Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kumwa Mowa N’kulakwa?

Kodi Kumwa Mowa N’kulakwa?

 Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kumwa Mowa N’kulakwa?

“VINYO achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.” Kodi mawu amenewa, opezeka m’Baibulo pa Miyambo 20:1, akusonyeza kuti kumwa mowa n’kulakwa? Ena amaganiza choncho. Monga umboni, iwo amatchula nkhani za m’Baibulo zimene anthu anachita zinthu zoipa chifukwa chomwetsa mowa.—Genesis 9:20-25.

Ndiyeno pali zinthu zoipa zambiri zimene zimakhalapo chifukwa chomwetsa mowa. Zina mwa zinthu zimenezi ndi matenda monga otupa chiwindi, kuchita ngozi zoopsa, kugwera m’mavuto a zachuma, kuwononga banja, ndiponso kuvulaza mwana wosabadwa. Mwina chifukwa cha zotsatirapo zoipazi, “zipembedzo zambiri zaphunzitsa kuti kumwa mowa n’kulakwa,” limatero buku la The World Book Encyclopedia. Koma kodi kumwa mowa n’kulakwa? Kodi Baibulo limaletsa kumwa mowa pa mlingo uliwonse?

Kodi Baibulo Limati Chiyani?

Baibulo limachenjeza za zotsatirapo zoipa za kumwetsa mowa. Lemba la Aefeso 5:18 limati, “Musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa.” Ndiponso, pa Miyambo 23:20, 21 pamati: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka.” Ndipo lemba la Yesaya 5:11 limati: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa!”

Baibulo limatchulanso za ubwino womwa mowa pang’ono. Mwachitsanzo, lemba la Salmo 104:15 limati imodzi mwa mphatso za Mulungu ndi “vinyo wokondweretsa mtima wa munthu.” Ndipo phindu la kugwira ntchito zabwino, monga mmene Mlaliki 9:7 amanenera, ndi “[kudya] zakudya zako mokondwa, ndi kumwa vinyo wako mosekera mtima.” Podziwa mmene vinyo amathandizira thanzi la munthu, Paulo anauza Timoteyo kuti, “Usamangomwa madzi okha, koma uzimwanso vinyo pang’ono, chifukwa cha m’mimba mwako ndi kudwaladwala kwako kuja.” (1 Timoteyo 5:23) Baibulo limanenanso za mmene mowa umathandizira munthu kupirira ndi kuiwalako mavuto.—Miyambo 31:6, 7.

 N’zoonekeratu kuti Baibulo sililetsa kumwa mowa. Koma limaletsa kumwetsa ndi kuledzera. Choncho, Paulo analembera Akhristu oyang’anira, atumiki othandiza, ndi akazi achikulire kuti asakhale “oledzera,” ndipo anam’langiza Timoteyo kuti azimwa “vinyo pang’ono.(1 Timoteyo 3:2, 3, 8; Tito 2:2, 3) Akhristu onse akukumbutsidwa kuti “zidakwa” sizidzalowa “mu Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.

Mfundo yochititsa chidwi ndi yoti Baibulo limagwirizanitsa uchidakwa ndi kususuka kapena kudya kwambiri, ndipo limatilangiza kuti tiyenera kupewa ziwiri zonsezi. (Deuteronomo 21:20) Ngati kumwa mowa ngakhale pang’ono chabe kukanakhala kulakwa, kodi kudya chakudya sikukanakhala kulakwanso? M’malo mwake, Baibulo limati kumwetsa mowa mpaka kuledzera ndiponso kususuka ndi kudya kwambiri n’kulakwa, osati kudya ndi kumwa pang’ono.

Kodi Yesu Anatani?

Khristu anatisiyira “chitsanzo kuti [titsatire] mapazi ake mosamalitsa,” anatero mtumwi Petulo. “[Yesu] sanachite tchimo.” (1 Petulo 2:21, 22) Ndiyeno kodi Yesu ankaziona bwanji zakumwa zoledzeretsa? Chozizwitsa chake choyamba chinali chosintha madzi n’kukhala vinyo. Kodi ndi vinyo wotani amene Yesu anasandutsa kuchokera ku madzi? “Woyang’anira phwando” anayamikira mkwati chifukwa cha vinyo wopangidwa mozizwitsayo. Woyang’anirayo anati: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba, ndipo anthu akaledzera, m’pamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.”—Yohane 2:9, 10.

Vinyo ankamwedwa pa phwando la Paskha, ndipo Yesu anagwiritsa ntchito vinyo pamene anayambitsa mwambo wa Mgonero wa Ambuye. Popereka chikho kwa ophunzira ake, iye anawauza kuti: “Imwani nonsenu.” Podziwa kuti imfa yake ili pafupi, iye anawonjezera kuti: “Sindidzamwanso chakumwa ichi chochokera ku mpesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano limodzi ndi inu mu ufumu wa Atate wanga.” (Mateyo 26:27, 29) N’zoona, anthu ankadziwa kuti Yesu ankamwa vinyo.—Luka 7:34.

Ifeyo Titani?

Ngakhale kuti Baibulo sililetsa kumwa mowa, chimenecho sichifukwa choti tiyambe kumwa. Pali zifukwa zambiri zopewera mowa. Mwachitsanzo, munthu yemwe anali chidakwa amadziwa bwino kuopsa komwa ngakhale botolo limodzi. Mzimayi wapakati angapewe kumwa mowa poopa kuvulaza mwana wake wosabadwa. Podziwa mmene mowa umasokonezera bongo, woyendetsa galimoto angapewe kumwa kapena kuchita chilichonse chimene chingaike moyo wake kapena wa anthu ena pangozi.

Ndipo Mkhristu sangafune kuchita chinthu chimene chingakhumudwitse munthu wina amene chikumbumtima chake sichimulola kumwa mowa. (Aroma 14:21) Mkhristu angachite mwanzeru popewa kumwa panthawi imene akupita mu utumiki wakumunda. N’zochititsa chidwi kuti m’Chilamulo cha Mulungu kwa Aisiraeli akale, ansembe ankaletsedwa kumwa “vinyo, kapena choledzeretsa” panthawi imene anali kuchita utumiki wawo. (Levitiko 10:9) Ndiponso, m’mayiko amene amaletsa mowa kapena anauikira malamulo enaake, Mkhristu ayenera kutsatira malamulowo.—Aroma 13:1.

Ngakhale kuti nkhani yokhudza kumwa kapena kusamwa ndiponso kuchuluka kwa mowa umene munthu wafuna kuti amwe ndi yaumwini, Baibulo limalimbikitsa kusapitirira muyezo. Ilo limati: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

Kodi ndi chenjezo lotani lonena za kumwa mowa limene latchulidwa m’Malemba?—1 Akorinto 6:9, 10.

▪ Kodi Yesu Khristu anamwapo mowa?—Luka 7:34.

▪ N’chiyani chimene chimatsogolera Akhristu oona pankhani yokhudza kudya ndi kumwa?—1 Akorinto 10:31.