Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Umene Adzabweretse

Moyo Umene Adzabweretse

 Moyo Umene Adzabweretse

“TAONANI! Mfumu idzalamulira m’chilungamo.” Maulosi osangalatsa ngati amenewa onena za ulamuliro wa Ufumu wa Yesu ali mbali yofunika kwambiri ya Baibulo. Ulosi wina wofanana ndi umenewo umati: “Adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. . . . Mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”—Yesaya 32:1; Salmo 72:12-14.

Kodi alipo amene angatsutse zoti anthu padziko lonse lapansi akufunikira ulamuliro wolungama woterowo? Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti asaiwale Ufumu wa Mulungu. Iye anawaphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”—Mateyo 6:9, 10.

Umboni Woti Ufumu wa Mulungu Wayandikira

Kodi tingadziwe bwanji nthawi imene Ufumuwo udzabwere kuti pemphero lija liyankhidwe? Ophunzira oyambirira a Yesu anafunitsitsa kudziwa ndipo anafunsa kuti: “Kodi chizindikiro cha kukhalapo kwanu [monga Mfumu yolamulira] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” Yesu anayankha kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina . . . , ndiponso kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Zonsezi ndi chiyambi cha masautso.” Ndipo iye anachenjezanso kuti: “Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, ochuluka chikondi chawo chidzazirala.”—Mateyo 24:3-12.

Ulosi winanso wa m’Baibulo umati “m’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.”—2 Timoteyo 3:1-5.

Mungavomereze ndithu kuti zochitika za “m’masiku otsiriza” zimene zalongosoledwazi zikugwirizana ndendende ndi zomwe zikuchitika m’nthawi yathu ino. Pali umboni wochuluka wotsimikizira kuti ino ndiyo nthawi yoti ulosi wa m’Baibulo wotsatirawu ukwaniritsidwe: “Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Ulamuliro wa Ufumu wotsogozedwa ndi “Kalonga Wamtendere” udzachotsa chilichonse chimene chingasokoneze mtendere wa anthu amene adzapulumuke mapeto a dzikoli. (Yesaya 9:6) Ulosi wa m’Baibulo umalonjeza kuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.” (1 Yohane 2:17) Mapeto a dzikoli adzapereka mwayi kwa anthu ochita chifuniro cha Mulungu kuti asangalale ndi madalitso amene makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava anataya pamene anapandukira Mulungu.

 Moyo Umene Wayandikira

“Panthawi ya kukonzanso zinthu, Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wachifumu wa ulemerero,” anatero Yesu. (Mateyo 19:28) Kodi mawu oti “kukonzanso zinthu” akutanthauzanji? Baibulo lina limati, “kulenganso zinthu zonse.” (New International Version) Nkhani ina ya m’Baibulo yofanana ndi yomweyi imanena kuti “dongosolo la zinthu likubweralo.” (Luka 18:30) Panthawi imeneyo, Yesu adzagwiritsira ntchito ulamuliro wake wopatsidwa ndi Mulungu monga Kalonga Wamtendere mwa kupereka moyo wosatha kwa onse okhulupirira nsembe yake ya dipo.—Yohane 5:21.

M’dongosolo la zinthu latsopano la Mulungu, anthu adzasangalala ndi moyo wofanana ndi umene Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava pamene anawaika m’Paradaiso padziko lapansi. Kumbukirani kuti Mulungu anawalangiza kuti abereke ana, inde, ‘adzadze dziko lapansi ndi kuligonjetsa.’ Ntchito yawo inali yoti afutukule Paradaiso wa mu Edene kufika padziko lonse lapansi! (Genesis 1:28) Chimodzimodzinso, panthawi ya kukonzanso zinthu, padziko lapansi pano padzadzadza anthu opulumuka mapeto a dzikoli, ana awo, ndiponso anthu oukitsidwa kwa akufa. Ntchito ya anthu amenewa idzakhala yothandiza kukonzanso dziko kuti likhale paradaiso, monga mmene Mulungu anafunira poyamba.

Taonani ena mwa madalitso amene Baibulo limasonyeza kuti anthu adzasangalala nawo m’dziko latsopano lachilungamo.—2 Petulo 3:13.

 Ngakhale kuti malonjezo amene afotokozedwa pa masamba ano angaoneke ngati osatheka, adzakwaniritsidwa ndithu mu “dongosolo la zinthu lomwe likubwerali.” Popemphera kwa Mulungu, Yesu analongosola zimene anthu ayenera kuchita kuti adzalandire madalitso amenewa, pamene anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yohane 17:3) Inuyo mukhaletu mmodzi mwa anthu amene akufunafuna modzichepetsa kudziwa mfundo zopatsa moyo zimenezi.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]

Aliyense Adzakhala ndi Nyumba ndi Ntchito

“Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

Anthu Onse Adzakhala ndi Chakudya Chochuluka

“Dziko lapansi lapereka zipatso zake.” “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.”—Salmo 67:6; 72:16.

Mtendere wa Padziko Lonse Udzakhudza Ngakhale Nyama

“Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; . . . ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”—Yesaya 11:6.

Nkhondo Idzathetsedwa, Mtendere Sudzatha

“Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 2:4; 9:7.

Okondedwa Athu Amene Anamwalira Adzaukitsidwa

“Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Sikudzakhalanso Matenda Kapena Imfa

“Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” “Imfa sidzakhalaponso . . . Zakalezo zapita.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.