Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Woposa Onse Amene Anakhalapo

Munthu Woposa Onse Amene Anakhalapo

Munthu Woposa Onse Amene Anakhalapo

KODI mungasankhe ndani kuti ndi munthu woposa onse amene anakhalapo? Kodi mungasankhe Nowa, amene anapulumuka Chigumula ndiyeno n’kukhala tate wa aliyense amene ali ndi moyo lerolino? (Genesis 7:1, 21, 22; 9:18, 19) Kapena Nebukadinezara, wolamulira wakale wa dziko lonse ndiponso amene anamanga mzinda wokongola umene anautcha dzina lakuti Babulo Wamkulu? (Danieli 4:28-30) Mwinamwake Alexander Wamkulu, amene anatchulidwa ngakhale m’maulosi a m’Baibulo chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo? (Danieli 8:5-8, 21, 22) Nanga bwanji Julius Caesar, mtsogoleri wotchuka wachiroma?

Pomatha zaka pafupifupi 45 chimwalilireni Julius Caesar, ku Betelehemu kunabadwa mwana wotchedwa Yesu. Kodi mwana ameneyu ndiye anadzakhala munthu woposa onse amene anakhalapo? Pafupifupi zaka 100 zapitazo, buku lotchedwa The Historians’ History of the World linati: “Mbiri imasonyeza kuti zochitika za [Yesu] zinakhudza kwambiri moyo wa anthu, ngakhale tikaziona m’njira yosagwirizana ndi zauzimu, kuposa zochitika za munthu wina aliyense m’mbiri. Nyengo yatsopano, imene imadziwika kwa anthu okhala ku madera akuluakulu kumene chitukukuko chinayambira padziko lapansi, inayambira pa kubadwa kwa Yesu.”

Mpaka lero, anthu amachita chidwi kwambiri ndi Yesu Khristu. Zaka zingapo zapitazo, magazini otchuka a ku United States a Time, Newsweek, ndi U.S.News and World Report analemba pa nthawi imodzimodzi nkhani zoyambira pa chikuto zokhudza Yesu. Ndipo zikuoneka kuti chidwi cha anthu ponena za Yesu chikuwonjezereka. “Moyo wa Yesu ukupitirizabe kuonekera m’mafilimu, m’nyimbo ndi pa zovala. Iye ali pakati pa anthu amene timawaona kuti ndi otchuka kwambiri,” inalemba choncho nyuzipepala ya Toronto Star mu 2004.

Komabe, n’zodabwitsa kuti osati kale kwambiri, anthu ena anaphunzitsa zoti Yesu sanakhalepo n’komwe. Bruno Bauer (amene anakhala ndi moyo kuyambira mu 1809 mpaka 1882) anali mphunzitsi wotchuka amene ananenapo zimenezi. Mmodzi mwa ophunzira ake anali Karl Marx. Posachedwapa, Robert E. Van Voorst, analemba m’buku lake lotchedwa Jesus Outside the New Testament kuti: “Marx anatengera maganizo a Bauer akuti Yesu sanali munthu weniweni, ndipo kenaka mabuku a boma la Soviet Union ndiponso nkhani zina zolimbikitsa chikomyunizimu zinafalitsa mabodzawa.”

Komabe, masiku ano ndi anthu ochepa kwambiri amene amatsutsa zoti Yesu anakhalapodi. Kwenikweni, anthu ambiri amavomereza kuti Yesu anali weniweni ndiponso wofunika kwambiri. Magazini ya Wall Street Journal ya mu December 2002 inali ndi nkhani ya mutu wakuti: “Sayansi Siingatsutse za Yesu.” Mlembi wa nkhani imeneyi anamaliza ndi mawu akuti: “Ambiri mwa akatswiri a maphunziro, kupatulapo anthu ochepa amene amati kulibe Mulungu, avomereza kale Yesu wa ku Nazarete kuti anali munthu wa m’mbiri.”

Koma sikuti Yesu anali munthu wa m’mbiri chabe ayi. Magazini ya Time inati: “Munthu angafunike kuganiza mopitirira muyezo kuti akane mfundo yoti munthu amene moyo wake wakhudza anthu kwambiri, osati m’zaka 2000 zokhazi ayi, koma m’mbiri yonse ya anthu, anali Yesu wa ku Nazarete.” Magaziniyo inapitiriza kuti: “Pali chifukwa chachikulu chonenera kuti palibe munthu winanso amene moyo wake wakhudza anthu kwambiri ndiponso kwa nthawi yaitali ngati wa Yesu.”

Komabe, mafunso alipo: Kodi iye anali ndani kwenikweni? Nanga anachokera kuti? Kodi cholinga chake padziko lapansi chinali chotani? Ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuti tidziwe chilichonse chimene tingathe chokhudza iyeyo?