Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anakonda Zimene Anaphunzira

Anakonda Zimene Anaphunzira

Anakonda Zimene Anaphunzira

POSACHEDWAPA, anthu anapeza kalata imene mayi wina analemba atatsala pang’ono kufa ndi nthenda ya khansa m’mwezi wa May 2004. Zikuoneka kuti sanamalize kulemba kalatayi chifukwa anadwala kwambiri mwadzidzidzi. Kalatayi sinatumizidwe n’komwe, koma onse amene anadzaiwerenga anagwetsa misozi ndipo inalimbitsa chikhulupiriro chawo mwa Mulungu.

Kalatayi inalembedwa ndi Susan, ndipo anafotokoza yekha m’kalata yake kuti ali mtsikana, anaimbira foni mkulu wina wa Mboni za Yehova wa ku Connecticut, ku United States of America. Ndipo anam’fotokozera zinthu zimene anakumana nazo pa zaka zake za unamwali. Koma kumapeto kwa chaka chatha chomwechi, m’pamene mayi ake a Susan anapeza kalata yochititsa chidwi imeneyi n’kuitumiza ku likulu la Mboni za Yehova ku New York.

M’kalata yake, Susan analemba kuti anapeza nambala ya foni ya mkulu wa ku Connecticut ameneyu m’buku la manambala a foni m’chaka cha 1973. “Chaka chimenecho, ndili ndi zaka 14,” anafotokoza choncho Susan, “nditawerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndinazindikira kuti chinali choonadi. Popeza ndinali ndisanakumanepo ndi wa Mboni za Yehova aliyense, ndinawafufuza m’buku la manambala a mafoni n’kusankha nambala imene inali ndi manambala oyambirira ofanana ndi nambala yanga. M’bale Genrich atayankha foniyo, anadabwa kwambiri kuti ndinali ndisanakumanepo ndi munthu aliyense wa Mboni.” *

Vuto Lalikulu

Susan anafotokoza m’kalata yake kuti ali ndi zaka 10, anatumizidwa ku Connecticut kumakakhala ndi mayi ake aang’ono. Cholinga chinali choti akakhale kumeneko nthawi yochepa chabe, koma n’kupita kwanthawi Susan analembera kalata mayi ake, amene ankakhala okha ku Florida, kuwauza kuti akufuna kumakhalabe ndi mayi ake aang’ono. M’kalata yakeyo, Susan anafotokoza kuti zimene zinachitikazo zinali zofanana ndi “khalidwe linalake limene anthu amasonyeza nthawi zina, loyamba kukondana ndi anthu amene akuwazunza.” * Ndipo Susan ankazunzidwadi kwambiri.

Susan analembanso kuti: “Mayi anga aang’ono ndi mwamuna amene anali kukhala naye ankandizunza kwambiri. Komanso, ndi alendo ochepa okha amene ankawalola kulowa m’nyumba. Akandilola kupita kusukulu, sankandipatsa chakudya chamasana kapena zovala zabwino ngakhale kuti mayi anga ankanditumizira ndalama. Ndinali ndi kabudula mmodzi yekha wam’kati, koma ana aakazi awiri a mayi anga aang’onowo, amene anali aang’onopo kuyerekeza ndi ine, anali ndi chilichonse.” Susan analemba zimenezi pofuna kusonyeza chifukwa chake anadziwa kuti adzakhala m’vuto lalikulu ngati mayi ake aang’ono atatulukira kuti iye ali ndi chidwi chophunzira Baibulo.

Mmene Susan Anadziwira Zambiri za M’Baibulo

“M’bale Genrich anandidziwikitsa kwa Laura, mlongo wachikhristu wokhwima mwauzimu,” analemba motero Susan, “ndipo nthawi zambiri ndinkakumana naye kumalo ochapitsirako zovala kumene iye ankatha nthawi yambiri kuyankha mafunso anga a m’Baibulo.” Susan anafotokoza kuti anali asanapangepo chosankha chilichonse payekha koma pambuyo pa makambirano amenewa ndi kuwerenga buku lofotokoza Baibulo la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, anasankha yekha zochita.

Susan anapitiriza kufotokoza kuti: “Lachisanu lina usiku, nditauza mayi anga aang’ono kuti ndakhala ndikukambirana ndi Mboni za Yehova, sanandilole kugona, ndipo anandiumiriza kuima chilili usiku wonse pakatikati pa khitchini. Pambuyo pake, ndinatsimikiza mtima kuposa kale lonse kukhala wa Mboni.”

Kuyambira nthawi imeneyo, m’bale Genrich ankam’bweretsera Susan mabuku ophunzirira Baibulo. “Ndikukumbukira kwambiri Yearbook ya Mboni za Yehova ya chaka cha 1974,” analemba choncho Susan, “chifukwa inafotokoza mmene Mboni za Yehova zinapiririra chizunzo cha Anazi, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanachitike komanso ili m’kati . . . Ndi panthawi imeneyi pamene ndinapempha m’bale uja kundiikira nyimbo za Ufumu pa tepi kuti ndiziziphunzira. Patatha chaka, ndinkatha kuimba mwatsatanetsatane nyimbo zonse 119 za m’buku la nyimbo la chaka cha 1966, lotchedwa ‘Kuyimba ndi Kutsagana ndi Nyimbo za Malimba M’mitima Mwanu.’”

“Panthawi imeneyi, m’bale Genrich ankandibweretseranso matepi a nkhani za m’Baibulo, masewero, ndi nkhani za pamisonkhano. Akabwera nazo zinthu zimenezi ankazisiya pamalo enaake pafupi ndi pholo la telefoni, pamsewu wotchedwa Route 10 ndipo ine ndinkakazitengera pamenepo. . . Tsopano ndinayamba kudandaula ndi mmene zinthu zinalili, chifukwa ngakhale kuti ndinapita patsogolo mwauzimu, ndinali ndisanapiteko n’komwe ku msonkhano ngakhale umodzi. Ndinkaona kuti ndilibenso mphamvu zopitirizira.”

Susan ananena kuti zaka zingapo zotsatira zinali zovuta kwambiri. Anali atasiya kukumana ndi Mboni ziwiri zimene ankazidziwa zija. Koma kenako ananena kuti “kudziwa nyimbo zonse za m’buku la nyimbo kunali ‘temberero’ kwa ine.” Chifukwa chiyani anatero? “Chifukwa mawu ena ndi ena a m’nyimbozo ankandibwerera m’mutu, monga akuti, ‘As’kali a Ya safuna zofewa.’ Ndinkadziwa kuti mawu amenewa analembedwa ndi Mboni ina ili mumsasa wozunzirako anthu ku Germany panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, ndipo kukumbukira zimenezi kunkangowonjezera mavuto anga. Ndinkamva ngati ndine munthu wamantha, ndipo ndinkaganizanso kuti Yehova wanditaya.” *

Anapeza Ufulu Pomalizira Pake

“Zinthu zinasintha tsiku limene ndinakwanitsa zaka 18. Palibe wa Mboni amene anafikapo kunyumba kwathu kwa zaka zambiri chifukwa chakuti nyumba yathu inali m’gulu la nyumba zimene a Mboni samayenera kufikapo. Koma tsiku limeneli, munthu wina wochokera ku mpingo wina wa Mboni za Yehova, anabwera kunyumba kwathu, ndipo ndinalankhula naye chifukwa chakuti kunyumbako kunalibe wina aliyense. Limeneli linali tsiku loyamba limene ndingakumbukire lomwe ndinakhalapo ndekha panyumba Loweruka. Ndinaona ngati umenewu ndi umboni wakuti Yehova sananditaye. Ndiyeno ndinaimbira foni m’bale Genrich, yemwe ndinamuimbira koyambirira uja, n’kumuuza kuti tsopano ndakonzeka kuchoka, ndipo ndinamupempha kuti andithandize maganizo ngati pangakhale malangizo ena alionse ofunikira. Kenako ndinathandizidwa kuchoka.”

Susan anasamukira kudera lina m’mwezi wa April, 1977. M’kalata yake analembanso kuti: “M’kati mwa chaka chotsatira, ndinkapita ku misonkhano yonse ya mpingo ndi ku misonkhano ikuluikulu, ndipo ndinkalalikira nawo mu utumiki. Kenako ndinadzapezananso ndi mayi anga. Iwo sanadziwe kuti pa zaka zonse zam’mbuyozi ndinakhala ndikuzunzidwa kwambiri, ndipo anamva chisoni kwambiri. Anachitapo kanthu mwamsanga n’kuonetsetsa kuti ndinali ndi chilichonse chimene ndimafuna. Mayi anali atasamukira ku Alaska zaka zingapo zapitazo. Ndipo anali ndi chidwi kwambiri ndi choonadi cha m’Baibulo. Ndiyeno m’chaka cha 1978, ndinasamukira ku Alaska komweko n’kumakakhala nawo limodzi. Kenaka, nawonso anakhala Mboni ya Yehova ndipo n’ngokhulupirikabe mpaka pano.

“Nditayamba kupita ku misonkhano, m’bale Genrich anakonza zoti gulu la anthu angapo likaone likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, ku New York, ndipo anandipempha kuti nanenso ndipite nawo. Imeneyo inali imodzi mwa mphatso yokhalitsa kwambiri imene ndinapatsidwapo, chifukwa chipitireni ku ulendo umenewu ndakhala ndikuyamikira kwambiri gulu la Yehova. Basi, nkhani yanga ndi imeneyi. Nkhaniyi ndailemba mwachidule chifukwa ndimafuna kuimaliza mwamsanga.”

Mawu a m’kalata ya Susan amene talembawa ndi mbali yochepa chabe ya kalata yake yonse, chifukwa nkhani yonse inali ndi masamba 6 ndi theka. Kumapeto kwa kalata yake, Susan analemba kuti: “Ndinadwala kwambiri ndipo anandigoneka ku chipatala mwezi watha, moti ndimangoona ngati ndifa . . . Ndinapemphera kwa Yehova kuti andilole ndikhale ndi thanzi labwinoko milungu iwiri yokha, kuti ndikonze kaye zinthu zina ndi zina . . . Ndikudziwa kuti sindikhala ndi moyo nthawi yaitali, komabe ndikufuna kunena kuti kukhala zaka zimenezi m’choonadi kunali chinthu chosangalatsa kwambiri, moyo wabwino kuposa wina uliwonse.”

Kalatayi inalibe mawu othera kapena siginecha kumapeto kwake, ndipo siinatumizidwe n’komwe. Amene anapeza kalatayi sanadziwe kuti n’njopita kwa ndani. Koma, monga mmene tafotokozera kale, potsirizira pake inaperekedwa kwa mayi ake a Susan.

Kudziwa Zambiri za Susan

Susan atabatizidwa pa April 14, 1979, mayi ake anabwerera ku Florida. Koma iye anatsala ku Alaska komweko, chifukwa chakuti anafuna kukhalabe ndi mabwenzi ake a pamtima mu mpingo wa North Pole. Pambuyo pake anayamba utumiki wa nthawi zonse monga mpainiya. M’chaka cha 1991, nayenso anasamukira ku Florida, komwe anakwatiwa ndi mkulu mu mpingo wachikhristu yemwe analinso mpainiya mnzake, ndipo mwamunayo anamwalira patapita nthawi yochepa chimwalirireni Susan.

Susan ndi mwamuna wake anali banja lokondedwa kwambiri lomwe linkachitira limodzi utumiki wa nthawi zonse mpaka pamene Susan anayamba kudwala, zimene zinachititsa kuti asapitirize upainiya wawo. Pofika nthawi imeneyo, Susan anali atachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 20. Mwambo wa maliro ake unalumikizidwa pafoni ndi mpingo wa Mboni za Yehova wa North Pole.

Kalata ya Susan ikutithandiza kuyamikira kwambiri madalitso auzimu amene timapeza chifukwa choti timatumikira Yehova ndipo tili ndi chiyembekezo chabwino kwambiri cha kuuka kwa akufa. (Machitidwe 24:15) Nkhani ya moyo wa Susan imeneyi ikutitsimikiziranso kuti Yehova ali pafupi ndi onse amene amayandikira kwa iye!—Yakobe 4:7, 8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 M’bale Genrich ndi mkazi wake anamwalira pa ngozi m’chaka cha 1993.

^ ndime 6 Onani Galamukani! yachingelezi ya December 22, 1999, tsamba 7.

^ ndime 13 Imbirani Yehova Zitamando, Nyimbo 29, “Tiyeni, Mboninu!”

[Mawu Otsindika patsamba 23]

“Kukhala zaka zimenezi m’choonadi kunali chinthu chosangalatsa kwambiri, moyo wabwino kuposa wina uliwonse”

[Chithunzi patsamba 21]

Susan ali ndi zaka 10

[Chithunzi patsamba 23]

Susan ali ndi mwamuna wake, James Seymour