unatithandiza kuzindikira zambiri zokhuza kufunika ndi kudalirika kwa mchere, ndiponso tinamvetsa bwino chifukwa chake wakhala wofunika kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Ndithudi, tikuyamikira kwambiri kuti mchere, womwe “unabadwa kwa makolo oyera kuposa onse, omwe ndi dzuwa ndi nyanja,” ukupezeka wambiri chonchi.

[Chithunzi patsamba 16]

Thalakitala yochotsa mchere ili padziwe loumitsira mchere

[Chithunzi patsamba 16]

Mchere usanatsukidwe

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Malo otsukira, kutsukuluzira, ndi kusungira mchere