Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

 Kodi Mungayankhe Bwanji?

ZINACHITIKIRA KUTI?

1. Kodi Yesu anabadwira kuti?

Lembani mzere kuzunguliza mayankho anu pa mapupa.

Betelehemu [Zebuloni]

Nazarete

Yerusalemu

Betelehemu (Efrata)

◆ Kodi zikuoneka kuti Yesu anabadwa liti?

․․․․․

◆ Kodi openda nyenyezi amene anakaona Yesu analipo angati?

․․․․․

◆ Kodi ndani anatsogolera nyenyezi zimene zinalondolera openda nyenyezi popita kwa Yesu?

․․․․․

Kambiranani: Kodi n’koyenera kukondwerera kubadwa kwa Yesu pa December 25? Perekani zifukwa zake.

ZINACHITIKA LITI?

Lembani mzere kulumikiza chochitika chilichonse ndi chaka choyandikana kwambiri ndi chaka chomwe chinachitikira.

706 B.C.E. 607 537 455 66 C.E. 70

2. Nehemiya 2:5-8, 18

3. 2 Mafumu 25:8-10

4. Luka 21:20, 21

NDINE NDANI?

5. Ndinakhala wosalankhula chifukwa chakuti ndinakayikira Gabrieli.

NDINE NDANI?

6. Ndine mneneri wamkazi amene anakumana ndi Yesu pa kachisi.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 11 Kodi makolo amene amakhazikitsa malamulo abwino amatsatira Yehova m’njira yotani? (Salmo 32:․․․)

Tsamba 12 Kodi munthu wopusa amatulutsa chiyani? (Miyambo 29:․․․)

Tsamba 17 Kodi n’chinthu chotani chimene chinagwiritsidwa ntchito ngati chizindikiro cha pangano losasweka? (Numeri 18:․․․)

Tsamba 18 Kodi chifukwa chimodzi chimene tiyenera kukhalira osamala ndi mowa n’chiti? (Yesaya 5:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 22)

 MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Betelehemu (Efrata).

◆ Mwezi wa Etanimu (September/October) 2 B.C.E.

◆ Nambala yake sikudziwika.

◆ Ayenera kukhala Satana.

2. 455 B.C.E.

3. 607 B.C.E.

4. 66 C.E.

5. Zakariya.—Luka 1:18-23.

6. Anna.—Luka 2:36-38.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Bottom circle: ‘The Donkey Sanctuary’, Sidmouth, Devon, UK