Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Calypso Nyimbo Zamakolo za ku Trinidad

Calypso Nyimbo Zamakolo za ku Trinidad

 Calypso Nyimbo Zamakolo za ku Trinidad

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU TRINIDAD

KODI anthu amaganizira za chiyani akamva za dziko lopangidwa ndi zilumba ziwiri la Trinidad ndi Tobago? Ambiri amaganizira za gulu la anthu oimba nyimbo za zing’wenyeng’wenye kapena kaimbidwe kokoma ka nyimbo za calypso. Nyimbo za calypso zili ndi kaimbidwe kakekake kaluso ndi kokoka mtima kwambiri. N’chifukwa chake kusiyapo komwe zinayambira, kum’mwera kwa nyanja ya Caribbean, nyimbozi zafalikiranso kumayiko ena akutali. *

Malinga ndi buku lakuti calypso Calaloo, dzina lakuti calypso limatanthauza “nyimbo zonse zimene pambuyo pa chaka cha 1898 zinkaimbidwa pa zikondwerero za carnival ku Trinidad, kaya zinkaimbidwa m’misewu ndi anthu oledzera kapenanso kumalo oyimbirako nyimbo komwe nyimbozi zinkaimbidwa mokoma ndi oimba wamba kapena akatswiri.” Zikukhala ngati nyimbo za calypso zinayambira ku nthano za anthu a ku Africa zomwe zinafika ku Trinidad ndi akapolo ochokera ku Africa. Kenako, anadzaziphatikiza ndi mbali zabwinozabwino za kaimbidwe, kavinidwe komanso ng’oma za ku Africa, n’kuzisakanizanso ndi mbali zina za nyimbo za ku France, ku Latin America, ku England, ndi mayiko ena, msakanizo wabwino kwambiri womwe potsirizira pake unabala nyimbo za calypso.

Koma chiyambi cha dzina lakuti calypso ndiye sichimadziwika bwinobwino. Ena amati dzinali linachokera ku mawu a kumadzulo kwa Africa, akuti kaiso, omwe kawirikawiri ankawanena poyamikira munthu akaimba bwino kwambiri nyimbo. Ngakhale kalelo ukapolo usanathe ku Trinidad ndi Tobago m’zaka za m’ma 1830, anthu ankasonkhana pa zikondwerero za carnival kukamvetsera oimba akuonetsa luso lawo komanso akunyozana kudzera mu nyimbo. Kuti adziwike bwino, oimba nyimbo za calypso ambiri ankadzipatsa dzina lina ndipo ankakhala ndi kaimbidwe kawokawo komwe ankadziwika nako.

Kaimbidwe Kake ndi Mmene Nyimbo za Calypso Zimakhudzira Anthu

Kwa zaka zambiri, anthu oimba nyimbo za calypso akhala akulemekezedwa chifukwa cha nthabwala zawo. Ambiri a iwo, ali ndi luso lopeka mosavuta mawu omveka mofananafanana ngati ndakatulo, akumawakometsera mwanjira yoti munthu n’kumakhala ngati akuona zimene akumvazo, uku akutsatana bwino kwambiri ndi nkhani yonse ya m’nyimbozo. Kuchiyambi kwenikweni,  oimba nyimbo za calypso ankakhala anthu osauka a ku Trinidad komweko koma omwe makolo awo oyambirira anachokera ku Africa, pamene masiku ano amakhala anthu a mtundu kapena a khungu lililonse, osauka ndi olemera omwe.

Dr. Hollis Liverpool, mkulu wakale wa zachikhalidwe m’dziko la Trinidad ndi Tobago, yemwenso ndi katswiri wa mbiri yakale komanso woimba nyimbo za calypso, pothirira ndemanga pa oimba akale a nyimbo za calypso anauza Galamukani! kuti: “Ukatswiri wawo unagona pa nthabwala, chifukwa kwenikweni anthu ankapita kokamvera nyimbo za calypso kuti akasangalale, ndi kukamva mphekesera komanso kukatsimikizira zinthu zimene akhala akuzimva m’malo mongomva zam’maluwa. Anthu ochokera m’mabanja a pamwamba ankakamvera nyimbozi n’cholinga chokaona zimene anthu ochokera m’mabanja otsika amachita, pamene nduna ndi otsatira awo amapitako n’cholinga chokaona ngati anthu akuwakondabe pandale.”

Nthawi zambiri anthu oimba nyimbo za calypso ankanyoza ndi kunyogodola akuluakulu a boma ndi anthu ochokera m’mabanja a pamwamba. N’chifukwa chake anthu oimba nyimbo za calypso ankalemekezedwa n’kutengedwa ngati anthu omenyera ufulu wa anthu osauka, koma anthu olamulira ankawatenga anthu oimbawo ngati anthu ovuta. Oimba nyimbo za calypso ambiri ankaimba nyimbo zotsutsana ndi boma la chitsamunda ndipo zimenezi zinachititsa kuti kukhazikitsidwe lamulo loyang’anira mmene nyimbozi zikuimbidwira. Pothawa zimenezi, oimba anayamba kuimba nyimbozi m’mawu okuluwika okhala ndi matanthauzo awiri, ndipo ena anali akatswiri kwambiri paluso limeneli. Mpaka pano nyimbo za calypso zimadziwika bwino chifukwa cha mawu ake okuluwika.

Kuwonjezera pa kugwiritsa ntchito mawu omwe analipo kale, oimba nyimbo za calypso, ankayambitsanso mawu atsopano. N’chifukwa chake ku West Indies kuli mawu ambiri ndithu amene anthu amakonda kuwagwiritsa ntchito pocheza omwe anayambira ku nyimbo za calypso. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri, ngakhale andale, amakonda kutchula mawu a m’nyimbo za calypso akafuna kutsindika mfundo zawo.

Nyimbo Zamakono za Calypso

Masiku ano kwabadwa mitundu yosiyanasiyana ya nyimbo za calypso, zina zosakanikirana ndi nyimbo za mitundu ina, zomwe anthu amitundu yosiyanasiyana akukonda kumvera. Monga mmene zililinso ndi nyimbo za mitundu ina, nyimbo zina za calypso sizilimbikitsa makhalidwe abwino. Mwachidziwikire tifunika kusamala ndi zinthu zimene timamvetsera. (Aefeso 5:3, 4) Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingachite manyazi kufotokoza mawu okuluwika a m’nyimbo za calypso kwa ana anga kapena kwa munthu amene sazidziwa bwinobwino nyimbozi?’

Sitikukayika kuti ngati mutabwera ku dziko la Trinidad ndi Tobago, mudzasangalala kuona magombe ndi miyala ya m’madzi zokongola kwambiri ndipo mudzachita chidwi ndi msakanizo wokongola wa mitundu ya anthu ndi zikhalidwe zawo. Mungasangalalenso kumvetsera nyimbo za zing’wenyeng’wenye komanso nyimbo za calypso, nyimbo zokoka mtima kwambiri zomwe zadolola mitima ya ana ndi akulu omwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nthawi zambiri magulu oimba nyimbo za zing’wenyeng’wenye akamaimba nyimbo za calypso saimba ndi mawu omwe, koma oimba amawu amakonda kugwiritsa ntchito zida monga gitala, lipenga, chitoliro, ndi ng’oma.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Ng’oma zachitsulo