Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinali Mwana Wolowerera

Ndinali Mwana Wolowerera

Ndinali Mwana Wolowerera

Yosimbidwa ndi Meros William SUnday

Ndinaphunzitsidwa kukonda Mulungu kuyambira ndili khanda, koma nditafika zaka 18, ndinapanduka n’kuchoka panyumba. Kwa zaka 13, ndinakhala ndi moyo wofanana ndi wa mwana wolowerera wa m’fanizo la Yesu. (Luka 15:11-24) Ndinayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo moyo wanga unatsala pang’ono kuwonongekeratu. Tadikirani ndikuuzeni chimene chinandichititsa kuti ndisinthe moyo wanga n’kubwereranso.

NDINABADWIRA m’banja lachikhristu m’chaka cha 1956, ndipo ndine mwana wachiwiri mwa ana 9. Tinkakhala ku Ilesha, tauni yomwe ili kum’mwera chakumadzulo kwa Nigeria. Bambo anga anakulira m’banja lachikatolika, koma mu 1945 anapatsidwa buku lotchedwa Zeze wa Mulungu * ndi amalume awo. Atamaliza kuliwerenga, bambo anafufuza Mboni za Yehova. Mu 1946, iwo anabatizidwa, ndipo patapita nthawi yochepa, nawonso mayi anabatizidwa.

Ndimakumbukirabe mpaka pano mmene Yehova analili weniweni kwa ine m’masiku a ubwana wanga ndiponso mmene ndinalili wachangu polalikira pamodzi ndi makolo anga. Bambo anga ankaphunzira nane Baibulo. Nthawi zina, Alice Obarah, amene mwamuna wake anali woyang’anira dera wa m’dera lathu, ankaphunziranso nane. Makolo anga ankafuna kuti ndidzakhale mtumiki wanthawi zonse. Komabe, amayi anaganiza kuti ndiyambe ndapita kaye kusukulu ya sekondale.

Koma nditangoyamba kumene sukuluyo, ndili ndi zaka 16, mopanda nzeru ndinayamba kucheza ndi anzanga amene sankatsatira mfundo za m’Baibulo. Ndinachita zinthu zopusa bwanji! Posapita nthawi, ndinayamba kusuta ndiponso kuchita zachiwerewere. Ndinazindikira kuti moyo wanga watsopanowu n’ngosagwirizana ndi malangizo amene ndinkamva ku misonkhano yachikhristu, choncho ndinasiya kusonkhana ndiponso kulalikira kunyumba ndi nyumba. Makolo anga zinawapweteka kwambiri, komabe panthawi imeneyi sindinkasamala za aliyense.

Ndinachoka Panyumba

Zaka ziwiri zokha zitatha chiyambireni maphunziro a ku sekondale, ndinachoka panyumba pathu ndipo ndinayamba kukhala ndi anzanga ena a m’dera lathu lomwelo. Nthawi zina ndinkabwera kunyumba kwathu mozemba, n’kuba chakudya chilichonse chimene ndapeza, kenaka n’kuthawa. Bambo atathedwa nane nzeru, anasiya kundilipirira sukulu, poganiza kuti ndisintha moyo wanga.

Komabe, chapanthawi yomweyo, ndinapeza mwayi wolipiriridwa sukulu ndi munthu wina wakunja. Munthuyo ankanditumizira ndalama zolipirira sukulu kuchokera ku Scotland ndipo nthawi zina ankanditumiziranso mphatso, kuphatikizapo ndalama. Panthawi imeneyi, awiri mwa azichimwene anga nawonso anasiya kusonkhana ndi Mboni za Yehova, zimene zinabweretsa chisoni chosaneneka kwa makolo anga. Nthawi zambiri, amayi ankandidandaulira kuti ndisinthe uku akulira. Ngakhale kuti zimenezi zinkandimvetsa chisoni, sindinasinthe khalidwe langa.

Kumizinda Ikuluikulu

Nditamaliza sukulu mu 1977, ndinapita ku Lagos ndipo ndinayamba ntchito. Pasanapite nthawi yaitali, ndinapeza ndalama mwachinyengo ndipo ndinagula galimoto ya takisiyi. Popeza ndinkakhala ndi ndalama zambiri tsopano, ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kuthera nthawi yaitali ku mabala ndi kunyumba za mahule. Kenaka, moyo wa ku Lagos unanditopetsa, ndipo mu 1981 ndinasamukira ku London. Kuchokera kumeneko ndinapita ku Belgium, kumene ndinayamba sukulu yophunzira Chifalansa ndiponso ndinkagwira ntchito mu lesitilanti. Komabe, nthawi yanga yambiri inkathera n’kutumiza magalimoto ndiponso zipangizo za magetsi zogulitsa ku Nigeria.

Bambo analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Belgium n’kupempha kuti andifufuze n’cholinga choti andiyambitse phunziro la Baibulo. Koma a Mboniwo ankati akangofika panyumba panga, ndin’kawathamangitsa. Ndinayamba kupita ku tchalitchi chinachake kumene tinkadya, kumwa, ndi kusewera masewero osiyanasiyana tikamaliza mapemphero.

Moyo Wogulitsa Mankhwala Osokoneza Bongo

Mu 1982, ndinatumiza galimoto yapamwamba kwambiri ku Nigeria ndipo ndinapita kudoko kuti ndikalowetse ndekha galimotoyo m’dzikolo. Akuluakulu a kasitomu a ku Nigeria anazindikira kuti kalata yanga yosonyeza kuti ndalipira kale msonkho wa galimotoyo inali yachinyengo, choncho anandiika m’ndende kwa masiku 40. Koma bambo anga anandilipirira belo ndipo ndinatuluka. Popeza ndinkafuna ndalama zoti ndimalize kulipirira mlandu wangawo, ndinabwerera ku Belgium ndi katundu wina woti ndikagulitse, kuphatikizapo makilogalamu angapo a chamba. Nditamaliza kulipira mlanduwo ku kasitomu, ndinakhazikika m’ntchito yogulitsa mankhwala osokoneza bongo.

Ndili paulendo winawake, ndinamangidwa m’dziko la Netherlands. Akuluakulu oona za anthu olowa m’dzikolo ananditumiza kwathu pondikweza ndege yomwe inkapita ku Nigeria. Paulendowo, ndinakumana ndi anthu ena ogulitsa mankhwala osokoneza bongo, ndipo tinapanga gulu logulitsa mankhwalawo. Mu January 1984, ndinasamukira ku dziko lina la ku Africa. Popeza ndimatha kulankhula Chifalansa, chinenero chomwe chimalankhulidwa kumeneko, sindinachedwe kupanga ubwenzi ndi apolisi, asilikali, ndi akuluakulu oona za anthu olowa m’dzikolo. Choncho, tinakwanitsa kulowetsa m’dzikolo chamba cholemera makilogalamu masauzande ambiri.

Kumangidwa N’kuikidwa M’ndende

Kenaka ndinagweranso m’mavuto. Ndinagwirizana ndi mkulu wa asilikali kuti andithandize kulowetsa mankhwala anga m’dzikolo. Koma anafika mochedwa ku bwalo la ndege, choncho ndinamangidwa. Apolisi anandimenya ndi kundizunza kwambiri, mpaka ndinakomoka. Ananditengera kuchipatala n’kundisiya komweko, akumaganiza kuti ndifa. Koma sindinafe, ndipo kenaka ananditengera kukhoti, kundiimba mlandu, ndi kundiika m’ndende.

Panthawi imene ndimatuluka m’ndende, mnzanga wina amene ndinam’pempha kuti aziyang’anira nyumba yanga anali atagulitsa katundu wanga yense n’kuthawa. Nthawi yomweyo ndinayambiranso kugulitsa chamba kuti ndithe kupeza zofunika za pamoyo. Koma patangotha masiku 10 okha chitulukireni m’ndende, ndinamangidwanso n’kuikidwa m’ndende kwa miyezi itatu. Panthawi imene ndinatulutsidwa ku ndende, ndinali ndikudwala kwambiri ndipo ndinatsala pang’ono kumwalira. Komabe, ndinayesetsa kudzilimbitsa mpaka ndinabwerera ku Lagos.

Kuyambiranso Ntchito Yanga ija

Ku Lagos, ndinakumana ndi anzanga ena ndipo tinapita ku India, komwe tinakagula mankhwala osokoneza bongo otchedwa heroin a ndalama zokwana madola 600,000. Kuchoka ku Bombay (kumene tsopano kumatchedwa Mumbai) tinapita ku Switzerland, kenaka ku Portugal, ndipo pomaliza tinapita ku Spain. Tinapeza ndalama zambiri ndithu, ndipo tinabwerera ku Lagos, podzera njira zosiyana. Chakumapeto kwa 1984, ndinagulitsanso mankhwala ena osokoneza bongo. Cholinga changa chinali choti ndipeze ndalama zokwana madola 1 miliyoni, kenaka n’kukakhala ku United States.

Mu 1986, ndinasonkhanitsa ndalama zanga zonse n’kugula mankhwala a heroin osaphatikizidwa ndi chilichonse ku Lagos. Mankhwalawo ndinapita nawo ku dziko lina, koma anafikira m’manja mwa munthu wina wadyera yemwe anangowatenga osandipatsa ndalama. Poopa kuphedwa, ndinabwerera ku Lagos koma sindinanene chilichonse chokhudza zomwe zinandichitikirazo. Panthawi imeneyi ndinalibiretu ndalama ndipo ndinavutika maganizo kwambiri. Kwa nthawi yoyamba, ndinakhala pansi ndi kusinkhasinkha za cholinga cha moyo wanga. Ndinadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani zinthu zikumangosokonekera chonchi pamoyo wanga?’

Kubwerera kwa Mulungu

Patapita nthawi yochepa, tsiku linalake usiku ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Ndiyeno, m’mawa wotsatira mwamuna wina wachikulire pamodzi ndi mkazi wake anagogoda pa chitseko changa. Anali a Mboni za Yehova. Ndinamvetsera mwachidwi ndipo ndinalandira magazini. Ndinawauza kuti, “Makolo anga ndi Mboni za Yehova, ndipo Alice Obarah ankaphunzira nane Baibulo.”

Mwamuna wachikulireyo, P. K. Ogbanefe, anayankha kuti: “Tikulidziwa bwino banja la a Obarah. Pakalipano likutumikira pa ofesi yathu ya nthambi ku Nigeria kuno, ku Lagos.” A Ogbanefe ndi akazi awo anandilimbikitsa kuti ndikaonane ndi banja la a Obarah. Kukumana ndi banja la a Obarah, kunandilimbikitsa kwambiri. Pambuyo pake, mbale Ogbanefe anayamba kuphunzira nane Baibulo, ndipo ndinayamba kusintha mwachangu moyo wanga woipa. Zimenezi sizinali zophweka chifukwa ndinakhala ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kwa nthawi yaitali ndipo zinali zovuta kusiya. Komabe, ndinatsimikiza kusiyiratu makhalidwe oipa.

Komatu panali ziyeso zambiri! Anzanga akale aja ankabwera kawirikawiri kunyumba kwanga n’kumandinyengerera kuti ndiyambirenso khalidwe langa lija. Moti kwakanthawi ndithu, ndinayambiranso kusuta ndiponso khalidwe loipa. Ndinakhuthula nkhawa za mumtima mwanga kwa Mulungu m’pemphero. Kenaka, ndinazindikira kuti popeza anzanga a kudziko ndi amene anandipatutsa, iwo sangandithandize tsopano. Ndinazindikira kuti, kuti ndipite patsogolo mwauzimu, ndiyenera kuchoka ku Lagos. Koma ndinkachita manyazi kubwerera kwathu ku Ilesha. Komabe, patapita nthawi ndinalemba kalata kwa bambo ndi mkulu wanga, n’kuwafunsa ngati angandilole kuti ndibwerere kunyumba.

Bambo ananditsimikizira kuti ndine wolandiridwa, ndipo mkulu wanga anandiuza kuti azindithandiza kumbali ya zachuma. Choncho ndinabwerera kunyumba, patatha zaka 10 chiwasiyireni makolo anga. Anandilandira mwansangala. Amayi anafuula kuti, “Zikomo Yehova!” Bambo atafika madzulo a tsiku limenelo, ananena kuti, “Yehova akuthandiza.” Bambo anapemphera kwa Yehova pamodzi ndi banja lonse, kupempha kuti andithandize tsopano popeza ndabwerera kuti ndichite chifuniro chake.

Kubwezeretsa Nthawi Imene Ndinawononga

Ndinayambiranso phunziro la Baibulo ndipo ndinapita patsogolo kwambiri, moti ndinabatizidwa pa April 24, 1988. Nthawi yomweyo, ndinakhala wachangu kwambiri mu utumiki. Pa November 1, 1989, ndinayamba kutumikira monga mpainiya, mlaliki wanthawi zonse. Mu 1995, ndinaitanidwa kukalowa nawo kalasi ya nambala 10 ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Nigeria. Ndiyeno, mu July 1998, ndinakhala woyang’anira woyendayenda, n’kumachezera mipingo ya Mboni za Yehova. M’chaka chotsatira, ndinadalitsidwa chifukwa ndinapeza Ruth, amene anakhala mkazi wanga ndiponso mnzanga wotumikira naye pa ntchito yanga yoyendayenda.

Anthu ena a m’banja lathu nawonso apita patsogolo mwauzimu. Mkulu wanga, amenenso anasiya kutumikira Yehova, anayambiranso kulambira koona ndipo anabatizidwa. Ndine wokondwa kuti bambo aona kubwerera kwathu m’choonadi. Bambo anatumikira mosangalala monga mtumiki wothandiza mu mpingo mpaka kumwalira kwawo mu 1993, ali ndi zaka 75. Amayi akutumikirabe Yehova mwachangu ku Ilesha.

Ndayenda m’mayiko okwana 16 a ku Ulaya, Asia, ndi Africa pofunafuna chuma. Zotsatira zake, ndinadzibweretsera zopweteka zambiri. (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndikayang’ana m’mbuyo, ndimamva chisoni kwambiri kuti ndinawononga nthawi yochuluka ya moyo wanga wachinyamata ndi mankhwala osokoneza bongo ndiponso khalidwe lachiwerewere. Ndimamva chisoni chifukwa cha ululu umene ndinaubweretsa kwa Yehova Mulungu ndiponso banja lathu. Komabe, ndikuthokoza kuti ndinapulumuka zonsezo ndipo ndabwereranso kwa Mulungu. Cholinga changa n’choti ndikhalebe wokhulupirika kwa Yehova ndi kum’tumikira kosatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 13]

Ndili mnyamata wopanduka

[Chithunzi patsamba 15]

Patsiku la ubatizo wanga

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi mkazi wanga Ruth